Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO: KODI PALI CHIPEMBEDZO CHOMWE TINGACHIKHULUPIRIRE?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kufufuza za Chipembedzo Chanu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kufufuza za Chipembedzo Chanu?

Tiyerekeze kuti mukudwala matenda oopsa kwambiri ndipo mukufunika opaleshoni. Pamenepa mungafunike dokotala yemwe mungamukhulupirire chifukwa pokupangani opaleshoni, moyo wanu umakhala m’manja mwake. Choncho mungayesetse kufufuza za dokotalayo kuti mudziwe mmene wakhala akuchitira maopaleshoni.

Mofanana ndi zimenezi, ndi nzeru kufufuza mosamala za chipembedzo chanu. Zili choncho chifukwa mukakhala m’chipembedzo chinachake moyo wanu wauzimu umakhala m’manja mwa chipembedzocho. Mwachitsanzo, kuti mudzapulumuke zidzadalira chipembedzo chimene muli.

Yesu anapereka mfundo zimene zingatithandize kudziwa ngati chipembedzo chathu chimachita zoyenera kapena ayi. Iye ananena kuti: “Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.” (Luka 6:44) Mwachitsanzo, mukaganiza za chipembedzo chinachake, kodi mumaona kuti chili ndi zipatso zotani? Kodi atsogoleri a chipembedzocho amakonda kwambiri ndalama? Kodi anthu a m’chipembedzocho amatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani zokhudza nkhondo komanso makhalidwe? Ndipo kodi pali chipembedzo chimene mungachikhulupirire? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa.

“Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.”—Luka 6:44