Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Chipembedzo Chimene Mungachikhulupirire?

Kodi Pali Chipembedzo Chimene Mungachikhulupirire?

Ngati munakhumudwapo ndi zochita za chipembedzo chinachake mwina zingakuvuteni kukhulupirira chipembedzo china. Koma dziwani kuti pali chipembedzo chomwe mungachikhulupirire. Yesu atabwera padziko lapansi, anakhazikitsa chipembedzo ndipo anaphunzitsa anthu a m’chipembedzocho kutsatira zimene Mulungu amafuna. Mpaka pano chipembedzo chimenechi, chomwe Akhristu ake amayesetsa kutsatira malamulo a Mulungu pamoyo wawo, chidakalipo. Kodi chipembedzo chimenechi mungachipeze kuti?

Estelle, yemwe tamutchula m’nkhani yoyambirira uja, ananena kuti: “Ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Patangopita nthawi yochepa ndinamvetsa mawu omwe ali palemba la Yohane 8:32, omwe amati: ‘Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.’”

Ray, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Nditayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndinadziwa kuti Mulungu si amene amayambitsa mavuto amene anthu amakumana nawo. Ndinasangalalanso kudziwa kuti ngakhale kuti Mulungu amalola zinthu zoipa kuchitika, analonjeza kuti posachedwa adzathetsa zoipa zonse.”

N’zoona kuti n’zovuta kukhala ndi makhalidwe abwino m’dzikoli lomwe anthu ambiri ali ndi makhalidwe oipa, koma n’zotheka. Anthu ambiri amafuna munthu wina woti aziwathandiza kumvetsa komanso kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova akuphunzitsa Baibulo anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse. Mlungu uliwonse anthu ambiri akuphunzira Baibulo ndipo akuyesetsa kuyamba kukonda Mlengi wawo. Zimenezi zikuwathandiza kuti azikhala ndi moyo wosangalala. *

Funsani a Mboni za Yehova chimene chimawapangitsa kuti azikhulupirira chipembedzo chawo

Ulendo wina mukadzakumananso ndi a Mboni za Yehova, mudzawafunse chimene chimawapangitsa kuti azikhulupirira chipembedzo chawo. Fufuzani zimene amaphunzitsa komanso mbiri yawo. Kenako ganizirani ngati pali chipembedzo chimene mukuona kuti mungachikhulupirire.

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.