Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Kodi Lamulo Loyamba Ndi Liti pa Malamulo Onse?”

“Kodi Lamulo Loyamba Ndi Liti pa Malamulo Onse?”

Kodi Mulungu amafuna kuti tizichita chiyani kuti tizimusangalatsa? Kodi pali mndandanda wa malamulo amene tiyenera kuwatsatira? N’zosangalatsa kuti yankho lake ndi lakuti, ayi. Mogwirizana ndi zimene Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu ananena, zimene Mulungu amafuna kuti tizichita tingazinene m’mawu amodzi okha basi.—Werengani Maliko 12:28-31.

Choyamba, taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawi imene Yesu ananena mawu amenewa. Panali pa Nisani 11, kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe, ndipo ankaphunzitsa m’kachisi. Adani ake ankamufunsa mafunso n’cholinga choti amutole pakamwa. Koma nthawi zonse ankawasowetsa chonena ndi mayankho ake. Kenako Yesu anafunsidwa funso lakuti: “Kodi lamulo loyamba ndi liti pa malamulo onse?”—Vesi 28.

Funso limeneli linali lovuta kwambiri. Ayuda ankasiyana maganizo pa nkhani yoti pa malamulo 600 a m’Chilamulo cha Mose lofunika kwambiri ndi liti. Ena ankaona kuti malamulo onsewa ndi ofunika ndipo n’kulakwa kuona lamulo lina kukhala lofunika kuposa ena. Ndiye kodi Yesu akanayankha bwanji funso limeneli?

Poyankha iye ananena kuti lamulo lofunika si limodzi lokha koma awiri. Loyamba, Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Vesi 30; Deuteronomo 6:5) Mawu akuti “mtima,” “maganizo,” “moyo” ndiponso “mphamvu” ali ndi matanthauzo ofananafanana. * Choncho mfundo yaikulu ndi yoti, kukonda Yehova kuyenera kukhudza mbali zonse za moyo wathu komanso zonse zimene tili nazo. Buku lina lotanthauzira Baibulo linati: “Tiyenera kukonda Mulungu kwathunthu.” Choncho ngati mumakondadi Mulungu, muyenera tsiku lililonse kuchita zinthu zimene zingachititse kuti iye azisangalala nanu.—1 Yohane 5:3.

Lachiwiri, Yesu anati: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.” (Vesi 31; Levitiko 19:18) Kukonda Mulungu n’kogwirizana kwambiri ndi kukonda anthu anzathu. Kukonda Mulungu kumachititsa kuti munthu azikonda anthu anzake. (1 Yohane 4:20, 21) Ngati timakonda ena mmene timadzikondera, tidzawachitira zinthu zimene tingafune kuti ena atichitire ifeyo. (Mateyu 7:12) Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timakonda Mulungu yemwe anatilenga, ifeyo komanso anzathuwo, m’chifanizo chake.—Genesis 1:26.

Zimene Yehova amafuna kuti atumiki ake azichita tingazinene m’mawu amodzi. Mawu ake ndi akuti, chikondi

Kodi malamulo oti tizikonda Mulungu komanso anzathu ndi ofunika bwanji? Yesu anati: “Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” (Vesi 31) Mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, Yesu anati malamulo onse agona pa malamulo awiri amenewa.—Mateyu 22:40.

Kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu sikovuta kapena kosamvetsetseka. Zimene iye amafuna tingazinene m’mawu amodzi. Mawu ake ndi akuti, chikondi. Kuyambira kale, chikondi n’chofunika kwambiri pa nkhani ya kulambira Mulungu. Koma chikondi si nkhani yongonena pakamwa kapena kumangomva mumtima. Timafunika kuchita zinthu zosonyeza chikondicho. (1 Yohane 3:18) Tikukulimbikitsani kuti muphunzire zimene zingakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri Yehova, Mulungu yemwe “ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.

Mavesi amene mungawerenge mu March

Maliko chaputala 9-16 mpaka Luka chaputala 1-6

^ ndime 6 M’Baibulo mawu akuti “moyo” amatanthauza munthu yense. Choncho “moyo” ungaphatikizeponso “mtima,” “maganizo” komanso “mphamvu.”