Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Yehova Amaonera Atumiki Ake Okhulupirika

Mmene Yehova Amaonera Atumiki Ake Okhulupirika

Mmene Yehova Amaonera Atumiki Ake Okhulupirika

“Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Poona mawu a wamasalmo amenewa, ena angaganize kuti Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi osafunika ndipo ali ngati fumbi basi. Koma kodi Yehova amawaonadi choncho atumiki ake? Mawu a palembali sanalembedwe n’cholinga chosonyeza kufunika kwa atumiki a Yehova. Koma analembedwa pofuna kusonyeza kuti Yehova amachitira chifundo atumiki akewo akachimwa n’kulapa mochokera pansi pa mtima. Yehova amachita zimenezi chifukwa amadziwa kuti iwo ndi opanda ungwiro choncho samayembekezera kuti azichita zimene Iye akudziwa kuti sangathe. Ndiye kodi Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi ofunika motani?

Anthu ena amaganiza kuti atumiki a Mulungu amasiku ano ndi osanunkha kanthu ndipo ali ngati fumbi limene limakakamira kunsi kwa nsapato zawo. Koma umu si mmene Mulungu amawaonera. Mawu amene Yesu anauza ophunzira ake akutsimikizira zimenezi. Iye anawauza kawiri konse kuti iwo ndi “ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.” Pofotokoza za timbalameti, iye ananena kuti “palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa” ndiponso kuti “palibe ngakhale imodzi mwa izo imaiwalika kwa Mulungu.”​—Mateyo 10:29-31; Luka 12:6, 7.

Mpheta zimapezeka kwambiri ku Palestine. Kuyambira kale, mbalamezi zakhala zikugulitsidwa m’misika ya ku Middle East. Anthu akafuna kudya mbalamezi, ankazisosola n’kuziika kumpani kuti aziotche. Choncho, kwa anthu okonda kudya mpheta, iliyonse inali yofunika kwambiri. Komabe n’zosakayikitsa kuti anthu ena ankanyoza mpheta chifukwa zinali zotchipa kwambiri komanso amene ankakonda kugula anali anthu osauka. Koma malinga ndi mawu a Yesu, Yehova ankadziwa ngakhale mpheta imodzi yokha ikafa. Pofuna kutsindika mfundo yakuti atumiki a Mulungu okhulupirika ndi ofunika kwambiri, Yesu anagwiritsanso ntchito chitsanzo china. Iye anati: “Tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga.”​—Mateyo 10:30.

Kodi munayamba mwayesapo kuwerenga tsitsi lam’mutu mwa munthu winawake? Yehova amachita zimenezi ndipo amadziwa kuchuluka kwa tsitsi la m’mutu mwathu. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yehova amachita chidwi kwambiri ndi atumiki ake okhulupirika? Iye amayesetsa kudziwa munthu aliyense bwinobwino, ngakhale kuchuluka kwa tsitsi lake. Zimenezi zikusonyeza kuti iye amawakonda kwambiri atumiki ake.

Inde, Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi ofunika kwambiri ndipo amayamikira zimene iwo amachita pomutumikira. Iye adzaonetsetsa kuti aliyense walandira mphoto yake.​—Akolose 3:24.