Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NHANI YA PACHIKUTO: KODI KUUKITSIDWA KWA YESU N’KOFUNIKA BWANJI KWA INU?

Kodi Yesu Anaukitsidwadi?

Kodi Yesu Anaukitsidwadi?

WOLEMBA mbiri wina wachigiriki, dzina lake Herodotus, amene anakhalako zaka 2,500 zapitazo, analemba nkhani yonena za anthu a ku Iguputo a m’nthawi yake. Iye analemba kuti: “Pa maphwando a anthu olemera, akamaliza kudya wina ankatenga chifanizo cha munthu wakufa ali m’bokosi chomwe ankachigoba mofanana ndi mmene munthuyo ankaonekera. Ndiyeno ankaonetsa chifanizocho kwa munthu aliyense amene ali paphwandopo n’kunena kuti: ‘Idyani ndi kusangalala ndi moyo chifukwa mukadzafa, simudzatha kuchita chilichonse ndipo mudzakhala ngati chifanizochi.’”

Si anthu a ku Iguputo okha amene ankakhulupirira kuti munthu akafa, sadzaukitsidwanso. Masiku ano, mawu akuti “Tidye timwe, pakuti mawa tifa,” si achilendo. Anthu amene amaganiza kuti munthu akafa ndiye kuti kwake kwatha, amaona kuti ndi bwino kusangalala pamene uli ndi moyo. Amaonanso kuti palibe chifukwa chochitira zinthu zabwino. Zikanakhaladi kuti imfa ndi mapeto a zonse, bwenzi izi zili zoona. Komanso mtumwi Paulo anafotokoza zambiri pa nkhaniyi. Iye anafotokoza maganizo amene anthu omwe sakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa amakhala nawo. Ndipo anati: “Ngati akufa sadzauka, ‘tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’”—1 Akorinto 15:32.

Sikuti Paulo ankakhulupirira kuti akufa sadzauka. Iye ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Paulo ankakhulupirira zimenezi chifukwa ankadziwa kuti ngati Yesu Khristu anaukitsidwa, * ndiye kuti anthu amene anamwalira nawonso adzaukitsidwa. Mfundo yoti Yesu anaukitsidwa inali yofunika kwambiri kwa Akhristu oyambirira ndipo inalimbikitsa chikhulupiriro chawo.

Koma kodi nkhani ya kuuka kwa Yesu ndi yofunika motani kwa ife? Nanga tikudziwa bwanji kuti Yesu  anaukitsidwadi? Tiyeni tione zimene Paulo analemba pa nkhaniyi pamene ankalembera Akhristu a ku Korinto.

KODI CHIKANACHITIKA N’CHIYANI KHRISTU AKANAPANDA KUUKITSIDWA?

Akhristu ena a ku Korinto ankakayikira ngati Yesu anaukitsidwadi ndipo ena sankakhulupirira n’komwe zoti munthu wakufa angaukitsidwe. M’kalata yoyamba imene analembera Akhristuwo, mtumwi Paulo ananena zimene zikanachitika zikanakhala kuti akufa sangaukitsidwe. Iye analemba kuti: “Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke. Koma ngati Khristu sanauke, kulalikira kwathu n’kopanda pake, ndipo chikhulupiriro chathu n’chopanda pake. Ndiponso, ndiye kuti ifenso takhala mboni zonama za Mulungu, . . . chikhulupiriro chanu chilibe ntchito ndipo mukadali m’machimo anu. Ndiye kutinso anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu, kutha kwawo kunali komweko.”—1 Akorinto 15:13-18.

“Anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi . . . Kenako anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine.”—1 Akorinto 15:6-8.

Onani kuti Paulo anayamba ndi mfundo yosatsutsika yakuti: Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sanauke. Kodi chikanachitika n’chiyani zikanakhala kuti Khristu sanaukitsidwe? Ndiye kuti kulalikira uthenga wabwino kukanakhala kopanda phindu komanso uthengawo ukanakhala wabodza. Komanso kuukitsidwa kwa Yesu inali nkhani yaikulu pa chikhulupiriro cha Akhristu. N’kogwirizananso kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani yokhudza dzina la Mulungu, Ufumu wake, mmene tingapezere chipulumutso komanso mfundo yoti Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Zikanakhala kuti Yesu sanaukitsidwe, uthenga umene Paulo ndi atumwi ena ankalalikira ukanakhala wosamveka komanso wopanda ntchito.

Komanso zikanakhala kuti Khristu sanaukitsidwe, bwenzi chikhulupiriro cha Akhristu chili chopanda ntchito komanso chabodza. Ndiponso Paulo ndi Akhristu ena akanakhala akunena zabodza, osati zokhudza Yesu yekha, koma zokhudzanso Yehova Mulungu amene ankati anaukitsa Yesuyo. Kuwonjezera pamenepa, mfundo yoti Khristu “anafera machimo athu,” ikanakhala yabodza chifukwa ngati munthu sanapulumutsidwe ku imfa angakhale bwanji Mpulumutsi wa anthu ena? (1 Akorinto 15:3) Zimenezi zikanatanthauzanso kuti Akhristu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, anafa ndi chikhulupiriro chabodza choti adzaukitsidwa.

Paulo anamaliza ndi kunena kuti: “Ngati tayembekezera Khristu m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.” (1 Akorinto 15:19) Mofanana ndi Akhristu ena, Paulo analolera kudzimana zinthu zina, kuzunzidwa, kukumana ndi mavuto komanso kuphedwa kumene chifukwa ankakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa. Zikanakhala kuti mfundo yoti akufa adzaukitsidwa ndi yabodza, bwenzi zonsezi zilibe phindu.

N’CHIFUKWA CHIYANI MUYENERA KUKHULUPIRIRA KUTI YESU ANAUKITSIDWA?

Paulo sankakhulupirira kuti zimene Akhristu amakhulupirira ndi zabodza ndipo ankadziwa kuti Yesu anaukitsidwadi. Iye analembera Akhristu a ku Korinto umboni wa zimenezi kuti: “Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba. Ndiponso kuti anaikidwa m’manda, kenako anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba. Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja.” * Paulo anawonjezeranso kuti: “Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero, koma ena anagona mu imfa. Kenako anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine.”—1 Akorinto 15:3-8.

Paulo anafotokoza motsimikiza kuti Khristu anafera machimo athu, anaikidwa m’manda ndipo anaukitsidwa. Kodi n’chifukwa chiyani Paulo ankakhulupirira  ndi mtima wonse kuti zimenezi zinachitikadi? Chifukwa choyamba n’chakuti panali anthu ambiri omwe anaona zimenezi. Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa anthu payekhapayekha (kuphatikizapo Paulo), anaonekeranso kwa anthu angapo nthawi imodzi, ndipo kenako anaonekera kwa gulu la anthu 500. Ambiri mwa anthu amenewa ayenera kuti ankakayikira atamva zoti Yesu waukitsidwa. (Luka 24:1-11) Komanso ambiri mwa anthuwa anali adakali moyo pa nthawi imene Paulo ankalemba zimenezi ndipo anthu akanatha kuwafunsa za nkhaniyi. (1 Akorinto 15:6) Umboni wa munthu mmodzi kapena awiri ukhoza kutsutsidwa, koma ndani angatsutse umboni wa anthu oposa 500?

Komanso onani kuti kawiri konse, Paulo anasonyeza kuti imfa, kuikidwa m’manda komanso kuuka kwa Yesu, zinali ‘zogwirizana ndi Malemba.’ Zimene zinachitikira Yesuzi, zinasonyeza kuti maulosi onena za Mesiya opezeka m’Malemba Achiheberi anali oona. Zinasonyezanso kuti iye analidi Mesiya wolonjezedwa.

Ngakhale kuti pali umboni wa anthu amene anaona ndi maso komanso umboni wa m’Malemba, panali anthu ena amene ankakayikirabe zoti Yesu anaukitsidwa. Masiku anonso pali anthu ena amene amakayikira za nkhaniyi. Ena amanena kuti ophunzira ake anaba thupi la Yesuyo n’kumanama kuti waukitsidwa. Koma zimenezi zi zoona chifukwa ophunzirawo sakanatha kuchita zimenezi popeza panali alonda achiroma amene ankalondera manda a Yesu. Anthu ena amanena kuti anthu omwe ankati anaona Yesu ataukitsidwawo ankangoona zilubwelubwe. Koma mfundo imeneyi si yoona chifukwa Yesu anaonekera kwa anthu ambiri komanso pa nthawi zosiyanasiyana. Komanso kodi n’zoona kuti chilubwelubwe chingaotche nsomba n’kupatsa anthu kuti adye, ngati mmene Yesu anachitira ku Galileya ataukitsidwa? (Yohane 21:9-14) Ndiponso kodi zingatheke kuti chilubwelubwe chikhale munthu n’kuuza anthu kuti achikhudze?—Luka 24:36-39.

Komabe anthu ena amati, zoti Yesu anauka ndi bodza limene ophunzira anangopeka. Koma kodi kuchita zimenezi kukanakhala ndi phindu lanji? Ophunzirawo  ankanyozedwa, kuzunzidwa ngakhale kuphedwa kumene chifukwa chochitira umboni za kuukitsidwa kwa Yesu. Kodi iwo akanalolera kukumana ndi mavuto onsewa chifukwa chochitira umboni nkhani yabodza? Ndiponso, ku Yerusalemu n’kumene ophunzirawo anapereka umboni woyamba woti Yesu anaukitsidwa ndipo pa nthawiyi panali anthu ambiri otsutsa amene ankafunafuna mpata woti agwire ophunzirawo.

Nkhani ya kuukitsidwa kwa Yesu ndi imene inalimbikitsa ophunzira kuchitira umboni za Ambuye wawo ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri. Ndipo nkhaniyi inali yofunika kwambiri pa chikhulupiriro cha Akhristu. Akhristu oyambirira sakanalola kuika miyoyo yawo pa ngozi n’kumachitira umboni za Yesu, zikanakhala kuti Yesuyo anali mphunzitsi wanzeru basi amene anaphedwa. Iwo analolera kuika miyoyo yawo pa ngozi n’kumalalikira za kuukitsidwa kwa Yesu chifukwa panali umboni woti Yesuyo anali Khristu, Mwana wa Mulungu. Anali wamphamvu komanso ankathandiza ndi kutsogolera ophunzira akewo. Ophunzirawo ankadziwa kuti, ngati Yesu anaukitsidwa nawonso adzaukitsidwa. Ndithudi Yesu akanakhala kuti sanaukitsidwe, bwenzi kulibe Chikhristu mwinanso sitikanamva n’komwe za iye.

Koma kodi nkhani ya kuuka kwa Khristu ndi yofunika motani kwa inu?

^ ndime 5 M’Baibulo, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “kuuka” amatanthauza “kuimiranso.” Amatanthauza kuti moyo wa munthu wabwezeretsedwa ndipo munthuyo ali mmene analili poyamba komanso akukumbukira zonse zimene ankadziwa.

^ ndime 13 Mawu akuti “atumwi 12 aja” akunena za “atumwi okhulupirika” ngakhale kuti pa nthawi ina Yudasi Isikariyoti atafa, atumwi analipo 11 okha. Pa nthawi inanso pamene Yesu ankaonekera kwa atumwi, panali atumwi 10 okha chifukwa Tomasi panalibe. Komabe atumwi 10 amenewa anaimira atumwi 12.—Yohane 20:24.