Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi zinthu zofunika pa moyo wathu, monga chakudya, zidzatheratu padzikoli?

Kodi zinthu zofunika pa moyo wathu, monga chakudya, zidzatheratu padzikoli?

 Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi zinthu zofunika pa moyo wathu, monga chakudya, zidzatheratu padzikoli?

▪ Dziko lapansili ndi lokongola kwambiri ndipo lili ndi zinthu zonse zofunika pa moyo. Komabe, chiwerengero cha anthu chikukula kwabasi ndiponso zinthu zambiri zofunikira pa moyo zikuwonongeka modetsa nkhawa kwambiri. Choncho, mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi tsiku lina sitidzapeza kuti chakudya ndi zinthu zina zofunika pa moyo zatheratu? Kodi zinthu zimenezi zidzakhalapobe zokwanira padzikoli?’

Ngati muli ndi mafunso amenewa, mungalimbe mtima mutaganizira lonjezo limene Mulungu anapereka kwa anthu zaka 4,000 zapitazo, lakuti: “Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekayi.” (Genesis 8:22) Tsiku lililonse sitikayika kuti dzuwa lituluka, motero tisamakayikenso kuti zinthu zofunika pa moyo zidzapitirizabe kupezeka padzikoli.

M’chaka cha 2004, kunatulutsidwa lipoti lofotokoza za chakudya lamutu wakuti, “Kodi Dzikoli Lili ndi Chakudya Chokwanira Tonsefe?” Mu lipotili, Alex Kirby, yemwe ndi mtolankhani wa zachilengedwe, ananena kuti: “Dzikoli lili ndi chakudya chokwanira aliyense. Kungoti nthawi zambiri chakudyachi sichipezeka kumene chikufunikira, kapena chimakhala chokwera mtengo, kapenanso chimakhala choti sichingasungidwe kwa nthawi yaitali. Choncho, atsogoleri andale ndi amene angachititse kuti aliyense akhale ndi chakudya chokwanira, osati akatswiri a zaulimi.” Amene amayang’anira chakudya ndiponso zinthu zina zofunika padzikoli, atamagwira bwino ntchito yawo sipangakhale vuto la kusowa kwa chakudya. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Aisiraeli, Mulungu anapereka malangizo omveka bwino othandiza kuti nthaka isamaguge. Lemba la Levitiko 25:4 limanena zimene Mulungu anauza Aisiraeli. Iye anati: “Chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale sabata lakupumula la dziko. . . Usamabzala m’munda mwako.” Ngakhale kuti iwo sankalima chaka cha 7 chilichonse, Mulungu anawalonjeza kuti iye adzaonetsetsa kuti aliyense akupeza zinthu zabwino zambiri ndiponso sadzakhala ndi nkhawa yoti chakudya chingawathere.​—Levitiko 26:3-5.

Masiku ano anthu ena akuyesetsa kukonza zimene anthu awononga padzikoli, komabe ambiri akuona kuti ayamba kuchita zimenezi madzi atafika kale m’khosi. Lemba la Chivumbulutso 11:18 limanena za njira yokhayo imene ingathetseretu vutoli. Lembali limanena kuti Yehova ‘adzawononga owononga dziko lapansi.’ Yehova adzawononga anthu amene amawononga dzikoli komanso adzaonetsetsa kuti dzikoli lili ndi zinthu zofunikira zokwanira aliyense. Anthu onse osamvera Mulungu ndiponso onse amene amawononga dzikoli chifukwa cha mtima wadyera adzawonongedwa. Koma anthu ofunitsitsa kumvera Yehova adzalandira madalitso otchulidwa pa lemba la Salmo 72:16 lomwe limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”

Chifukwa cha chikondi ndi nzeru zake zakuya, Yehova anakonza zakuti anthu onse adzakhale padziko lapansi n’kumalisamalira kuti likhale paradaiso. (Genesis 1:28) Mu ulamuliro wake, anthu omvera adzaphunzira kugwiritsa ntchito mwanzeru zinthu zachilengedwe ndipo zinthu zofunika padzikoli sizidzatha. Timasangalala kwambiri chifukwa Mulungu wathu ndi woolowa manja ndiponso ndi wachikondi kwambiri moti adzakwaniritsa zokhumba za aliyense.​—Salmo 145:16.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Atsogoleri andale ndi amene angachititse kuti aliyense akhale ndi chakudya chokwanira, osati akatswiri a zaulimi”