Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Uli Ndi Phindu Lililonse?

Kodi Moyo Uli Ndi Phindu Lililonse?

 Kodi Moyo Uli Ndi Phindu Lililonse?

“KODI moyo uli ndi phindu lililonse?” Anthu ambirimbiri amafunsa funso limeneli. Koma n’zomvetsa chisoni kuti munthu aliyense, sangathe kupewa zimene dokotala wina woona za ubongo, wa ku Austria, dzina lake Viktor E. Frankl, ananena. Iye ananena kuti anthu ambiri amaona kuti moyo “ulibe phindu lililonse ndipo ndi wachabechabe.”

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amaona choncho? Chifukwa chimodzi n’choti anthu mamiliyoni ambiri akukhala moyo womvetsa chisoni ndipo athedwa nzeru chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo pa moyo wawo. Tsiku ndi tsiku amakumana ndi mavuto monga umphawi, matenda, chiwawa ndiponso kuponderezedwa. Malinga ndi zimene Yobu ananena zokhudza mavuto a anthu, moyo wa anthu ambiri ndi “wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Iwo amaona kuti chofunika kwambiri n’kungoyesetsa kuchita zinthu zowathandiza kuti akhalebe ndi moyo.

Komabe pali anthu ena mamiliyoni ambiri omwe ndi olemera ndipo amaoneka kuti akusangalala ndi moyo. Koma ambiri mwa anthu oterewa sakhala osangalala chifukwa nthawi zambiri amakumana ndi “mavuto ndi zopweteka” monga kusayenda bwino kwa chuma kapena imfa ya mwana. Zimenezi zimawalepheretsa kukwaniritsa zimene amalakalaka pa moyo wawo.​—Salimo 90:10.

Ndiponso anthu ambiri amaona kuti moyo wawo “ulibe phindu lililonse ndipo ndi wachabechabe” chifukwa amaona kuti moyo ndi waufupi kwambiri. Iwo samvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthufe, ngakhale kuti tili ndi nzeru zotha kupanga zinthu zaluso kwambiri, timakhala ndi moyo waufupi chonchi. Komanso samamvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthufe timafa. Ngakhale munthu atakhala kuti sakukumana ndi mavuto aakulu pa moyo wake, amakhalabe ndi nkhawa chifukwa amadziwa kuti tsiku lina adzafa ndipo zonse zidzathera pomwepo.​—Mlaliki 3:19, 20.

Kodi Moyo Uzionekabe Ngati Wopanda Phindu Mpaka Kalekale?

Solomo, yemwe anali mfumu ya Isiraeli anafotokoza mwachidule zimene zimachitika pa moyo wathu. Iye anaona mmene anthu a m’nthawi yake ankagwirira ntchito mwakhama monga kulima, kukolola, kumanga nyumba ndiponso kusamalira mabanja awo, ngati mmenenso anthu amachitira masiku ano. Tinganene kuti iye ankadzifunsa kuti, ‘Kodi mapeto a  zonsezi n’chiyani?’ Iye anapeza kuti zinthu zonse zimene anthu amachita ndi “zachabechabe ndipo kuchita zimenezi kuli ngati kuthamangitsa mphepo.”​—Mlaliki 2:17.

Koma kodi Mfumu Solomo ankakhulupirira kuti chilichonse chimene munthu angachite ndi ‘chachabechabe ndiponso zili ngati kuthamangitsa mphepo’? Ayi, pamenepa iye ankangofotokoza zimene zimachitikira anthu opanda ungwirofe. Komabe Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti moyo wathu sudzakhala chonchi mpaka kalekale.

Kodi mungatsimikizire bwanji kuti zinthu zidzasinthadi? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani ziwiri zotsatirazi. Nkhanizi zikuthandizani kumvetsa chifukwa chake moyo umaoneka ngati wopanda phindu. Zikuthandizaninso kuona mmene vuto limeneli lidzathetsedwere komanso zimene mungachite kuti moyo wanu ukhale waphindu ngakhale panopa.