NSANJA YA OLONDA July 2013 | Kodi Pali Chipembedzo Chomwe Tingachikhulupirire?

Anthu ambiri sakhulupirira chipembedzo chifukwa chinawakhumudwitsapo. Werengani kuti mudziwe chipembedzo chimene mungachikhulupirire ndi ntima wonse.

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kufufuza za Chipembedzo Chanu?

Mukakhala m’chipembedzo chinachake moyo wanu wauzimu umakhala m’manja mwa chipembedzocho.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Ndalama?

Kodi zipembedzo za m’dera lanu zimakakamiza anthu mochita kuonetsera kapena mwakabisira kuti azipereka ndalama? Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Nkhondo?

Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azikonda anthu anzawo. Kodi zipembedzo masiku ano zimatsatira lamulo limeneli?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Zipembedzo Mungazikhulupirire pa Nkhani ya Makhalidwe Abwino?

Atsogoleri ambiri achipembedzo satsatira mfundo za makhalidwe abwino. Kodi Mulungu zimamukhudza bwanji zimenezi?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Pali Chipembedzo Chimene Mungachikhulupirire?

Kodi nthawi ina chipembedzo chinakukhumudwitsanipo? Ngati zimenezi zinakuchitikirani, mwina zingakuvuteni kukhulupirira chipembedzo chilichonse. Kodi kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni bwanji pa nkhani imeneyi?

CHINSINSI CHA BANJA LOSANGALALA

Mmene Mungakhalire Osangalala Ngati Mwakwatira Kapena Kukwatiwanso

Munthu akakwatira kapena kukwatiwanso amakumana ndi mavuto omwe mwina sankakumana nawo m’banja lake loyamba. Kodi mwanuna ndi mkazi angatani kuti azikhalabe osangalala?

YANDIKIRANI MULUNGU

‘Amadzaza Mitima Yathu’

Tsiku lililonse amatichitira zinthu zabwino ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu osayamika.

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Panopa Ndilibenso Maganizo Ofuna Kusintha Zinthu M’dzikoli”

Kodi Baibulo linathandiza bwanji munthu wina womenyera ufulu wa anthu ndi zinyama kudziwa chimene chingathandizedi kusintha zinthu padzikoli?

KUCHEZA NDI MUNTHU WINA

Kodi Mulungu Amamva Chisoni Tikamavutika?

Anthu ena akaona mavuto omwe akuchitika padzikoli, amakayikira zoti Mulungu alipo. Werengani m’Mawu a Mulungu kuti mudziwe mmene Iye amamvera akaona anthu akuvutika.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Anthu ayesa njira zosiyanasiyana kuti mwina asamakalambe koma palibe amene wakhalapo ndi moyo wosatha. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amalalikira Anthu Amene Ali Kale ndi Chipembedzo Chawo?

N’chiyani chimatichititsa kulalikira anthu amene ali kale ndi chipembedzo chawo?