Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

Kodi Yesu Analonjeza Munthu Wochita Zoipa Kuti Akakhala Naye Kumwamba?

Kodi Yesu Analonjeza Munthu Wochita Zoipa Kuti Akakhala Naye Kumwamba?

Anthu amafunsa funso limeneli chifukwa Yesu anauza munthu wochita zoipa amene anapachikidwa naye limodzi, kuti adzakhala naye m’Paradaiso. Yesu anati: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Onani kuti apa Yesu sanatchule kuti Paradaisoyo adzakhala kuti. Kodi ndiye kuti Yesu ankatanthauza kuti munthu wochita zoipayo akakhala naye kumwamba?

Choyamba, tiyeni tione ngati munthuyu anali woyenerera kukakhala kumwamba. Anthu amene ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba, amakhala oti anabatizidwa m’madzi komanso anabatizidwa ndi mzimu woyera ndipo iwo ndi ophunzira a Yesu obadwa ndi mzimu. (Yohane 3:3, 5) Chinthu chinanso chimene anthuwa amafunika kuchita ndi kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino monga kukhala oona mtima, okhulupirika ndi achifundo. (1 Akorinto 6:9-11) Ayeneranso kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu ndi Khristu mpaka pamapeto a moyo wawo. (Luka 22:28-30; 2 Timoteyo 2:12) Akakwaniritsa zimenezi, m’pamene amasonyeza kuti ndi oyenerera kuukitsidwira kumwamba n’kupatsidwa udindo wotumikira monga ansembe ndi mafumu. Iwo limodzi ndi Khristu adzalamulira anthu kwa zaka 1,000.—Chivumbulutso 20:6.

Koma munthu amene anapachikidwa ndi Yesuyu, anali wachifwamba ndipo anafa ali wotero. (Luka 23:32, 39-41) N’zoona kuti pamene anauza Yesu kuti, “mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu,” anasonyeza kuti ankalemekeza Yesu. (Luka 23:42) Komabe iye anali asanabatizidwe n’kukhala wophunzira wa Yesu wobadwa ndi mzimu. Analinso asanasonyeze kuti ndi munthu wokhulupirika komanso wambiri yabwino. Ndiye kodi zikanakhala zomveka kuti Yesu alonjeze munthu wotereyu kuti akalamulira naye kumwamba limodzi ndi otsatira ake omwe anasonyeza kukhulupirika pa moyo wawo?—Aroma 2:6, 7.

Kuti timvetse mfundoyi, taganizirani chitsanzo ichi: Munthu amene anakuberani ndalama atakupemphani kuti mum’khululukire, mungamukhululukire ndipo simungamuimbenso mlandu. Koma kodi mungauze munthu wotereyu kuti aziyendetsa bizinesi yanu kapena kuti aziyang’anira banja lanu? N’zoonekeratu kuti udindo umenewu mungapereke kwa munthu wodalirika amene mumamukhulupirira. N’chimodzimodzinso ndi anthu amene apatsidwa chiyembekezo chopita kumwamba. Iwo ayenera kusonyeza kuti ndi okhulupirika moti adzatha kutsatira mfundo za Mulungu polamulira anthu. (Chivumbulutso 2:10) Ngakhale kuti munthu wochita zoipayu, atatsala pang’ono kufa anapempha Yesu moona mtima kuti akufuna kudzakhala nawo mu Ufumu, iye analibe mbiri yoti anali munthu wokhulupirika.

Kodi Yesu anauza munthuyu kuti akakhala naye kumwamba tsiku lomwelo? Ayi, chifukwa Yesu sanapite kumwamba tsiku lomwelo. Iye anakhala “mumtima wa dziko lapansi,” kapena kuti m’manda kwa masiku atatu. (Mateyu 12:40; Maliko 10:34) Komanso ataukitsidwa, anakhalabe padziko lapansi kwa masiku 40 asanapite kumwamba. (Machitidwe 1:3, 9) Choncho, sizikanatheka kuti munthu wochita zoipayo akakhale ndi Yesu kumwamba tsiku lomwelo.

Nanga kodi Yesu ankanena za Paradaiso uti? Yesu ankatanthauza kuti munthuyu akadzaukitsidwa, adzakhala padziko lapansi laparadaiso limene Yesuyo azidzalamulira. (Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 21:3, 4) Kuti mudziwe zambiri za Paradaiso ameneyu komanso zimene Mulungu amafuna, funsani wa Mboni za Yehova aliyense.