Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Maulendo Akale Apanyanja Zamchere

Maulendo Akale Apanyanja Zamchere

Maulendo Akale Apanyanja Zamchere

Masiku ano anthu savutika poyenda maulendo owoloka nyanja zamchere chifukwa amatha kungokwera ndege. N’zochititsanso chidwi kuti ngakhale m’nthawi za m’Baibulo anthu ankayendanso maulendo ataliatali.

PAFUPIFUPI zaka 1,000 Khristu asanabwere, Mfumu Solomo inakonza zombo zapamadzi zomwe zinkayendera limodzi ndi zombo za mfumu ya ku Turo. Zombozi zinkabweretsa ku Isiraeli katundu wochokera m’madera akutali. (1 Mafumu 9:26-28; 10:22) M’zaka za m’ma 800 B.C.E., mneneri Yona anakwera chombo chopita ku Tariso kuchokera pa doko la ku Isiraeli lotchedwa Yopa, lomwe linali m’mphepete mwa nyanja ya Mediterranean. * (Yona 1:3) Komanso mtumwi Paulo anayenda panyanja kuchoka m’chigawo cha Kaisareya, ku Isiraeli, n’kukafika ku Potiyolo. Dera la Potiyolo lili ku Naples, m’dziko la Italy ndipo masiku ano limatchedwa Pozzuoli.​—Machitidwe 27:1; 28:13.

Akatswiri a mbiri yakale amadziwa kuti pofika m’nthawi ya Paulo, amalonda ochokera m’madera ozungulira nyanja ya Mediterranean ankakonda kupita ku India podutsa m’Nyanja Yofiira. Amadziwanso kuti pofika m’zaka za m’ma 150 C.E. amalonda ena ankafika mpaka ku China. * Koma panalinso ena amene analowera kumadera akumadzulo. Kodi anthu amenewa anakafika mpaka kuti?

Maulendo Oyambirira a Afoinike

Anthu oyenda panyanja anakhazikitsa misika m’madera osiyanasiyana a kumadzulo, zaka zambirimbiri nthawi ya Paulo isanafike. Akatswiri a mbiri yakale amakhulupirira kuti pofika mu 1200 B.C.E., Afoinike, omwe anachokera m’dera limene masiku ano limatchedwa Lebanon, anafika m’nyanja yamchere ya Atlantic. Cha mu 1100 B.C.E., iwowa anadutsa malire a nyanja ya Mediterranean ndi Atlantic omwe amadziwika ndi dzina loti Gibraltar ndipo anamanga mzinda womwe anautcha Gadir, m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic. Masiku ano mzindawu umatchedwa Cádiz ndipo uli m’dziko la Spain. Zinthu zina zimene zinkapezeka kumeneku ndi siliva amene ankakumbidwa m’migodi ya m’derali ndi miyala ina yamtengo wapatali, yomwe amalonda okhala m’derali ankagula m’madera ena podutsa m’nyanja ya Atlantic.

Wolemba mbiri yakale wa ku Greece, dzina lake Herodotus, analemba kuti cha m’ma 600 B.C.E. mfumu ya ku Iguputo, yotchedwa Farao Neko, inasonkhanitsa zombo zambiri za ku Foinike kumtunda kwenikweni kwa Nyanja Yofiira. Amene ankayendetsa zombozi ndi Afoinike omwewo. Cholinga cha mfumuyi chinali choti zombozi ziyende mozungulira Africa kuchokera kum’mawa mpaka kukafika kumadzulo.

Panthawiyi n’kuti Afoinike atayamba kalekale kufika m’madoko a ku Africa. Komabe, zinali zovuta kuyenda molowera kum’mwera kwa Africa podutsa m’nyanja ya Atlantic chifukwa cha mphepo zamkuntho ndiponso mafunde. Herodotus analemba kuti Afoinike anaona kuti ndi bwino kuti ulendowo auyambire m’Nyanja Yofiira n’kudzera kum’mawa kwa Africa, kulowera kum’mwera kuti akadutse m’nyanja ya Indian. Pakati pa mwezi wa May ndi June, iwo anakocheza zombozo m’dera lina. Anakhalapo ndithu moti anabzala mbewu mpaka kukolola ndipo kenako anapitiriza ulendo wawo. Herodotus anafotokoza kuti potha zaka zitatu, anthuwa anali atazungulira Africa yense ndipo analowa m’nyanja ya Mediterranean n’kukafikanso ku Iguputo.

Kumapeto kwa nkhani yake yonena za ulendowu, Herodotus anati nkhani zina zimene Afoinike ankasimba atafika ku Iguputo zinamuvuta kukhulupirira. Mwachitsanzo, iwo ananena kuti ali kum’mwera kwenikweni kwa Africa, dzuwa ankalionera kumanja kwawo. Zinalidi zovuta kwa munthu wa ku Greece wapanthawiyo kukhulupirira zimenezi chifukwa munthu amene wakhala moyo wake wonse kumpoto kwa dziko lapansi, nthawi zonse dzuwa amalionera kum’mwera. Motero akamayenda molowera kumadzulo, dzuwa amalionera kumanzere. Koma kudera la kum’mwera kwenikweni kwa Africa lotchedwa Cape of Good Hope, dzuwa limaonekera kumadzulo chifukwa derali lili kum’mwera kwa dziko lapansi. Choncho masana, munthu amene akuyenda molowera kumadzulo dzuwa amalionera kumanja.

Kwa zaka zambiri akatswiri a mbiri yakale akhala akutsutsana kwambiri pa zimene Herodotus analemba zokhudza ulendowu. Ambiri amaona kuti zinali zosatheka kuti anthu oyenda panyanja a nthawi imeneyo athe kuzungulira Africa yense. Komabe, akatswiri ena ambiri amakhulupirira kuti Farao Neko analamula zoti pakhale ulendo umenewo ndipo amakhulupiriranso kuti zinali zotheka kuyenda ulendo ngati umenewu panthawiyo. Amatero poganizira za luso komanso nzeru zimene anthu anali nazo panthawiyo. Mwachitsanzo, katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Lionel Casson, anati: “Zinali zotheka kuyenda ulendo ngati umenewu. Palibe chimene chikanalepheretsa gulu la Afoinike kuyenda ulendo ngati umenewu pa zaka zimene Herodotus anatchulazi.” N’zoona kuti palibe umboni wotsimikizira zonse zimene Herodotus analemba. Komabe, zimene analembazi zimatithandiza kudziwa khama limene ena anasonyeza pofuna kupeza njira zapanyanja zopita m’madera ena amene sankadziwika kalelo.

Pytheas Analowera Kumpoto

Kuwonjezera pa anthu a ku Foinike, panalinso anthu ena a m’madera ozungulira nyanja ya Mediterranean amene anayenda molowera chakumadzulo, kunyanja ya Atlantic. Agiriki oyendetsa zombo zapamadzi anayamba kulamulira madera osiyanasiyana ozungulira nyanja ya Mediterranean. Limodzi mwa madera amenewa linali dera la Massalia, lomwe masiku ano ndi mzinda wa ku France wotchedwa Marseilles. Mzindawu unatukuka kwambiri chifukwa amalonda amene ankafika kumeneku ankatha kuyenda panyanja ndiponso pamtunda. Kuchokera ku Massalia, amalondawa ankatumiza kumadera akumpoto zinthu zosiyanasiyana monga vinyo, mafuta, ndiponso miyala ya mkuwa ya m’madera ozungulira nyanja ya Mediterranean. Kumadera a kumpotoko, iwo ankagulako miyala ina yamtengo wapatali yopangira zinthu zosiyanasiyana. N’zoonekeratu kuti anthu a ku Massalia ankafuna atadziwa kumene miyala imeneyi inkachokera. Choncho cha mu 320 B.C.E., munthu wina wa ku Massalia, dzina lake Pytheas, anayamba ulendo wolowera kumpoto kuti akadzionere yekha.

Atabwerera kwawo, Pytheas analemba buku lotchedwa Ulendo Wapanyanja. Bukuli linali m’Chigiriki, koma mabuku oyambirirawo sapezekanso masiku ano. Komabe akatswiri osachepera 18 olemba mabuku akale anakopera mawu ena a m’bukuli. Ena mwa mawu amenewa amasonyeza kuti Pytheas anafotokoza mwatsatanetsatane zinthu zokhudza nyanja, mafunde, malo ndiponso anthu osiyanasiyana a m’madera amene anafikako. Iye ankagwiritsira ntchito kachipangizo kenakake kothandiza kudziwa mmene dzuwa lapendekekera. Akadziwa zimenezi ankatha kuwerengetsera mtunda umene wayenda.

Pytheas anali katswiri wa sayansi. Komabe, zikuoneka kuti sanayende ulendowu pongofuna kufufuza za sayansi basi. M’malomwake, akatswiri ena ananena kuti iye anatumidwa ndi anthu a malonda a ku Massalia omwenso anam’patsa ndalama zofunika pa ulendowu. Iwo ankafuna kuti iye akafufuze njira yapanyanja yopita kumadera akutali a kumpoto, kumene ankadziwa kuti kunkapezeka miyala yamtengo wapatali yosiyanasiyana. Ndiyeno kodi Pytheas anakafika kuti?

Anafika ku Brittany, Britain ndi Madera Ena

Zikuoneka kuti Pytheas anayenda mozungulira dera la Iberia ndipo analowera kumpoto kukafika ku Brittany podutsa m’mphepete mwa dera la Gaul. Atafika ku Brittany anaima pang’ono. Tikudziwa zimenezi chifukwa zimene anayeza zokhudza mmene dzuwa linapendekekera zimasonyeza kuti anali pamalo ena akumpoto kwa dera la Brittany. *

Anthu a ku Brittany anali akatswiri odziwa kupanga ndi kuyendetsa zombo zapamadzi ndipo ankachita malonda ndi anthu a ku Britain. Pytheas atachoka ku Brittany anafika ku dera la Cornwall lomwe lili kum’mwera chakumadzulo kwa Britain. Kumeneku kunali migodi yambiri ya miyala inayake yamtengo wapatali. Zikuoneka kuti Pytheas anazungulira chilumba cha Britain, chifukwa m’buku lake anafotokoza kukula kwa derali komanso mmene mapu ake angaonekere.

Ngakhale kuti njira yeniyeni imene Pytheas anadutsa sidziwika, n’kutheka kuti iye anadutsa pakati pa Britain ndi Ireland n’kukakocheza pachilumba cha Man. Tikutero chifukwa chakuti zimene analemba m’buku lake atayezanso kupendekeka kwa dzuwa zimasonyeza kuti anali pachilumbachi. Zikuoneka kuti kenako anayezanso kachitatu kupendekeka kwa dzuwa ali pachilumba cha Lewis chomwe chili pa gulu la zilumba zotchedwa Outer Hebrides, kufupi ndi dziko la Scotland. Atachoka kumeneku iye analowerabe kumpoto mpaka kukafika ku zilumba zotchedwa Orkney zomwe zili kumpoto kwa Scotland. Umboni wa zimenezi ndi woti wolemba mbiri yakale wina, dzina lake Pliny Wamkulu, anakopera zimene Pytheas analemba zoti zilumbazi zilipo 40.

Pytheas analemba kuti munthu atayenda pa chombo chapamadzi kwa masiku 6 kulowera kumpoto kwa Britain, angafike pachilumba cha Thule. Olemba mabuku akale angapo analemba zimene Pytheas anafotokoza kuti ku Thule dzuwa limakhala likuwalabe pakati pausiku. Pytheas analembanso kuti anthu atayenda ulendo wa tsiku limodzi kuchokera ku Thule angakafike kudera la madzi oundana. Akatswiri ambiri sagwirizana za malo enieni amene Pytheas anawatcha Thule. Ena amati ndi zilumba za Faeroe, ena amati ndi dziko la Norway, ndipo ena amatinso ndi dziko la Iceland. Koma olemba mabuku akale ankakhulupirira kuti Thule linali “dera lakumpoto kwenikweni kwa madera ena onse amene amatchulidwawa.”

Zikuoneka kuti Pytheas anabwerera ku Britain kudzera njira imene anadutsa popita ndipo panthawiyi anamaliza kuzungulira chilumba cha Britain. Koma sizikudziwika ngati iye anapitiriza ulendo mpaka kukafika kumadera am’mphepete mwa nyanja kumpoto kwa Ulaya asanabwerere m’chigawo chozungulira nyanja ya Mediterranean. Kaya zimenezi ndi zoona kapena ayi, Pliny Wamkulu anasonyeza kuti Pytheas anali katswiri wodziwa bwino za madera omwe anali ndi miyala yamtengo wapatali chifukwa iye ankakonda kugwiritsira ntchito zimene Pytheas analemba. Poyamba, miyala yamtengo wapataliyi inkapezeka m’madera akum’mwera m’mphepete mwa nyanja ya Baltic ndiponso ku dera lotchedwa Jutland, lomwe panopa ndi mbali ya dziko la Denmark. Pytheas sananene kuti anafika kumadera amenewa ndipo n’kutheka kuti iye anadziwa za maderawa pamene anali kumadoko am’madera akum’mawa kwa dziko la Britain.

Munthu winanso wa m’madera ozungulira nyanja ya Meditarranean amene akudziwika kuti analemba za ulendo wake wopita ku Britain, ndi Julius Caesar. M’chaka cha 55 B.C.E, iye anafika kum’mwera kwa chilumba cha Britain. Pofika m’chaka cha 6 C.E., magulu enanso a anthu ochokera ku Rome analinso atafika kale kumadera ena akumpoto kwa Jutland.

Anatsegula Anthu M’maso

Afoinike ndi Agiriki anatsegula m’maso anthu ophunzira am’madera ozungulira nyanja ya Mediterranean. Moti anthuwa anadziwanso za madera akunyanja ya Atlantic, mpaka kukafika kumadera akum’mwera kwa Africa, ndiponso a ku Arctic, komwe ndi kumpoto kwenikweni kwa dzikoli. Nthawi imeneyo, anthu ankakonda kupita kumadera osiyanasiyana, kuchita malonda, kuphunzira zambiri zokhudza dzikoli ndiponso kuyenda maulendo ataliatali. Chifukwa cha zimenezi anthu anatseguka m’maso kwambiri.

Mabuku ofotokoza za maulendo amenewa omwe alipobe panopa, ndi okhudza maulendo ochepa chabe pa maulendo ambiri amene akatswiri olimba mtima oyendetsa zombo zapamadzi akale anayenda. Sizikudziwika kuti ndi anthu angati amene anayenda maulendo angati amenewa n’kubwerera kwawo bwinobwino koma osalemba za maulendowo. Komanso sizikudziwika kuti ndi angati amene anayenda maulendo otero koma osabwereranso kwawo. Palibe mabuku a mbiri yakale amene amafotokoza zimenezi. Komabe mabuku amene alipo amatithandiza kudziwa mmene Chikhristu chinafalikira kalelo.​—Onani  bokosi lili pamwambapo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Akatswiri ambiri amati Tariso ndi dera limene lili kum’mwera kwa dziko la Spain, lomwe Agiriki ndiponso Aroma olemba mabuku ankalitcha kuti Tartessus.

^ ndime 4 Kuti mudziwe zambiri zokhudza maulendo apanyanja olowera kumadera a kum’mawa, onani nkhani yakuti “Kodi Amishonale Analalikira Kum’mawa Mpaka Kukafika Kuti?” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2009.

^ ndime 16 Tikatengera za masamu odziwira malo masiku ano, derali lili pa 48° 42’ chakumpoto.

[Bokosi patsamba 29]

 Uthenga Wabwino “Unalalikidwa M’chilengedwe Chonse”

Nthawi ina pakati pa chaka cha 60 ndi 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Kodi iye ankatanthauza kuti panthawi imeneyi Akhristu anali atafika kale ku India, ku Far East, ku Africa, ku Spain, ku Gaul, ku Britain, ku Baltic, ndiponso kudera limene Pytheas analitcha kuti Thule? N’kutheka kuti Akhristu analidi atafika kumadera onsewa, komabe sitinganene motsimikiza.

Koma chomwe tikudziwa n’chakuti uthenga wabwino unalalikidwa m’madera ambiri. Mwachitsanzo, Ayuda ndiponso ena amene anangolowa Chikhristu pa Pentekoste mu 33 C.E., anakalalikira za chikhulupiriro chawo mpaka kumadera monga Pati, Elamu, Medi, Mesopotamiya, Arabiya, Asia Minor, ku madera ena a Libiya amene ali kufupi ndi Kurene ndiponso Roma, kapena tingoti dziko lonse lodziwika kwa anthu amene ankawerenga makalata a Paulo.​—Machitidwe 2:5-11.

[Chithunzi/​Mapu pamasamba 26, 27]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Herodotus ananena kuti ali kum’mwera kwenikweni kwa Africa, Afoinike ankaliona dzuwa kumanja kwawo

[Mapu]

AFRICA

NYANJA YA MEDITERRANEAN

NYANJA YA INDIAN

NYANJA YA ATLANTIC

[Chithunzi/​Mapu pamasamba 28, 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ulendo wautali woyenda panyanja wa Pytheas wa ku Greece

[Mapu]

IRELAND

ICELAND

NORWAY

Nyanja ya Kumpoto

BRITAIN

BRITTANY

IBERIAN PENINSULA

KUMPOTO KWA AFRICA

NYANJA YA MEDITERRANEAN

Marseilles