Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amaona Kuti Mtundu Wina Wa Anthu Ndi Wofunika Kuposa Mitundu Ina?

Kodi Mulungu Amaona Kuti Mtundu Wina Wa Anthu Ndi Wofunika Kuposa Mitundu Ina?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Amaona Kuti Mtundu Wina Wa Anthu Ndi Wofunika Kuposa Mitundu Ina?

▪ Ayi, iye samaona choncho. Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

Nkhani imeneyi Mulungu amaiona mosiyana kwambiri ndi mmene anthu opanda ungwirofe timaionera. Anthu ambiri amakhulupirira kuti mtundu wina (makamaka wawo) ndi wapamwamba kuposa mitundu ina. Maganizo atsankho amenewa ndi ofanana ndi zimene katswiri wina dzina lake Charles Darwin ananena. Iye analemba kuti: “M’tsogolomu, . .  mitundu yotukuka idzachotsa padzikoli mitundu yonse yosatukuka moti dziko lonse lidzakhala ndi mtundu umodzi wotukuka.” N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri achitiridwapo zinthu zoipa zosiyanasiyana ndi anthu amitundu imene imadziona kuti ndi yapamwamba kuposa mitundu ina.

Kodi pali chifukwa chomveka chimene chingapangitse munthu kuganiza kuti mtundu wawo ndi wofunika kuposa mitundu ina? Mwachitsanzo, kodi asayansi anapeza kuti pali anthu a mitundu ina omwe mwachibadwa amakhala apamwamba pomwe anthu amitundu ina amakhala otsika? Ayi. Mwachitsanzo, katswiri wina wa maphunziro a chibadwa cha anthu yemwenso ndi pulofesa wa pa yunivesite ya Oxford, dzina lake Bryan Sykes ananena kuti: “Palibe umboni uliwonse wokhudza chibadwa cha anthu umene ungatithandize kusiyanitsa pakati pa anthu a fuko kapena mtundu wina ndi anthu amitundu ina. . . . Nthawi zambiri anthu amandifunsa kuti, kodi pali DNA yosonyeza kuti munthu ndi Mgiriki kapena ndi Mtaliyana? Koma yankho la mafunso onsewa ndi lakuti ayi.  . . Anthu tonsefe ndife pachibale.”

Zomwe pulofesayu anapeza n’zogwirizana ndi zimene Malemba amanena. Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu analenga mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi ndipo anthu tonsefe ndife mbadwa za anthu awiri amenewo. (Genesis 3:20; Machitidwe 17:26) Choncho Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana ndiponso kuti anthu onse ndi mtundu umodzi.

Zoti munthu ali ndi khungu lotani kapena nkhope yotani, zilibe ntchito kwa Yehova. Kwa iye, chofunika kwambiri ndi mtima wathu wophiphiritsira kapena kuti mmene timaonera zinthu. Iye amatiuza kuti: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero?

Zilibe kanthu kuti kaya ndife ochokera mu mtundu uti, ambirife sitisangalala ndi mmene timaonekera ndipo mwina palibe chimene tingachite kuti tizioneka mmene timafunira. Komabe tingathe kusintha umunthu wathu n’kukhala munthu wabwino kuposa mmene tilili panopa ndipo zimenezi ndiye zofunika kwambiri kuposa maonekedwe athu. (Akolose 3:9-11) Titati tidzifufuze bwinobwino tingapeze kuti mwina timaona kuti mtundu wathu ndi wapamwamba kapena ndi wotsika kuposa mtundu wa anthu ena. Koma popeza kuti maganizo onsewa ndi osagwirizana ndi mmene Mulungu amaonera anthu, tiyenera kuyesetsa kuchotsa maganizo olakwikawa mumtima mwathu.​—Salimo 139:23, 24.

Tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova atithandiza kuyesetsa kuti tizidziona kapena kuona ena monga mmene iye amachitira. Mawu ake amatiuza kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Mawu amenewa akugwira ntchito kwa aliyense mosaganizira za mtundu wake.