Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi buku la Mika lili ndi machaputala angati, linalembedwa liti, ndipo zinthu zinali bwanji panthaŵi imeneyo?

Buku la Mika lili ndi machaputala asanu ndi aŵiri. Mneneri Mika analemba buku limeneli m’ma 700 B.C.E., panthaŵi imene anthu a Mulungu apangano anali ogaŵikana mitundu iŵiri, Israyeli ndi Yuda.​—8/15, tsamba 9.

Malinga ndi Mika 6:8, kodi Mulungu amafunanji kwa ife?

Tifunika ‘kuchita chilungamo.’ Mmene Mulungu amachitira zinthu ndiwo muyezo wa chilungamo chotero tifunika kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za kuona mtima ndi kukhulupirika. Iye akutiuza kuti ‘tizikonda chifundo.’ Akristu asonyeza kukoma mtima pothandiza ena pa zosoŵa zawo monga pakachitika tsoka. Kuti ‘tiyenda modzichepetsa ndi’ Yehova, tiyenera kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita ndipo tifunika kum’dalira.​—8/15, masamba 20-2.

Ngati Mkristu wachotsedwa ntchito, kodi angafune kuchita chiyani?

Kungakhale kwanzeru kuonanso moyo wake. Zingatheke kukhala ndi moyo wosalira zambiri mwa kusamukira m’nyumba yaing’onopo kapena kuchotsa katundu wina wosafunikira. Zoonadi, tifunika kusiya kuda nkhaŵa ndi zofunika zatsiku ndi tsiku, kudalira Mulungu kuti angatheketse kuti tikhale ndi zofunika. (Mateyu 6:33, 34)​—9/1, masamba 14-15.

Kodi tiyenera kukumbukira chiyani popereka kapena polandira mphatso za ukwati?

Mphatso zodula kwambiri n’zosafunika ndipo sitiyenera kuziyembekezera. Mmene mtima wa munthu wopereka mphatsoyo ulili ndicho chinthu chofunika kwambiri. (Luka 21:1-4) Sibwino kulengeza dzina la munthu wopereka mphatsoyo. Kuchita zimenezi kungakhale kochititsa manyazi. (Mateyu 6:3)​—9/1, tsamba 29.

N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kosaleka?

Kupemphera nthaŵi zonse kungalimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu ndipo kungatikonzekeretse kukumana ndi mayesero aakulu. Mapemphero athu angakhale aafupi kapena aatali, kudalira ndi zimene zikufunika ndiponso mmene zinthu zilili. Pemphero limakulitsa chikhulupiriro chathu ndipo limatithandiza kuthetsa mavuto.​—9/15, masamba 15-18.

Kodi lemba la 1 Akorinto 15:29, limene m’mabaibulo ena analimasulira kuti ‘kubatizidwa chifukwa cha akufa,’ tiyenera kulimva bwanji?

Mtumwi Paulo anatanthauza kuti Akristu odzozedwa amabatizidwa, kapena kumizidwa kuloŵa m’njira ya moyo imene idzawapangitsa kufa chifukwa cha kukhulupirika monga Kristu. Ndiyeno pambuyo pake adzaukitsidwa ku moyo wauzimu monga mmene zinachitikira kwa Kristu.​—10/1, tsamba 29.

Kodi timadziŵa bwanji kuti kukhala Mkristu kumafuna zambiri osati chabe kupeŵa zolakwa zotchulidwa pa 1 Akorinto 6:9-11?

Mtumwi Paulo sananene kuti Mkristu ayenera kupeŵa kokha zolakwa monga dama, kulambira mafano ndi kuledzera. Kusonyeza kuti kusintha kwina kunali kofunika, iye anapitiriza m’vesi lotsatira kuti: “Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula.”​—10/15, masamba 18-19.

Kodi akazi ena a nthaŵi zakale omwe anakondweretsa mtima wa Mulungu ndani?

Amaphatikizapo anamwino aja Sifra ndi Puwa, amene sanamvere Farao ndi kupha ana aamuna achiisrayeli obadwa kumene. (Eksodo 1:15-20) Mkazi wadama wa ku Kanani Rahabi anateteza azondi aŵiri achiisrayeli. (Yoswa 2:1-13; 6:22, 23) Kuchita zinthu mwanzeru kwa Abigayeli kunathandiza kupulumutsa miyoyo ya anthu ndipo kunaletsa Davide kuti asakhale ndi mlandu wakupha. (1 Samueli 25:2-35) Iwo ali zitsanzo kwa akazi masiku ano.​—11/1, masamba 8-11.

Kodi ndi motani mmene ‘nyenyezi zinam’thirira nkhondo yochokera kumwamba’ Sisera monga mmene Oweruza 5:20 amanenera?

Ena amanena kuti zimenezi zimatanthauza thandizo la Mulungu. Ena amaganiza za thandizo la angelo, kugwa kwa miyala kuchokera kumwamba, kapena maulosi amene Sisera ankadalira chifukwa chokhulupirira nyenyezi. Popeza Baibulo silifotokoza, m’pomveka kuwatenga mawuŵa kuti akutanthauza kuti Mulungu anawamenyera nkhondo asilikali a Israyeli mwanjira inayake.​—11/15, tsamba 30.

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri akukhulupirirabe Mulungu pamene chidwi cha anthu ena pankhani ya chipembedzo padziko lonse lapansi chikucheperachepera?

Anthu ena amapita ku tchalitchi kufunafuna mtendere wa m’maganizo. Ena amafuna kudzakhala ndi moyo wosatha akadzamwalira, kapena thanzi labwino, chuma, ndi kuti zinthu ziwayendere bwino pamoyo wawo. M’madera ena, anthu amafuna kupeza zinthu zimene amasoŵa mwauzimu zimene zikuchitika chifukwa cha kusintha kwa ulamuliro kuchoka mu Chikomyunizimu kuloŵa mu ulamuliro umene anthu ali ndi ufulu wokhala ndi zinthu zawozawo. Kudziŵa zifukwa zimenezi kungathandize Mkristu kuyambitsa makambirano ofunika.​—12/1, tsamba 3.