Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Mukakumana Ndi Mayesero

Zimene Mungachite Mukakumana Ndi Mayesero

 Zoti Achinyamata Achite

Zimene Mungachite Mukakumana Ndi Mayesero

YOSEFE​—GAWO 1

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Yosefe ndi mkazi wa Potifara

Chidule cha nkhaniyi: Yosefe anakana kugona ndi mkazi wa Potifara.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI GENESIS 39:1-12.

Kodi mukuganiza kuti nyumba ya Potifara inali yaikulu bwanji, nanga inali yokongola bwanji?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yosefe ankaoneka bwanji? (Zokuthandizani: Werenganinso vesi 6.)

․․․․․

Malinga ndi zimene zalembedwa mu vesi 8 ndi 9, kodi mukuganiza kuti Yosefe ankamva bwanji mumtima mwake pamene ankalankhula ndi mkazi wa Potifara, nanga mawu ake ankamveka bwanji?

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Kodi n’chiyani chikanachititsa Yosefe kulolera kuphwanya mfundo za makhalidwe abwino? (Zokuthandizani: Werengani Afilipi 2:12 ndipo ganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyi. Mwachitsanzo, kodi makolo ndi achibale a Yosefe anali kuti pa nthawiyi? Nanga anthu ena olambira Yehova anali kuti?)

․․․․․

  3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA  . . .

Kugwirizana pakati pa kudziletsa ndi kudzisungira ulemu.

․․․․․

Phindu limene anthu omwe amatsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino amapeza.

․․․․․

Kufunika kophunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikira.’ (Aheberi 5:14)

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Kodi ndi pa zinthu ziti pamene muyenera kukana motsimikiza mtima kuti musagonje pa mayesero oti muchite chiwerewere? (Zokuthandizani: Werengani ndipo ganizirani mozama malemba awa: Yobu 31:1; Salimo 119:37; Aefeso 5:3, 4.)

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati mulibe Baibulo uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.