Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi n’zotheka kukhala ndi moyo wosatha?

Kodi Mulungu wapereka chiyani chomwe chingatithandize kuti tidzapeze moyo wosatha?

Munthu woyambirira Adamu anakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Koma kenako anakalamba n’kumwalira. Kungoyambira nthawi imeneyo anthu akhala akuyesa njira zosiyanasiyana kuti asamakalambe. Koma palibe amene wakwanitsa kuthawa imfa. Chifukwa chiyani? Adamu anakalamba n’kumwalira chifukwa chakuti sanamvere Mulungu. Anthufe timakalamba ndi kufa chifukwa tinatengera uchimo kwa Adamu. Ndipo Baibulo limati mphoto ya uchimo ndi imfa.—Werengani Genesis 5:5; Aroma 5:12.

Kuti anthufe tidzathe kupeza moyo wosatha, panafunika wina woti adzapereke moyo wake ngati dipo. (Yobu 33:24, 25) Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa pofuna kuwombola munthu wina ndipo anthufe tinafunika kuwomboledwa ku imfa. (Ekisodo 21:29, 30) Yesu anapereka malipiro amenewo pamene anatifera.—Werengani Yohane 3:16.

Kodi tingatani kuti tidzapeze moyo wosatha?

Koma si anthu onse amene adzawomboledwe ku matenda ndi ukalamba. Anthu amene samvera Mulungu, ngati mmene Adamu anachitira, sadzapeza moyo wosatha. Anthu amene adzasangalale ndi moyo wosatha ndi okhawo amene machimo awo adzakhululukidwe.—Werengani Yesaya 33:24; 35:3-6.

Kuti machimo athu akhululukidwe tiyenera kuphunzira Baibulo n’cholinga choti timudziwe bwino Mulungu. Baibulo limatiphunzitsa zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso kuti tizichita zinthu zokondweretsa Mulungu kuti tidzapeze moyo wosatha.—Werengani Yohane 17:3; Machitidwe 3:19.