Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI mukudziwa zimene zinachititsa mayi wina wa zaka zoposa 60 kusiya kulambira mafano? Nanga n’chiyani chinachititsa kuti wansembe wina wachishinto asiye ntchito yake ya pakachisi wolambira makolo n’kukhala Mkhristu? Komanso kodi n’chiyani chinachititsa kuti mayi wina amene analeredwa ndi anthu omwe si makolo ake, asiye kudera nkhawa kwambiri zoti makolo ake omubereka anamutaya? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mumve zimene anthu amenewa akunena.

“Ndinasiya kulambira mafano.”​—ABA DANSOU

CHAKA CHOBADWA: 1938

DZIKO: BENIN

POYAMBA: NDINKALAMBIRA MAFANO

KALE LANGA: Ndinakulira m’mudzi winawake wa m’mbali mwa nyanja wotchedwa So-Tchahoué. Anthu a m’mudzi umenewu ndi asodzi komanso amaweta ng’ombe, mbuzi, nkhosa, nkhumba, nkhuku ndi nkhunda. Kuderali kulibe misewu choncho anthu akafuna kuyenda amagwiritsa ntchito maboti ndi mabwato. Nyumba zambiri n’zomangidwa ndi matabwa komanso udzu ndipo ndi anthu ochepa okha amene amamanga nyumba zawo ndi njerwa. Anthu ambiri m’derali ndi osauka komabe sikuchitika zaumbava kapena chiwawa kawirikawiri ngati mmene zilili m’mizinda.

Ndili mwana, bambo anga ananditumiza ineyo ndi mkulu wanga kumalo olambirirako milungu ya makolo komwe tinaphunzirako kulambira milungu imeneyi. Nditakula ndinayamba kulambira mulungu wachiyoruba wotchedwa Dudua, kapena kuti Oduduwa. Ndinamangira nyumba mulungu ameneyu ndipo nthawi zambiri ndinkapereka kwa iye nsembe za zilazi, mafuta akanjedza, nkhono, nkhuku, nkhunda ndi nyama zosiyanasiyana. Ndinkawononga ndalama zambiri kuti ndipeze zinthu zimenezi, moti nthawi zambiri ndinkatsala opanda ndalama iliyonse.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti Yehova yekha ndiye Mulungu woona. Ndinaphunziranso kuti Yehova amadana ndi kulambira mafano. (Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14) Ndinazindikira kuti ndinafunika kusintha, choncho ndinataya mafano anga onse ndiponso ndinachotsa m’nyumba mwanga chilichonse chogwirizana ndi kupembedza mafano. Komanso ndinasiya kupita kwa owombeza, kuchita nawo miyambo yachipembedzo komanso miyambo yosiyanasiyana ya pa maliro .

Koma kuchita zimenezi sikunali kophweka kwa mayi wazaka zoposa 60 ngati ine. Anzanga, abale anga komanso anthu okhala nawo pafupi sanasangalale ndi zimenezi ndipo ankandinyoza. Koma ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize kuti ndipitirize kuchita zabwino. Komanso lemba la Miyambo 18:10 linandilimbikitsa chifukwa limanena kuti: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.”

Chinanso chomwe chinandithandiza ndi kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Kumeneko anandisonyeza chikondi chimene Akhristu oona amayenera kukhala nacho ndipo ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti anthu amenewa amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Zimene ndinaona kumeneko zinandipangitsa kukhulupirira kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova chimaphunzitsadi zoona.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwandithandiza kuti ndizigwirizana kwambiri ndi ana anga. Komanso ndikuona kuti chimtolo cholemetsa chimene ndinasenza ndachitula pansi. Poyamba ndinkawononga ndalama zanga kupereka nsembe ku mafano opanda moyo amene anali osathandiza ngakhale pang’ono. Koma panopa ndikulambira Yehova, Mulungu amene wakonza zodzathetsa mavuto athu onse. (Chivumbulutso 21:3, 4) Komanso ndine wosangalala kwambiri chifukwa panopa sindinenso kapolo wa mafano koma ndikutumikira Yehova. Kuchita zimenezi kwachititsa kuti ndikhale ndi tsogolo labwino.

“Kuyambira ndili mwana ndinkafunitsitsa kudziwa Mulungu.”​—SHINJI SATO

CHAKA CHOBADWA: 1951

DZIKO: JAPAN

POYAMBA: NDINALI WANSEMBE WA CHIPEMBEDZO CHACHISHINTO

KALE LANGA: Ndinakulira m’tawuni yaing’ono m’chigawo cha Fukuoka ndipo makolo anga ankakonda kwambiri kupemphera. Kuyambira ndili mwana, anandiphunzitsa kuti ndizilemekeza milungu yachipembedzo chachishinto. Ndili mnyamata, nthawi zambiri ndinkaganizira kwambiri zimene ndingachite kuti ndidzapulumuke komanso ndinkafunitsitsa kuthandiza anthu ovutika. Ndikukumbukira tili ku pulayimale, aphunzitsi athu anatifunsa zimene tikufuna kudzachita tikadzakula. Anzanga onse ananena kuti akufuna kuti adzagwire ntchito zapamwamba monga kukhala akatswiri asayansi. Koma ine ndinayankha kuti ndimafuna kudzatumikira Mulungu ndipo anzanga onse anandiseka.

Nditamaliza maphunziro a ku sekondale, ndinayamba kuphunzira ntchito yoti ndizidzaphunzitsa anthu kukhala atsogoleri achipembedzo. Pa nthawi imeneyi, ndinakumana ndi wansembe wina wachishinto amene amayesetsa kupeza nthawi n’kumawerenga buku linalake lachikuto chakuda. Tsiku lina wansembeyu anandifunsa kuti “Kodi Sato, buku ili ukulidziwa?” Nditaona chikuto cha bukulo, ndinayankha kuti: “Inde ndikulidziwa, ndi Baibulo.” Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Aliyense amene akufuna kudzakhala wansembe wachishinto ayenera kuwerenga buku limeneli.”

Nthawi yomweyo ndinapita kokagula Baibulo. Ndinkalisunga pamalo abwino ndipo ndinkayesetsa kulisamalira. Komabe sindinkapeza nthawi yoliwerenga chifukwa ndinkatanganidwa kwambiri ndi sukulu. Nditamaliza sukulu ndinayamba kugwira ntchito pakachisi ngati wansembe wachishinto ndipo ndinkaona kuti ndakwaniritsa maloto anga.

Koma pasanapite nthawi ndinadabwa kuona kuti zinthu zimene ansembe achishinto ankachita sizimene ndinkayembekezera. Ansembe ambiri analibe chikondi komanso sankakhudzidwa ndi mavuto a anthu. Komanso iwo sankakhulupirira kwambiri Baibulo. Wansembe wina amene ankatiyang’anira anafika pondiuza kuti: “Ngati ukufuna zinthu zikuyendere bwino, uzilankhula zimene akatswiri a nzeru za anthu amaphunzitsa basi. Pano sitifuna anthu olankhula zinthu zauzimu ayi.”

Mawu amenewa anandikhumudwitsa kwambiri ndipo anandipangitsa kuti ndiyambe kukayikira chipembedzo chachishinto. Ngakhale kuti ndinapitiriza kugwira ntchito pamalopa, ndinayamba kufufuza ziphunzitso za zipembedzo zina. Koma sindinapeze chipembedzo chimene chinkaphunzitsa zogwira mtima. Pa zipembedzo zonse zimene ndinafufuza, palibe chimene ndinakhutira nacho. Choncho ndinayamba kuganiza kuti palibe chipembedzo chimene chimaphunzitsa zoona.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: M’chaka cha 1988, ndinakumana ndi munthu wina wachipembedzo chachibuda, amene anandilimbikitsa kuti ndiziwerenga Baibulo. Ndinakumbukira kuti izi n’zimenenso wansembe wachishinto uja anandiuza zaka zingapo m’mbuyomo, choncho ndinaganiza zotsatiradi malangizo amenewa. Nditayamba kuwerenga Baibulo, sindinkafunanso kulisiya moti nthawi zina ndinkaliwerenga usiku wonse mpaka m’mawa.

Zimene ndinkawerenga zinandichititsa kuyamba kupemphera kwa Mulungu amene amatchulidwa m’Baibulo. Ndinayamba ndi pemphero la Ambuye lomwe limapezeka pa Mateyu 6:9-13 ndipo ndinkalibwereza pakadutsa maola awiri alionse. Ndinkachita zimenezi ngakhale pogwira ntchito yanga ya unsembe pakachisi wachishinto.

Ndinali ndi mafunso ambirimbiri okhudza zinthu zomwe ndinkawerenga m’Baibulo. Pa nthawi imeneyi n’kuti nditakwatira ndipo ndinkadziwa kuti a Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo chifukwa anali atabwerapo kunyumba kwathu kudzacheza ndi mkazi wanga. Choncho ndinayamba kufufuza a Mboni ndipo ndinapeza mayi wina yemwe ndinamufunsa mafunso ambirimbiri. Ndinagoma nditaona kuti anagwiritsa ntchito Baibulo kuyankha funso lililonse. Iye anakonza zoti a Mboni aziphunzira nane Baibulo.

Pasanapite nthawi ndinayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Poyamba sindinazindikire kuti a Mboni ena amene ndinakumana nawo kumeneku anali oti ndinawachitapo chipongwe m’mbuyomu. Koma iwo anandipatsa moni mwansangala ndipo ankasonyeza kuti andilandira ndi manja awiri.

Ku misonkhanoko ndinaphunzira kuti Mulungu amafuna kuti amuna azikonda akazi awo komanso azisamalira mabanja awo. Ndisanaphunzire zimenezi, ndinkatha nthawi yambiri ndikugwira ntchito yanga ya unsembe moti sindinkacheza kwenikweni ndi mkazi wanga komanso ana athu. Ndinazindikira kuti ndinkamvetsera mwachidwi anthu akabwera kukachisi kudzandiuza mavuto awo koma sindinkamvetsera mkazi wanga akamandilankhula.

Kuphunzira Baibulo kunandithandiza kudziwa zambiri za Yehova ndipo izi zinandithandiza kuti ndikhale naye pa ubwenzi. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi malemba ena ngati la Aroma 10:13 limene limati: “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Kuyambira ndili mwana, ndinkafunitsitsa nditadziwa Mulungu woona ndipo pa nthawiyi ndinaona kuti ndamupeza.

Ndinayamba kuona kuti siinenso woyenera kumagwira ntchito pakachisi wachishinto. Koma poyamba ndinkadera nkhawa kuti anthu ena aganiza chiyani ndikasiya chipembedzochi. Nthawi zonse ndinkadziuza kuti ndikadzangopeza Mulungu woona ndidzasiya chipembedzo chachishinto. Choncho mu 1989, ndinasiya chipembedzochi n’kuyamba kutumikira Yehova.

Komabe kusiya chipembedzo changa kunali kovuta kwambiri. Ansembe amene ankatiyang’anira anakwiya nane kwambiri ndipo ankandikakamiza kuti ndisachoke. Koma ndinkadanso nkhawa kwambiri kuti ndikawafotokozera bwanji makolo anga za nkhaniyi. Tsiku lomwe ndinkapita kunyumba kwa makolo anga kuti ndikawauze za nkhaniyi, ndinali ndi nkhawa kwambiri moti pamtima panga pankapweteka komanso miyendo yanga inkangonjenjemera. Ndili m’njira ndinaima kangapo konse kupemphera kwa Yehova kuti andipatse mphamvu.

Nditafika kunyumba kwa makolo anga, ndinali ndi mantha kwambiri kuti ndiyambitse nkhaniyi moti panadutsa nthawi ndisanainene. Kenako, nditapemphera kwambiri, ndinawafotokozera bambo zimene ndinabwerera. Ndinawauza kuti ndapeza Mulungu woona ndipo ndikufuna kusiya chipembedzo chachishinto kuti ndiyambe kumutumikira. Bambo anga sanakhulupirire zimenezi ndipo anakhumudwa kwambiri. Kunabweranso achibale ena ndipo anayesetsa kundikakamiza kuti ndisinthe maganizo. Sindinkafuna kukhumudwitsa abale anga komabe ndinkadziwanso kuti ndiyenera kutumikira Yehova basi. Koma patapita nthawi, iwo anayamba kundilemekeza chifukwa cha zimene ndinasankha.

Ngakhale kuti ndinali nditasiya chipembedzo chachishinto, ndinafunikanso kusintha maganizo anga komanso mmene ndinkaonera zinthu. Moyo waunsembe unali utandilowerera kwambiri. Ndinkayesetsa kuti ndiiwale, koma chilichonse chimene ndinkachita chinkangondikumbutsa zimene ndinkachita ndili wansembe.

Koma pali zinthu ziwiri zomwe zinandithandiza kuti ndiiwale moyo wanga wakale. Choyamba, ndinafufuza bwinobwino m’nyumba mwanga kuti ndipeze chilichonse chogwirizana ndi chipembedzo changa chakale. Ndinapeza mabuku, zithunzi komanso zinthu zina ndipo zonsezo ndinaziwotcha ngakhale kuti zina mwa zinthu zimenezi zinali zodula. Chachiwiri, ndinkayesetsa kupeza nthawi yocheza ndi a Mboni ndipo kucheza ndi anthu amenewa kunandithandiza kwambiri. Pang’onopang’ono ndinayamba kuiwala za chipembedzo changa chakale.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Poyamba sindinkapeza nthawi yocheza ndi mkazi wanga ndi ana ndipo izi zinkapangitsa kuti azikhala osasangalala. Koma nditayamba kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti amuna azipeza nthawi yocheza ndi akazi awo ndiponso ana awo, tinayamba kugwirizana kwambiri. Patapita nthawi mkazi wanga nayenso anayamba kutumikira Yehova. Panopa ineyo ndi mkazi wanga, mwana wathu wamwamuna komanso mwana wathu wamkazi ndi mwamuna wake, tonse tikutumikira Mulungu.

Ndili mwana, ndinkafunitsitsa kuti ndikadzakula ndizidzatumikira Mulungu ndiponso kuthandiza anthu. Panopa ndimaona kuti ndakwaniritsadi cholinga changachi komanso ndakwanitsa kuchita zinthu zina zimene ndinali ndisanaziganizepo. Ndikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha zimene wandichitira.

“Ndinkadziwa kuti chinachake chikusoweka pa moyo wanga.”​—LYNETTE HOUGHTING

CHAKA CHOBADWA: 1958

DZIKO: SOUTH AFRICA

POYAMBA: NDINKAONA KUTI MAKOLO ANGA ANANDITAYA

KALE LANGA: Ndinabadwira m’tawuni ya Germiston. Anthu ambiri m’tawuniyi si osauka kwenikweni ndipo amagwira ntchito m’migodi. Komanso m’tawuniyi simuchitika zaumbava kapena zachiwawa zambiri. Nditangobadwa, makolo anga anaona kuti sangakwanitse kundilera choncho anaganiza zondipereka kwa amene angafune kunditenga n’kumandilera ngati mwana wawo. Choncho ndili ndi milungu iwiri yokha, banja lina linanditenga. Anthu amenewa anali achikondi kwambiri moti ndinkawaona kuti ndi makolo anga enieni. Komabe, nditadziwa kuti anthuwa sanali makolo anga enieni, ndinayamba kumadzimvera chisoni poganiza kuti makolo anga ananditaya. Makolo ondilera aja ndinasiya kuwaona ngati makolo anga enieni komanso ndinkaona kuti sakundimvetsa.

Ndili ndi zaka 16 ndinayamba kupita kumabala ndi anzanga komwe tinkakavina komanso kuonerera anthu akuimba. Chaka chotsatira, ndinayamba kusuta fodya n’cholinga chakuti ndichepe thupi mpaka ndifanane ndi anthu otchuka amene amawaonetsa akamanenerera fodya. Kenako ndinayamba kugwira ntchito mumzinda wa Johannesburg ndipo ndinayamba kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa. Apa n’kuti ndili ndi zaka 19. Pasanapite nthawi ndinayamba kutukwana, kusuta kwambiri, komanso kumwa mowa mwauchidakwa.

Ngakhale zinali choncho, ndinkaona kuti ndinali munthu wathanzi. Ndinkakonda kuchita masewera olimbitsa thupi, mpira wamiyendo wa azimayi komanso masewera ena. Ndinkalimbikiranso kwambiri ntchito yanga ya zamakompyuta ndipo ndinatchuka kwambiri chifukwa cha ntchitoyi. Zimenezi zinachititsa kuti ndizipeza ndalama zambiri ndipo anthu ankaona kuti zinthu zikundiyendera. Koma zoona zinali zakuti ndinali munthu wosasangalala ndipo ndinkaona kuti chinachake chikusoweka pa moyo wanga.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Nditayamba kuphunzira Baibulo, ndinazindikira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi. Ndinaphunziranso kuti anasonyeza chikondi chimenechi potipatsa Mawu ake Baibulo. Baibulo lili ngati kalata ya malangizo imene iye watilembera n’cholinga choti azititsogolera pa moyo wathu. (Yesaya 48:17, 18) Choncho ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kuti Yehova azinditsogolera, ndinayenera kusiya makhalidwe onse oipa.

Chinthu china chomwe ndinafunikira kusintha, ndi anthu omwe ndinkacheza nawo. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri ndi mawu a pa Miyambo 13:20 amene amati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mfundo imeneyi inandichititsa kuti ndisiye kucheza ndi anthu omwe ndinkacheza nawo poyamba, n’kuyamba kucheza ndi anthu a Mboni za Yehova.

Koma vuto lalikulu linali kusiya kusuta, chifukwa khalidwe limeneli linali litandilowerera kwambiri. Koma ndinayesetsa mpaka ndinasiyadi komano ndinakumananso ndi vuto lina. Vuto lake linali lakuti nditasiya kusuta ndinanenepa kwambiri. Zimenezi zinkandichititsa manyazi kwambiri moti zinanditengera zaka 10 kuti ndichepe thupi kufika pamene ndinkafuna. Komabe ndinkaona kuti ndiyenera kusiya kusuta fodya basi. Ndinapemphera kwa Yehova kambirimbiri kuti andithandize.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa ndili ndi thanzi labwino kuposa kale. Komanso ndine wosangalala chifukwa sindikuvutikanso kuchita zinthu zambiri kuti ndipeze chimwemwe chimene anthu amaganiza kuti chimapezeka ukakhala pa ntchito yabwino, ukakhala ndi udindo kapenanso ukakhala ndi chuma. M’malomwake ndikusangalala chifukwa chouza ena choonadi chopezeka m’Baibulo. Zimenezi zachititsa kuti anthu atatu amene ndinkagwira nawo ntchito ndiponso mwamuna wanga ayambe kutumikira Yehova. Komanso makolo anga amene anandilera aja asanamwalire, ndinawauza lonjezo la m’Baibulo lonena kuti anthu akufa adzaukitsidwa n’kukhala m’paradaiso padziko lapansi.

Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova kwandithandiza kuti ndisiye kudera nkhawa kwambiri zoti makolo anga ondibereka ananditaya. Yehova wandithandiza kuona kuti ndili m’banja lalikulu la padziko lonse la anthu omwe amamulambira. M’gulu la anthu amenewa ndapezamo amayi, abambo, azichimwene komanso azichemwali.​—Maliko 10:29, 30.

[Chithunzi patsamba 12]

A Mboni za Yehova anzanga amandisonyeza chikondi chimene Akhristu oona amayenera kukhala nacho

[Chithunzi patsamba 13]

Kachisi wachishinto komwe ndinkapemphera