Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu

Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu

“Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero . . . chifukwa munalenga zinthu zonse.”—CHIV. 4:11.

1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova?

ANTHU ambiri amanena kuti amangokhulupirira zinthu zokhazo zimene angathe kuziona. Kodi anthu otero tingawathandize bwanji kuti azikhulupirira Yehova? Paja Baibulo limati: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yoh. 1:18) Nanga ifeyo tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova, yemwe ndi ‘Mulungu wosaoneka’? (Akol. 1:15) Choyamba, tiyenera kudziwa zikhulupiriro zimene zimalepheretsa anthu kudziwa zoona zokhudza Yehova. Kenako tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo pogubuduza maganizo ‘otsutsana ndi kudziwa Mulungu.’—2 Akor. 10:4, 5.

2, 3. Kodi ndi ziphunzitso ziwiri ziti zimene zimalepheretsa anthu kudziwa zoona zokhudza Mulungu?

2 Chiphunzitso chimodzi chofala kwambiri chimene chimalepheretsa anthu kudziwa zoona zokhudza Mulungu ndi chakuti zamoyo zinangokhalako zokha. Zimenezi n’zosemphana ndi zimene Baibulo limanena ndipo sizithandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo. Zimachititsa anthu kuganiza kuti moyo wa anthu ulibe cholinga chilichonse.

3 Palinso atsogoleri ena a matchalitchi omwe amaphunzitsa kuti chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lapansi ndi zamoyo zonse zimene zili mmenemo, zangokhalapo kwa zaka masauzande ochepa chabe. N’kutheka kuti anthu amenewa amalemekeza kwambiri Baibulo. Koma amakhulupirira kuti masiku amene Mulungu anagwira ntchito yolenga zinthu zonse ndi a maola 24 enieni. Choncho amanena kuti dzikoli linalengedwa zaka masauzande ochepa zapitazo. Iwo amanyalanyaza umboni wamphamvu umene asayansi apeza, womwe umatsutsana ndi zimene amakhulupirirazo. Zimene anthu amenewa amaphunzitsa sizilemekeza Baibulo chifukwa zimachititsa kuti anthu azinena kuti Baibulo si lolondola. Anthu amene amakhulupirira zimenezi ali ngati anthu a m’nthawi ya atumwi omwe anali  odzipereka potumikira Mulungu ‘koma sankamudziwa molondola.’ (Aroma 10:2) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji Mawu a Mulungu pogubuduza ziphunzitso “zozikika molimba” zimenezi? * Tingachite zimenezi pokhapokha ngati titayesetsa kudziwa molondola zimene Baibulo limaphunzitsa.

MUNTHU AMAKHULUPIRIRA ZINTHU AKAPEZA UMBONI KOMANSO ZIFUKWA ZOMVEKA

4. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu?

4 Baibulo limasonyeza kuti kuphunzira zinthu n’kofunika kwambiri. (Miy. 10:14) Yehova amafuna kuti tizikhulupirira zinthu chifukwa chakuti tapeza umboni komanso zifukwa zomveka osati chifukwa chongotsatira nzeru za anthu kapena ziphunzitso zachipembedzo. (Werengani Aheberi 11:1.) Koma kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu, choyamba tiyenera kupeza umboni weniweni wakuti Yehova aliko. (Werengani Aheberi 11:6.) Umboni umenewu ukhoza kupezeka ngati munthu atafufuza ndiponso kuganizira mozama zimene wapezazo.—Aroma 12:1.

5. Kodi umboni wina wosonyeza kuti kuli Mulungu tingaupeze kuti?

5 Mtumwi Paulo anatchula umboni wina wotsimikizira kuti Mulungu aliko ngakhale kuti sitingamuone. Ponena za Yehova, Paulo analemba kuti: “Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.” (Aroma 1:20) Kodi mungathandize bwanji munthu amene amakayikira zoti kuli Mulungu kuti ayambe kukhulupirira zimene Paulo ananenazi? Mwina mungachite bwino kukambirana naye umboni umene wafotokozedwa m’nkhani ino, wosonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu komanso nzeru.

CHILENGEDWE CHIMASONYEZA KUTI MULUNGU NDI WAMPHAMVU

6, 7. Kodi zinthu ziwiri zimene zimateteza dzikoli zimasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wamphamvu?

6 Panopa tikambirana zinthu ziwiri zimene zimasonyeza kwambiri kuti Mulungu ndi wamphamvu. Choyamba, m’mlengalenga muli mpweya wosiyanasiyana umene umateteza dziko. Pali miyala imene imayenda m’mlengalenga yomwe ikhoza kuwononga zinthu padzikoli. Koma ikamadutsa mpweyawu imayaka n’kupserera moti sifika padziko. Zimenezi zimachititsa kuti nthawi zina usiku kumwamba kuziwala kwambiri ndipo zimaoneka ngati nyenyezi imene yathothoka.

7 Chachiwiri, pali mphamvu inayake imene imachokera pansi pa nthaka yomwe imatitetezanso. Pansi pa nthaka pali chiphalaphala chotentha kwambiri chomwe chimatulutsa mphamvu imeneyi. Mphamvuyi imatchinga dzikoli n’kuliteteza kuti lisapse ndi mphamvu yochokera kudzuwa. Zinthu ziwirizi zimasonyezeratu kuti Yehova “ali ndi mphamvu zambiri.”—Werengani Yesaya 40:26.

CHILENGEDWE CHIMASONYEZA KUTI MULUNGU NDI WANZERU

8, 9. Kodi nzeru za Yehova zimaoneka bwanji m’zinthu zimene analenga?

8 Tiyeni tsopano tikambirane zinthu zimene zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru. Tayerekezerani kuti muli mumzinda wokhala ndi mpanda mmene muli anthu ambirimbiri. Koma palibiretu njira yoti madzi abwino azilowera mumzindawo kapena yoti zinyansi zizichotsedwa. Mzindawo sungachedwe kuipa kwambiri moti anthu sangakhalemo. Dzikoli lili ngati mzinda wampandawu. Palibe njira yoti madzi atsopano azilowera ndipo n’zosatheka kuchotsa zinyansi kupititsa kwina. Ngakhale zili choncho,  zamoyo mabiliyoni ambiri zakhala bwinobwino padzikoli kwa zaka zambirimbiri. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Zimatheka chifukwa chakuti dzikoli lili ndi njira zake zokonzera zinthu.

9 Taganizirani zimene zimachitika ndi mpweya wabwino umene timapuma. Zamoyo mabiliyoni ambiri zikamapuma, zimagwiritsa ntchito mpweyawu n’kutulutsa woipa. Koma mpweya wabwinowu sutha ndipo woipawo sudzaza m’mlengalenga. Kodi n’chiyani chimachitika? Zomera zimagwiritsa ntchito mpweya woipawu, kuwala kwa dzuwa, madzi ndiponso mchere wa m’nthaka kuti zipange chakudya chake. Pochita zimenezi, zomerazo zimatulutsanso mpweya wabwino umene timapuma. Apa tingati Yehova amagwiritsa ntchito zomera kuti apatse ‘anthu onse moyo ndi mpweya.’ (Mac. 17:25) Kunena zoona Yehova ali ndi nzeru zodabwitsa.

10, 11. Kodi agulugufe ena ndi atombolombo amasonyeza bwanji nzeru za Yehova?

10 Nzeru za Yehova zimaonekanso tikaganizira zamoyo zambirimbiri zimene zili padzikoli. Anthu amanena kuti padzikoli pali mitundu ya zamoyo pakati pa 2 miliyoni ndi 100 miliyoni. (Werengani Salimo 104:24.) Tiyeni tione zamoyo zina zimene zimasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru.

Maso a tombolombo amasonyeza kuti Mulungu ndi wanzeru. Pachithunzichi, disoli alikulitsa (Onani ndime 11)

11 Chitsanzo choyamba ndi mtundu wina wa agulugufe. Kaubongo ka agulugufe amenewa n’kakang’ono kuposa kanjere ka mpiru. Koma angathe kuuluka mtunda wa makilomita pafupifupi 3,000 kuchokera ku Canada kupita kunkhalango ina ya ku Mexico osasochera. Iwo amaona dzuwa kuti adziwe kolowera. Yehova anakonza kaubongoka m’njira yoti agulugufewo asamasokonezeke ndi kayendedwe ka dzuwa. Maso a tombolombo n’chinthu chinanso chodabwitsa. Diso lililonse lili ndi mbali 30,000 zomwe zimatha kuona zinthu zosiyanasiyana pa nthawi imodzi. Ngakhale zili choncho, kaubongo kake kamatha kuzindikira zinthu zonsezo ndipo amatha kuona chinthu chilichonse chimene chikuchitika pamalopo.

12, 13. Mukaganizira mmene Yehova analengera selo, kodi n’chiyani chimene chakuchititsani chidwi?

12 Chinthu china chomwe n’chodabwitsa kwambiri ndi mmene Yehova anapangira maselo. Mwachitsanzo, thupi la munthu limapangidwa ndi maselo pafupifupi 100 thiriliyoni. M’kati mwa selo iliyonse mumakhala tinthu tina tosungira malangizo totchedwa DNA. Malangizo amenewa ndi okhudza mmene munthu azikulira ndiponso kuonekera.

13 Kodi mu DNA mumakhala malangizo ochuluka bwanji? Kuti tidziwe kuchuluka kwake, choyamba taganizirani za CD. Mu CD imodzi mukhoza kukhala zinthu zonse zimene zingalembedwe mudikishonale yathunthu. Izi n’zodabwitsa tikaganizira kuchepa kwa CD. Koma mukasipuni kakang’ono kamodzi kokha ka DNA mungakhale zinthu zimene zingakwane m’ma CD okwana 5 thiriliyoni. M’mawu ena tingati DNA yochepa chonchi ingasunge malangizo okwanira kupangira anthu pafupifupi mathiriliyoni awiri ndi hafu.

14. Kodi inuyo mumafunitsitsa kuchita chiyani mukamva zimene asayansi atulukira posachedwapa?

 14 Taonani zimene Davide ananena zokhudza malangizo amene amafunika kuti thupi la munthu lipangike. Pofotokoza za Yehova Mulungu, iye anati: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.” (Sal. 139:16) M’pake kuti Davide anatamanda Yehova ataganizira mmene analengera thupi lake. Zinthu zina zimene asayansi atulukira posachedwapa zokhudza thupi lathu zimatithandizanso kuona kuti Yehova anatilenga modabwitsa. Choncho timafunitsitsa kutamanda Yehova ngati mmene anachitira wamasalimoyu. Iye anati: “Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha. Ntchito zanu ndi zodabwitsa, ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.” (Sal. 139:14) Ndiye timangodabwa anthu ena akamanena kuti kulibe Mulungu amene analenga zinthu zonsezi. Kodi umboni wonsewu sauona?

THANDIZANI ENA KUTI AZILEMEKEZA MULUNGU

15, 16. (a) Kodi mabuku athu athandiza bwanji anthu kumvetsa kuti Yehova analenga zinthu mwanzeru kwambiri? (b) Kodi ndi nkhani iti yamutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” kapena yakuti “Panagona Luso” imene inakusangalatsani kwambiri?

15 Kwa zaka zambiri, magazini ya Galamukani! yathandiza anthu ambiri kuzindikira kuti chilengedwe chimatiphunzitsa zambiri zokhudza Mulungu wathu. Mwachitsanzo, magazini ya September 2006 inali ndi mutu wakuti “Kodi Mlengi Alipo?” Cholinga chake chinali kuthandiza anthu amene asokonezedwa ndi ziphunzitso zimene tatchula kumayambiriro a nkhani ino. Ponena za magazini yapadera imeneyi, mlongo wina analembera ofesi ya nthambi ku United States kuti: “Ntchito yogawira magazini yapaderayi inayenda bwino kwambiri. Mayi wina anapempha kuti timupatse magazini okwana 20. Mayiyu amaphunzitsa Biology ndipo ankafuna kuti akapatse ana a m’kalasi yake.” M’bale wina analemba kuti: “Ndakhala ndikulalikira kuyambira kumapeto kwa m’ma 1940. Panopa ndatsala pang’ono kukwanitsa zaka 75, koma sindinasangalalepo ndi utumiki ngati mmene zinalili pogawira Galamukani! yapaderayi.”

16 Posachedwapa m’magazini a Galamukani! mwakhala mukutuluka nkhani zakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” komanso zakuti “Panagona Luso.” Nkhani zazifupi zimenezi zimapereka umboni wakuti zinthu za m’chilengedwezi zinapangidwa mwanzeru. Komanso zimafotokoza zimene anthu akuchita poyesa kutengera nzeru za Mlengi wathu. Kabuku kachingelezi (Was Life Created?) kamene kanatuluka mu 2010 n’kabwinonso pothandiza ena kuti azitamanda Mulungu. M’kabukuka anaikamo zithunzi zokongola kuti zitithandize kumvetsa kuti Yehova analenga zinthu mwanzeru kwambiri. Mafunso amene ali kumapeto kwa chigawo chilichonse amathandiza munthu kuganizira zimene wawerengazo. Mukhoza kugwiritsa ntchito kabuku kameneka polalikira kwa anthu amene amadziwa bwino Chingelezi.

17, 18. (a) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti aziyankha molimba mtima akafunsidwa zimene amakhulupirira? (b) Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu?

17 Makolo, mungachite bwino kugwiritsa ntchito kabuku kameneka pokambirana ndi banja lanu ngati ana anu akudziwa bwino Chingelezi. Kapena mungagwiritse ntchito nkhani zakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” ndiponso “Panagona Luso.” Kuchita zimenezi kungathandize kuti ana anu azikhulupirira kwambiri Mulungu. Ngati muli ndi ana amene amapita kusekondale, ndiye kuti akhoza kuphunzitsidwa zoti zamoyo zinangokhalako zokha. Akhoza kumva zimenezi kuchokera kwa akatswiri a sayansi, aphunzitsi awo, mabuku, ma TV ndi  mafilimu. Choncho mungathandize anawo kudziwa zoona zake pa nkhaniyi pogwiritsa ntchito kabuku kena kofotokoza mmene moyo unayambira kamene kanatulukanso mu 2010. (The Origin of Life—Five Questions Worth Asking) Mofanana ndi kabuku kamene tatchula mu ndime 16 kaja, kabukuka kamalimbikitsa achinyamata kukhala ‘oganiza bwino.’ (Miy. 2:10, 11) Kangawathandize kuona ngati zimene akuphunzira kusukulu n’zoona kapena ayi.

Makolo thandizani ana anu kuti azitha kuyankha akafunsidwa zimene amakhulupirira (Onani ndime 17)

18 Cholinga cha kabuku kofotokoza mmene moyo unayambira ndi kuthandiza ana asukulu kuti asamangokhulupirira zilizonse zimene akatswiri asayansi amanena zokhudza mmene moyo unayambira. Kamalimbikitsa achinyamata kuti azifufuza okha kuti aone ngati zinthu zakale zimene asayansi amafukula zimatsimikiziradi kuti anthufe tinachokera ku zinyama. Komanso kabukuka kamaphunzitsa anawo mmene angayankhire zimene asayansi amanena zoti zamoyo zinangokhalako zokha. Ngati mutakambirana ndi ana anu nkhani za m’timabuku timeneti mungawathandize kuti aziyankha molimba mtima pamene ena awafunsa chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mlengi.—Werengani 1 Petulo 3:15.

19. Kodi tonsefe tili ndi mwayi wotani?

19 Nkhani zofufuzidwa bwino zimene gulu la Yehova limatipatsa zimatithandiza kumvetsa makhalidwe a Mulungu amene amaonekera m’chilengedwechi. Zimenezi zimatipatsa zifukwa zomveka zotamandira Mulungu wathu. (Sal. 19:1, 2) Tilitu ndi mwayi waukulu wotamanda Yehova, Mlengi wa zinthu zonse, yemwe ndi woyenera kulandira ulemu ndi ulemerero.—1 Tim. 1:17.

^ ndime 3 Kuti mudziwe mmene mungathandizire anthu amene amakhulupirira kuti masiku olenga zinthu anali a maola 24, onani Galamukani! ya September 2006, tsamba 19 komanso kabuku kachingelezi kakuti Was Life Created?, tsamba 24 mpaka 28.