Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa Mwana wa Mulungu?

Mulungu alibe mkazi weniweni amene anabereka naye ana. Iye ndi Mlengi wa zamoyo zonse. Anthu analengedwa mwanjira yakuti azitha kutengera makhalidwe a Mulungu. N’chifukwa chake Adamu, munthu woyamba kulengedwa, amatchedwa “mwana wa Mulungu.” Yesu amatchedwanso “Mwana wa Mulungu,” chifukwa analengedwa ndi makhalidwe ofanana ndi a Atate wake.—Werengani Luka 3:38; Yohane 1:14, 49.

Kodi Yesu analengedwa liti?

Mulungu analenga Yesu asanalenge Adamu. Ndipo Mulungu atalenga Yesu anamugwiritsira ntchito kulenga zinthu zina zonse kuphatikizapo angelo. N’chifukwa chake Baibulo limati Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Werengani Akolose 1:15, 16.

Asanabadwe ku Betelehemu, Yesu anali kumwamba monga cholengedwa chauzimu. Nthawi itakwana, Mulungu anasamutsira moyo wa Yesu m’mimba mwa Mariya n’cholinga choti Yesuyo abadwe monga munthu.—Werengani Luka 1:30-32; Yohane 6:38; 8:23.

N’chifukwa chiyani Mulungu anakonza zoti Yesu abadwe padziko lapansi? Nanga Yesu anakwaniritsa udindo wotani? Mayankho a mafunso amenewa mungawapeze m’Baibulo. Mayankhowo adzakuthandizani kumvetsa bwino komanso kuyamikira zimene Mulungu ndi Yesu anakuchitirani.