Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Anthu Amene Ali Kale ndi Chipembedzo Chawo?

N’chifukwa Chiyani Mumalalikira Anthu Amene Ali Kale ndi Chipembedzo Chawo?

Taona kuti anthu ambiri amene ali kale ndi chipembedzo chawo amasangalala kukambirana nkhani za m’Baibulo. Komabe, timalemekeza ufulu umene munthu wina aliyense ali nawo wokhala m’chipembedzo chosiyana ndi chathu ndipo sitikakamiza anthu kuti amvetsere uthenga wathu.

Tikamakambirana ndi anthu nkhani zokhudza chipembedzo, timayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizichita zinthu ndi “mtima wofatsa” ndiponso “mwaulemu kwambiri.” (1 Petulo 3:15) Timadziwa kuti anthu ena akhoza kukana uthenga wathu. (Mateyu 10:14) Komabe, tikalankhula ndi munthu m’pamene timadziwa ngati munthuyo akufuna kumvetsera uthenga wathu kapena ayi. Timadziwanso kuti zinthu zimasintha pa moyo wa munthu.

Mwachitsanzo, tsiku lina munthu angakhale wotanganidwa moti sitingathe kulankhula naye koma tsiku lina angakhale ndi nthawi yoti tingalankhule naye. Komanso anthu angakumane ndi mavuto kapena zinthu zina zomwe zingawachititse kuti ayambe kuchita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo. Choncho timayesetsa kulankhula ndi anthu mobwerezabwereza.