Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

M’pemphero lake lachitsanzo, kodi Yesu anasonyeza kuti chifuniro cha Mulungu chinali kuchitika kumwamba ngakhale kuti angelo oipa anali asanachotsedweko?

Malinga ndi mmene timaŵerengera pa Mateyu 6:10, Yesu anati: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” Pempho limeneli lingamvedwe m’njira ziŵiri izi. Yoyamba, monga pempho kwa Mulungu loti chifuniro chake chichitidwe padziko lapansi monga momwe chinali kuchitidwira kumwamba kapena, yachiŵiri, monga pempho loti chichitidwe mokwanira kumwamba ndi padziko lapansi. * Tanthauzo la mawu oyambirira a Yesu akuti, “ufumu wanu udze,” akusonyeza kuti kamvedwe kachiŵirika ndi kogwirizana kwambiri ndi Malemba. Ndipo kakusonyeza nthaŵi imene Yesu anali padziko lapansi ndiponso nthaŵi yaitali imene inatsatira, iye atachoka. Kodi zimenezi zikugwirizana bwanji?

Buku la Chivumbulutso limanena za zotsatirapo ziŵiri zikuluzikulu za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu kumwamba. Choyamba chimakhudza miyamba ndipo chachiŵiri chimakhudza dziko lapansi. Chivumbulutso 12:7-9, 12 chimati: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”

Kuchotsedwa kwa Satana ndi ziwanda kumwamba pambuyo pa 1914 kunachititsa kuti opanduka auzimu onse asakhalenso kumwambako. Zimenezi zinasangalatsa kwambiri ana aungelo okhulupirika a Yehova, amene amaimira mbali yaikulu ya chiŵerengero cha zinthu zauzimu zimene iye analenga. (Yobu 1:6-12; 2:1-7; Chivumbulutso 12:10) Chotero, mbali yonse yokhudza kumwamba ya pempho la Yesu m’pemphero lake lachitsanzo inakwaniritsidwa. Onse amene anatsala kumwamba anali okhulupirika kwa Yehova ndipo anali ogonjera kotheratu ufumu wake.

Tinganene motsimikiza kuti ngakhale zimenezo zisanachitike, pamene angelo oipa anali adakali ndi mwayi wokhala kumwamba, iwo sanalinso mbali ya banja la Mulungu ndipo anali ataletsedwa kuchita zinthu zina. Mwachitsanzo, Yuda 6 amasonyeza kuti m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino anali ‘atawasunga [kale] m’ndende zosatha pansi pa mdima [wauzimu], kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.’ Mofananamo, 2 Petro 2:4 amati: “Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende [mkhalidwe wa m’malo otsika kotheratu] nawaika ku maenje a mdima [wauzimu], asungike akaweruzidwe.” *

Mosiyana kwambiri ndi khalidwe lawo losayanjidwalo pamene anali adakali kumwamba, angelo oipawo anasonyeza mphamvu yaikulu padziko lapansi. Ndipotu, Mawu a Mulungu amatcha Satana “mkulu [“wolamulira,” NW] wa dziko ili lapansi,” ndipo amatcha ziwanda kukhala “olamulira a dzikoli a mdima uno.” (Yohane 12:31; Aefeso 6:11, 12, NW; 1 Yohane 5:19) Chifukwa cha mphamvu zake, Mdyerekezi anatha kupereka kwa Yesu “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo” mosinthana ndi kum’gwadira. (Mateyu 4:8, 9) Mwachionekere, nthaŵi imene Ufumu wa Mulungu ‘udzabwera’ padziko lapansi, udzasintha kwambiri zinthu.

Kubwera kwa Ufumu wa Mulungu padziko lapansi kudzachititsa zinthu kusinthiratu kukhala zatsopano. Ufumu udzaphwanya maulamuliro onse opangidwa ndi anthu ndipo udzakhala boma lokhalo lolamulira padziko lapansi. Panthaŵi imodzimodziyo, nzika zake zoopa Mulungu zidzakhala “dziko latsopano.” (2 Petro 3:13; Danieli 2:44) Ufumuwu udzathetsanso tchimo pakati pa anthu omvera ndipo m’kupita kwanthaŵi kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Ndipo mwanjira imeneyi udzachotseratu ulamuliro wonse wa Satana.​—Aroma 8:20, 21; Chivumbulutso 19:17-21.

Zaka 1000 zikadzatha, pamene Ufumu wa Umesiya udzakwaniritsa zimene Mulungu akufuna kuti uchite, “Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anam’gonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:28) Ndiyeno padzakhala chiyeso chomaliza ndipo chikadzatha Satana, ziwanda zake ndi anthu ena opanduka osokeretsedwa adzawonongedwa kotheratu mu “imfa yachiŵiri.” (Chivumbulutso 20:7-15) Ndiyeno, zolengedwa zonse zanzeru, kumwamba ndi padziko lapansi mosangalala zidzagonjera ulamuliro wachikondi wa Yehova kosatha. Uku kudzakhala kukwaniritsidwa kwa mbali zonse za mawu a m’pemphero lachitsanzo la Yesu.​—1 Yohane 4:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Baibulo lakuti The Bible​—An American Translation, limamasulira mbali imeneyi ya pemphero lachitsanzo la Yesu kuti, “Ufumu wanu udze! Kufuna kwanu kuchitidwe padziko lapansi ndi kumwamba!”​—Mateyu 6:10.

^ ndime 6 Mtumwi Petro anafananitsa khalidwe losayanjidwa mwauzimu limeneli ndi kukhala mu ‘ndende.’ Komabe, sanatanthauze “phompho” limene ziwanda zidzaponyedwamo kwa zaka chikwi m’tsogolomu.​—1 Petro 3:19, 20; Luka 8:30, 31; Chivumbulutso 20:1-3.