Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Yesu

Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Yesu

“Atate, . . . lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.”—YOH. 17:1.

1, 2. Fotokozani zimene Yesu anachita ndi atumwi ake okhulupirika atamaliza chikondwerero cha Pasika mu 33 C.E.

MADZULO a pa Nisani 14 m’chaka cha 33 C.E, Yesu ndi ophunzira ake anachita chikondwerero cha Pasika. Chikondwerero chimenechi chinkawakumbutsa mmene Mulungu anapulumutsira makolo awo ku ukapolo m’dziko la Iguputo. Koma ophunzira a Yesu okhulupirika ankayembekezera kupulumutsidwa m’njira yapadera kwambiri ndiponso ‘kulanditsidwa kwamuyaya.’ Tsiku lotsatira, Mtsogoleri wawo amene anali wosalakwa, anaphedwa ndi adani ake. Koma zimenezi zinabweretsa madalitso chifukwa magazi a Yesu anatsegula njira kuti anthu adzapulumutsidwe ku uchimo ndi imfa.—Aheb. 9:12-14.

2 Potithandiza kuti tisaiwale zimene anachitazo, Yesu anayambitsa mwambo watsopano woti uzichitika chaka ndi chaka m’malo mwa Pasika. Poyambitsa mwambowu, iye ananyema mkate wopanda chofufumitsa n’kupereka kwa atumwi ake 11 okhulupirika. Iye anati: “Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.” Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu ya vinyo wofiira n’kunena kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.”—Luka 22:19, 20.

3. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atamwalira? (b) Kodi tingafunse mafunso ati okhudza pemphero la Yesu lomwe lili pa Yohane chaputala 17?

3 Pangano la Chilamulo la pakati pa Mulungu ndi Aisiraeli linali litatsala pang’ono kutha. Yesu atamwalira, pangano limeneli linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano la pakati pa Yehova ndi Akhristu odzozedwa. Yesu ankafunitsitsa kuti mtundu watsopanowu zinthu ziziuyendera bwino. Aisiraeli anali ogawanika pa nkhani ya chipembedzo komanso zinthu zina ndipo zimenezi zinanyozetsa  kwambiri dzina la Mulungu. (Yoh. 7:45-49; Mac. 23:6-9) Yesu sankafuna kuti otsatira ake akhale ngati Aisiraeliwo, koma azigwirizana kuti onse pamodzi azilemekeza dzina la Mulungu. Kodi Yesu anachita chiyani kuti zimenezi zitheke? Anapereka pemphero logwira mtima lomwe ndi losangalatsa kwambiri kuliwerenga. (Yoh. 17:1-26; onani chithunzi choyamba.) Panopa tingafunse kuti, “Kodi Mulungu anayankha pemphero la Yesu limeneli?” Komanso tiyenera kudzifunsa kuti, “Kodi ineyo ndikuchita zinthu mogwirizana ndi pempheroli?”

ZINTHU ZIMENE ZINALI ZOFUNIKA KWA YESU

4, 5. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu oyamba a pemphero la Yesu? (b) Kodi Yehova anayankha bwanji zimene Yesu anapempha zokhudza tsogolo lake?

4 Yesu analankhula ndi ophunzira ake mpaka usiku kuti awaphunzitse zinthu zamtengo wapatali zochokera kwa Mulungu. Kenako anayang’ana kumwamba n’kupemphera kuti: “Atate, nthawi yafika, lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni. Inu mwamupatsa ulamuliro pa anthu onse, kuti onse amene inu mwamupatsa, awapatse moyo wosatha. . . . Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa. Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.”—Yoh. 17:1-5.

5 Kumayambiriro kwa pemphero lakeli, Yesu anatchula zinthu zimene ankaona kuti ndi zofunika kwambiri. Choyamba ananena zokhudza kulemekeza Atate wake wakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi chinthu choyamba chimene Yesu ananena mu pemphero lake lachitsanzo. Paja iye anati: “Atate, dzina lanu liyeretsedwe.” (Luka 11:2) Chachiwiri, Yesu anapempherera ophunzira ake kuti Mulungu “awapatse moyo wosatha.” Kenako anapempherera zofuna zake. Anapempha kuti: “Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.” Yehova anapatsa Mwana wake wokhulupirikayu zinthu zambiri kuposa zimene anapempha chifukwa anamupatsa “dzina lapamwamba” kuposa la mngelo wina aliyense.—Aheb. 1:4.

‘KUDZIWA MULUNGU WOONA’

6. (a) Kodi atumwi anafunika kuchita chiyani kuti apeze moyo wosatha? (b) Nanga tikudziwa bwanji kuti iwo anakwanitsa kuchita zimenezo?

6 Kenako Yesu anatchula zimene anthu ochimwafe tiyenera kuchita kuti tilandire mphatso ya moyo wosatha. (Werengani Yohane 17:3.) Iye ananena kuti tiyenera kupitiriza ‘kuphunzira ndi kudziwa’ za Mulungu ndi Khristu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Choyamba, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiphunzire za Yehova ndiponso Mwana wake. Chachiwiri, tiyenera kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo. Atumwi a Yesu ankachita zimenezi ndipo Yesu ananena m’pemphero lake kuti: “Mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo. Iwo awalandira.” (Yoh. 17:8) Koma kuti atumwi okhulupirikawo apeze moyo wosatha, anafunika kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso kuwatsatira pa moyo wawo. Kodi iwo anakwanitsa kuchita zimenezi kwa moyo wawo wonse? Inde, anakwanitsa. Tikutero chifukwa chakuti mayina a atumwiwa analembedwa pa miyala 12 yomangira maziko a Yerusalemu Watsopano.—Chiv. 21:14.

7. (a) Kodi mawu akuti “kudziwa” Mulungu amatanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani kudziwa Mulungu n’kofunika kwambiri?

7 Akatswiri ena a chilankhulo cha Chigiriki ananena kuti mawu amene anawamasulira kuti “akamaphunzira ndi kudziwa” angamasuliridwenso kuti “ngati sasiya kudziwa” kapena kuti “akapitiriza kudziwa.” Mawu onsewa angatithandize kudziwa zoyenera kuchita. Akusonyeza kuti munthu amafunika kupitiriza kuphunzira za Mulungu kuti afike pomudziwa bwino. Komatu kudziwa Mulungu  kumatanthauza zambiri osati kungodziwa makhalidwe ake ndi cholinga chake. Kumatanthauzanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba komanso kugwirizana ndi atumiki ake. Paja Baibulo limanena kuti: “Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu.” (1 Yoh. 4:8) Munthu amene amadziwa bwino Mulungu amamumvera. (Werengani 1 Yohane 2:3-5.) Kunena zoona, kukhala m’gulu la anthu odziwa Yehova ndi mwayi waukulu kwambiri. Koma zimene zinachitikira Yudasi Isikariyoti zikusonyeza kuti ubwenzi umenewu ukhoza kusokonekera. Choncho tiyeni tiziyesetsa kuulimbitsa. Tikatero, tidzakhala oyenera kulandira mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosatha.—Mat. 24:13.

“CHIFUKWA CHA DZINA LANU”

8, 9. (a) Kodi cholinga chachikulu cha Yesu pa utumiki wake chinali chiyani? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anakana kutsatira mwambo uti wachipembedzo?

8 Tikawerenga pemphero la Yesu lopezeka pa Yohane chaputala 17, sitingakayikire zoti Yesu ankakonda kwambiri atumwi akewo komanso ophunzira ake am’tsogolo. (Yoh. 17:20) N’zoona kuti Yesu ankafuna kuti anthufe tipulumuke. Komabe tiyenera kuzindikira kuti nkhani yofunika kwambiri kwa Yesu ndi kuyeretsa ndiponso kulemekeza dzina la Atate wake. Kuchokera pachiyambi mpaka kumapeto a utumiki wake, cholinga chake chachikulu chinali chimenechi. Mwachitsanzo, Yesu ali m’sunagoge ku Nazareti analengeza za ntchito imene Yehova anamupatsa. Iye anawerenga mpukutu wa Yesaya pamene panalembedwa kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka.” Apatu Yesu ayenera kuti anatchula bwinobwino dzina la Mulungu pamene ankawerenga mpukutuwu.—Luka 4:16-21.

9 Malinga ndi zimene olemba mbiri yachiyuda amanena, Yesu asanabwere padziko lapansi, atsogoleri achipembedzo ankaletsa anthu kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. N’zodziwikiratu kuti Yesu anakana kutsatira mwambo wosemphana ndi Malembawo. Iye anauza anthu amene ankamutsutsa kuti: “Ndabwera m’dzina la Atate wanga, ndipo simunandilandire, koma wina akanabwera m’dzina lake, mukanamulandira ameneyo.” (Yoh. 5:43) Ndiyeno  kutangotsala masiku ochepa kuti aphedwe, Yesu ananena cholinga chachikulu pa moyo wake pamene ankapemphera kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” (Yoh. 12:28) M’pake kuti m’pemphero lonse limene tikukambiranali Yesu anasonyeza kuti ankafunitsitsa kuti dzina la Atate wake lilemekezedwe.

10, 11. (a) Kodi Yesu anachita chiyani podziwitsa anthu dzina la Atate wake? (b) Kodi cholinga cha ophunzira a Yesu chiyenera kukhala chiyani?

10 M’pemphero lake, Yesu ananena kuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. Anali anu, koma munawapereka kwa ine, ndipo iwo asunga mawu anu. Komanso, ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwera kwa inu, koma iwo adakali m’dzikoli. Atate Woyera, ayang’anireni chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili.”—Yoh. 17:6, 11.

11 Pali zambiri zimene Yesu anachita podziwitsa ophunzira ake dzina la Atate wake osati kungowaphunzitsa katchulidwe kake. Iye anawauzanso zimene dzinalo likuimira. Anawafotokozera makhalidwe abwino a Mulungu komanso mmene amachitira zinthu ndi anthufe. (Eks. 34:5-7) Panopa Yesu ali kumwamba ndipo akupitiriza kuthandiza ophunzira ake kuti aziuza ena za dzina la Yehova padziko lonse lapansi. Kodi cholinga cha ophunzira a Yesu pogwira ntchitoyi n’chiyani? N’choti athandize anthu ambiri kukhala ophunzira a Yesu dziko loipali lisanathe. Ndiyeno pamapeto pake, Yehova adzapulumutsa anthu ake okhulupirika ndipo dzina lake lidzalemekezedwa kwambiri.—Ezek. 36:23.

“KUTI DZIKO LIKHULUPIRIRE”

12. Kodi tiyenera kuchita zinthu zitatu ziti kuti tigwire bwino ntchito yathu yopulumutsa anthu?

12 Yesu ali padziko lapansi, anayesetsa kwambiri kuti athandize ophunzira ake kusintha makhalidwe awo. Iwo anayenera kuchita zimenezi kuti amalize ntchito imene Yesu anawasiyira. Yesu ananena m’pemphero lake kuti: “Monga mmene munanditumizira ine m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko.” Iye anatchula zinthu zitatu zimene zingawathandize kugwira bwino ntchito yopulumutsa anthuyi. Choyamba, anapemphera kuti ophunzira ake asakhale mbali ya dziko la Satana loipali. Chachiwiri, anapemphera kuti iwo ayeretsedwe chifukwa chotsatira Mawu a Mulungu. Chachitatu, anapempha mobwerezabwereza kuti ophunzira ake azikondana ndiponso kugwirizana monga mmene zilili pakati pa iye ndi Atate wake. Choncho tiyenera kudzifufuza ndiponso kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimachita zinthu mogwirizana ndi zinthu zitatu zimene Yesu anapemphazi?’ Yesu anasonyeza kuti ngati ophunzira ake achita zimenezi, ‘dziko likhulupirira kuti iye anatumidwa ndi Mulungu.’—Werengani Yohane 17:15-21.

Akhristu oyambirira anathandizidwa ndi mzimu woyera kuti akhale ogwirizana (Onani ndime 13)

13. Kodi pemphero la Yesu linayankhidwa bwanji m’nthawi ya atumwi?

13 Tingaone kuti pemphero la Yesuli linayankhidwa tikamaphunzira buku la Machitidwe a Atumwi, limene latsatizana ndi mabuku anayi a Uthenga Wabwino. Pakati pa Akhristu oyambirira panali Ayuda, anthu a mitundu ina, olemera, osauka, akapolo ndiponso mabwana. Choncho zikanakhala zovuta kuti onsewa azigwirizana bwinobwino. Komabe onse ankagwirizana kwambiri moti Baibulo limanena kuti anali ngati ziwalo zosiyanasiyana za thupi limodzi, lomwe mutu wake ndi Yesu. (Aef. 4:15, 16) Izitu zinali zodabwitsa kwambiri m’dziko la Satana limene anthu ake sagwirizana. Tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa ndi amene akuchititsa kuti zimenezi zitheke pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera.—1 Akor. 3:5-7.

Anthu a Yehova padziko lonse ndi ogwirizana (Onani ndime 14)

14. Kodi pemphero la Yesu layankhidwa bwanji masiku ano?

14 N’zomvetsa chisoni kuti atumwi atamwalira, mgwirizanowu unasokonekera. Malinga  ndi ulosi wa m’Baibulo, mpatuko waukulu unayamba ndipo zinachititsa kuti pakhale matchalitchi osiyanasiyana. (Mac. 20:29, 30) Koma m’chaka cha 1919, Yesu anamasula ophunzira ake odzozedwa ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga ndipo anawagwirizanitsa. (Akol. 3:14) Kodi ophunzirawa athandiza bwanji anthu m’dzikoli pogwira ntchito yolalikira? Iwo athandiza kuti anthu oposa 7 miliyoni ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” akhale m’gulu la “nkhosa zina” zimene zimagwirizana ndi Akhristu odzozedwa. (Yoh. 10:16; Chiv. 7:9) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova wayankhadi pemphero la Yesu lakuti: “Dziko lidziwe kuti inu munandituma ine, ndi kuti munawakonda iwo mmene munandikondera ine.”—Yoh. 17:23.

MAWU OMALIZA OLIMBIKITSA KWAMBIRI

15. Kodi Yesu anati chiyani popempherera Akhristu odzozedwa?

15 Madzulo a pa Nisani 14, Yesu analemekeza atumwi ake pochita nawo pangano kuti akalamulire nawo mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30; Yoh. 17:22) Ndiyeno ponena za odzozedwa onse, Yesu ananena m’pemphero lakeli kuti: “Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale, kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.” (Yoh. 17:24) A nkhosa zina sachita nsanje akaganizira mwayi umene odzozedwa ali nawo. M’malomwake, amasangalala ndipo umenewu ndi umboni wakuti Akhristu onse oona ndi ogwirizana.

16, 17. (a) Kodi kumapeto kwa pemphero lake, Yesu ananena kuti apitiriza kuchita chiyani? (b) Nanga ifeyo tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

16 Atsogoleri a zipembedzo akuchititsa kuti anthu ambiri azinyalanyaza umboni wakuti Yehova ali ndi gulu lake logwirizana limene limamudziwa bwino. Umu ndi mmene zinalilinso m’nthawi ya Yesu. N’chifukwa chake Yesu anamaliza pemphero lake ndi mawu olimbikitsa akuti: “Atate wolungama, ndithudi dziko silinakudziweni, koma ine ndikukudziwani ndipo awa adziwa kuti inu munandituma. Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”—Yoh. 17:25, 26.

17 Palibe amene angatsutse zoti Yesu wachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake. Popeza iye ndi Mutu wa mpingo, akupitiriza kutithandiza pamene tikuuza ena za dzina la Atate wake ndiponso cholinga chake. Tiyeni tipitirize kumugonjera pomvera ndi mtima wonse lamulo lake lakuti tizilalikira ndiponso kuphunzitsa anthu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 10:42) Tiziyesetsanso kukhalabe ogwirizana. Tikatero tidzasonyeza kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero la Yesu. Izi zidzalemekeza kwambiri dzina la Yehova komanso zidzathandiza kuti tidzapeze moyo wosatha.