Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

“Ndinkaona, Koma Sindinkadziwa Tanthauzo Lake”

“Ndinkaona, Koma Sindinkadziwa Tanthauzo Lake”

Mu 1975, ndili ndi zaka ziwiri, mayi anga anayamba kukayikira kuti mwina ndili ndi vuto linalake. Tsiku lina amayi atandinyamula, munthu wina anagwetsa chinthu chinachake pansi ndipo chinachita phokoso kwambiri. Amayi anadabwa kuona kuti ine sindinadzidzimuke ngakhale pang’ono. Nditakwanitsa zaka zitatu, ndinali ndisanayambebe kulankhula. Kenako makolo anga anakhumudwa kwambiri madokotala atawauza kuti ndine wogontha.

Ndidakali mwana, banja la makolo anga linatha, ndipo mayi ndi amene anatenga anafe, ineyo, mchimwene wanga ndi mchemwali wanga, n’kumatisamalira. Pa nthawi imeneyo, ku France, njira zimene ankagwiritsa ntchito pophunzitsa ana osamva zinali zosiyana ndi za masiku ano ndipo njira zambiri zinkachititsa kuti anawo azivutika kwambiri. Komabe ineyo kuyambira ndili mwana ndinali ndi mwayi kusiyana ndi ana ena osamva. Ndiloleni ndikufotokozereni chifukwa chake ndikutero.

Ndili ndi zaka pafupifupi zisanu

Kwa zaka zambiri, aphunzitsi ambiri ankakhulupirira kuti ana osamva ayenera kuphunzitsidwa powakakamiza kuti azilankhula komanso azidziwa zimene aphunzitsi akunena poona milomo ya aphunzitsiwo. Komanso ku France komwe ndinakulira, kunali lamulo loletsa kugwiritsa ntchito chinenero chamanja m’masukulu. Ana ena ankawamangirira manja kumbuyo pa nthawi imene akuphunzira.

Ndili mwana, mlungu uliwonse ndinkatha maola angapo ndikuphunzitsidwa kulankhula. Ankandigwira nsagwada kapena mutu n’kumandiuza kuti ndilankhule ngakhale kuti sindikanamva zimene ndikulankhulazo. Komanso sankandilola kulankhula ndi ana anzanga pogwiritsa ntchito manja. Ndimaona kuti zaka zimenezi zinali zovuta kwambiri pa moyo wanga.

Nditakwanitsa zaka 6, anandipititsa kusukulu inayake ya ana osamva, yogonera komweko. Kumeneku n’kumene ndinakumana kwa nthawi yoyamba ndi ana anzanga osamva. Komabe kusukulu imeneyinso sankalola kuti tizilankhulana pogwiritsa ntchito chinenero chamanja. Tikapezeka tikulankhula chinenero chamanjachi m’kalasi, ankatithyola zala kapena kutikoka tsitsi. Komabe tinkalankhula mobisa pogwiritsa ntchito zizindikiro zomwe tinayambitsa. Zimenezi zinkathandiza kuti ndizilankhulana ndi anzanga. Kwa zaka zinayi, ndinakhalako wosangalala.

Koma nditakwanitsa zaka 10 anandipititsa kusukulu ya pulayimale ya ana akumva. Ndinakhumudwa kwambiri moti ndinkangoona ngati ana onse osamva anafa ndipo ndatsala ndekha. Chifukwa chotsatira malangizo a madokotala, anthu a m’banja lathu sanaphunzire chinenero chamanja komanso sankandilola kucheza ndi ana ena osamva. Iwo ankachita izi chifukwa madokotala anawauza kuti zimenezi zipangitsa kuti ndiiwale zimene ndinaphunzira zondithandiza kuti ndiyambe kulankhula. Ndimakumbukira zimene zinachitika tsiku lina titapita kwa dokotala wina. Iye anaika buku la chinenero  chamanja padesiki lake. Nditaona chithunzi pachikuto cha bukulo, ndinapempha kuti andipatse bukulo koma nthawi yomweyo dokotalayo analibisa. *

MMENE NDINAYAMBIRA KUKONDA MULUNGU

Mayi anga ankayesetsa kutiphunzitsa anafe mfundo za m’Baibulo. Iwo ankapita nafe kumisonkhano ya Mboni za Yehova yomwe inkachitikira m’dera lathu. Popeza ndinali mwana, sindinkamva zambiri pamisonkhanoyo. Komabe anthu osiyanasiyana ankasinthana n’kumakhala nane pafupi ndipo ankandilembera manotsi a zimene zikukambidwa. Ndinkakhudzidwa kwambiri ndi chikondi chawo komanso mmene ankandisamalirira. Kunyumba, mayi ankaphunzira nane Baibulo komabe sindinkamvetsa bwino zimene ndinkaphunzirazo. Nthawi zina ndinkamva ngati mneneri Danieli, yemwe atalandira mawu aulosi kuchokera kwa mngelo ananena kuti: “Ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.” (Danieli 12:8) Kwa ine, “Ndinkaona, koma sindinkadziwa tanthauzo lake.”

Komabe pang’onopang’ono, ndinayamba kuphunzira mfundo za m’Baibulo. Mfundo iliyonse imene ndaimvetsa ndinkaiona kuti ndi yamtengo wapatali, ndipo ndinkayesetsa kuitsatira pa moyo wanga. Komanso ndinaphunzira zambiri kuchokera ku khalidwe la anthu ena. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti tiyenera kukhala oleza mtima. (Yakobo 5:7, 8) Koma mfundo imeneyi sindinkaimvetsa bwino. Komabe nditaona mmene Akhristu anzanga ankasonyezera khalidweli, ndinamvetsa bwino tanthauzo la kuleza mtima. Kunena zoona anthu a mu mpingo wathu andithandiza kwambiri.

NDINAKHUMUDWA KWAMBIRI KOMA KENAKO NDINASANGALALA

Stéphane anandithandiza kumvetsa bwino Baibulo

Ndisanakwanitse zaka 20, tsiku lina ndinaona anyamata osamva akulankhulana m’chinenero chamanja. Ndinayamba kucheza nawo mobisa moti ndinayamba kuphunzira chinenero chamanja cha ku France. Komanso ndinapitiriza kusonkhana ndi Mboni za Yehova ndipo kumisonkhanoko ndinkacheza ndi mnyamata wina dzina lake Stéphane, yemwe ankandikonda kwambiri. Iye ankayesetsa kulankhula nane ndipo chifukwa cha zimenezi inenso ndinayamba kumukonda kwambiri. Koma pasanapite nthawi, panachitika zinthu zimene zinandikhumudwitsa kwambiri. Stéphane anamangidwa atakana kupita kunkhondo chifukwa cha zimene amakhulupirira. Kumangidwa kwake kunandikhumudwitsa kwambiri moti ndinasiya kupita kumisonkhano.

Patatha miyezi 11, Stéphane anatuluka kundende. Ndinadabwa kwambiri kuona akulankhula nane m’chinenero chamanja. Iye anaphunzira chinenerochi kundende. Ndikamaona Stéphane akugwiritsa ntchito manja komanso nkhope yake polankhula nane, mumtima mwanga ndinkasangalala kwambiri.

NDINAYAMBA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA

Stéphane anayamba kuphunzira nane Baibulo m’chinenero chamanja. Apa m’pamene ndinayamba kugwirizanitsa mfundo za m’Baibulo zosiyanasiyana zimene ndinali nditamva. Ndili mwana, ndinkakonda kuona zithunzi zokongola za m’mabuku athu n’kumasiyanitsa anthu otchulidwa m’Baibulo. Zithunzizo zinkandithandizanso kuganizira makhalidwe a anthuwo ndipo zimenezi zinkachititsa kuti ndidziwe bwino nkhani zokhudza anthuwo. Ndinkadziwa zokhudza Abulahamu, “mbewu” yake ndiponso “khamu lalikulu.” Koma pamene Stéphane anandifotokozera mfundozi m’chinenero chamanja, m’pamene ndinazimvetsa bwino. (Genesis 22:15-18; Chivumbulutso 7:9) Zinali zoonekeratu kuti chimenechi ndiye chinenero changa chenicheni.

Popeza tsopano ndinkamvetsa zimene zinkanenedwa pa misonkhano, ndinayamba kufuna kudziwa zambiri chifukwa zinkandikhudza mtima. Chifukwa chothandizidwa ndi Stéphane, ndinayamba kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo mu 1992 ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova Mulungu. Komabe popeza ndili mwana ndinalibe mwayi wolankhula komanso kucheza ndi anthu, ndinali wamanyazi komanso ndinkachita mantha kulankhula ndi anthu.

ANANDITHANDIZA KUTHETSA MANYAZI

Patapita nthawi, kagulu kathu ka anthu osamva kanaphatikizidwa ndi mpingo wina wa Mboni za Yehova  womwe unkasonkhana mumzinda wa Bordeaux. Izi zinathandiza kuti ndipite patsogolo mwauzimu. Ngakhale kuti ndinkavutikabe kumvana ndi anthu, anzanga akumva ankaonetsetsa kuti ndikumvetsa zimene zikunenedwa. Gilles ndi mkazi wake, Elodie, ankayesetsa kulankhula nane. Nthawi zambiri, misonkhano ikatha, ankandiitanira kunyumba kwawo kuti tikadye chakudya kapena kumwa limodzi khofi. Izi zinachititsa kuti tizigwirizana kwambiri. N’zosangalatsa kwambiri kukhala pakati pa anthu amene amasonyezana chikondi potsanzira Mulungu.

Mkazi wanga Vanessa amandithandiza kwambiri

Mu mpingo womwewu ndinakumana ndi mtsikana wina wokongola kwambiri, dzina lake Vanessa. Ndinakopeka naye chifukwa amayesetsa kupewa kukhumudwitsa ena komanso amachita zinthu mwachilungamo. Iye ankaona kuti vuto langa lakusalankhula silingamulepheretse kulankhula nane koma lingamuthandize kuphunzira kulankhula ndi anthu ogontha. Zimenezi zinachititsa kuti tiyambe chibwenzi ndipo tinakwatirana m’chaka cha 2005. Ngakhale kuti ndimavutikabe kucheza ndi anthu, Vanessa wandithandiza kuthetsa vuto langa la manyazi komanso kuti ndizitha kufotokoza maganizo anga momasuka. Iye amandithandiza kwambiri kukwaniritsa udindo wanga kumpingo ndipo ndimayamikira kwambiri thandizo lake.

MADALITSO ENA OCHOKERA KWA YEHOVA

Chaka chimene tinakwatirana, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku France inandiitana kuti ndikaphunzire ntchito yomasulira mabuku a Mboni za Yehova. Pa zaka zapitazi, ofesi ya Mboni za Yehova ku France yakhala ikuyesetsa kutulutsa ma DVD a m’chinenero chamanja. Koma chifukwa choti pali zinthu zambiri zofunika kumasuliridwa, iwo anaona kuti pakufunikanso omasulira ambiri.

Ndikukamba nkhani ya m’Baibulo m’chinenero chamanja cha ku France

Ine ndi Vanessa tinaona kuti kukatumikira kumaofesi a Mboni za Yehova ndi madalitso, komabe poyamba tinkada nkhawa kuti mwina kuchita zimenezi kusokoneza zinthu zina. Tinkaganiza kuti ndikachoka, ndani azisamalira kagulu kathu ka chinenero chamanja? Nanga ndani azikhala m’nyumba yathu? Kodi Vanessa apeza ntchito? Koma Yehova anathandiza pa mavuto onsewa. Tinaona kuti Yehova amatikonda kwambiri komanso amakonda anthu osamva.

AKHRISTU ANZANGA AMANDITHANDIZA KWAMBIRI

Nditayamba kugwira ntchito yomasulira, ndinaona kuti Mboni za Yehova zikuyesetsa kuthandiza anthu osamva kuphunzira za Yehova. Komanso ndimasangalala kwambiri kuona kuti anthu ambiri amene ndikugwira nawo ntchito yomasulira amayesetsa kulankhula nane. Ndimakhudzidwa mtima kuona anthu ambiri akuyesetsa kulankhula nane pogwiritsa ntchito zizindikiro zochepa zimene aphunzira. Ndimaona kuti samandisala ngakhale pang’ono. Zonsezi ndi umboni woti anthu a Yehova amakondana komanso amagwirizana.—Salimo 133:1.

Ndikumasulira mabuku kumaofesi a Mboni za Yehova

Ndimayamikira Yehova kuti kudzera mu mpingo wachikhristu, amaonetsetsa kuti nthawi zonse pakhale munthu wina woti azindithandiza. Ndimayamikiranso mwayi womwe ndili nawo wothandiza anthu osamva anzanga kudziwa Mlengi wathu wachikondi komanso kukhala naye pa ubwenzi. Ndidzasangalala kwambiri ikadzafika nthawi imene anthu sadzalepheranso kulankhulana chifukwa chosiyana zinenero. Tonse, monga banja limodzi, tizidzalankhula “chilankhulo choyera” chomwe ndi choonadi chonena za Yehova Mulungu ndi zolinga zake.—Zefaniya 3:9.

^ ndime 9 M’chaka cha 1991 m’pamene boma la France linalola kuti ana azigwiritsa ntchito chinenero chamanja pophunzira.