Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Oyera Mtima Enieni Angakuthandizeni Bwanji?

Kodi Anthu Oyera Mtima Enieni Angakuthandizeni Bwanji?

Kodi Anthu Oyera Mtima Enieni Angakuthandizeni Bwanji?

M’MALEMBA, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “woyera mtima” m’mabaibulo ena amawamasulira kuti “wopatulika.” Kodi mawu ameneŵa amanena ndani? “Ponena mochulukitsa, monga akamanena za okhulupirira, mawu achigirikiwo amanena okhulupirira onse, sanena anthu okha oyera mwapadera, kapena amene anamwalira akudziŵika ndi ntchito zabwino kwambiri za oyera mtima.”​—Linatero buku lotchedwa An Expository Dictionary of New Testament Words.

Choncho mtumwi Paulo ananena Akristu oyambirira onse kuti anali oyera mtima enieni, kapena kuti opatulika. Mwachitsanzo, m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, analemba kalata yopita “kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali [m’chigawo cha Roma cha] m’Akaya lonse.” (2 Akorinto 1:1) Kenako, Paulo analemba kalata “kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima.” (Aroma 1:7) Mwachionekere oyera mtima ameneŵa anali asanamwalire, komanso sanawapatule chifukwa cha khalidwe lawo labwino kwambiri limene linali losiyana ndi okhulupirira ena onse. Kodi anali oyera mtima pachifukwa chiti?

Mulungu Ndi Amene Anawayeretsa

Mawu a Mulungu amasonyeza kuti si anthu kapena bungwe, limene limavomereza munthu kukhala woyera mtima. Malemba amati: “[Mulungu] anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo.” (2 Timoteo 1:9) Munthu woyera mtima amayeretsedwa chifukwa chakuti Yehova wamuitana, malinga ndi chisomo cha Mulungu, ndiponso mogwirizana ndi cholinga Chake.

Oyera mtima a mu mpingo wachikristu ali ‘m’pangano latsopano.’ Mwazi umene Yesu Kristu anakhetsa ndi umene unayambitsa pangano limeneli ndipo umayeretsa anthu a m’panganoli. (Ahebri 9:15; 10:29; 13:20, 24) Anthu amene Mulungu amati ndi oyera, ndi ‘ansembe oyera mtima ndipo amapereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu.’​—1 Petro 2:5, 9.

Kupempha kwa Oyera Mtima Ndiponso Kupemphera Kudzera mwa Iwo

Anthu ambirimbiri amalambira “oyera mtima” mwa kugwiritsa ntchito mafano awo kapena amawapempha kuti awapempherere pokhulupirira kuti angapereke mphamvu yapadera kwa okhulupirira. Kodi zimenezi n’zimene Baibulo limaphunzitsa? Yesu pa Ulaliki wa pa Phiri, anaphunzitsa ophunzira ake momwe angafikire kwa Mulungu. Anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Mapemphero ayenera kupita kwa Yehova Mulungu yekha basi.

Akatswiri ena a zaumulungu pofuna kuchirikiza mfundo yopemphera kudzera mwa “oyera mtima,” amatchula Aroma 15:30, pomwe pamati: “Ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi chikondi cha mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m’mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine.” Kodi Paulo anali kulimbikitsa okhulupirirawo kuti azipempha kwa iye kapena kuti azipemphera kwa Mulungu kudzera m’dzina lake? Ayi, si choncho. Ngakhale kuti Baibulo limalimbikitsa kupempherera oyera mtima enieni, kapena kuti opatulika, palibe pamene Mulungu anatilamula kuti tizipemphera kwa iwo kapena kudzera mwa iwo.​—Afilipi 1:1, 3, 4.

Koma, Mulungu anasankha munthu amene tikufunika kudzera mwa iye popemphera. Yesu Kristu anati: “Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.” Yesu ananenanso kuti: “Chilichonse mukafunse m’dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita.” (Yohane 14:6, 13, 14) Tikukhulupirira kuti Yehova amafuna kumva mapemphero amene amaperekedwa m’dzina la Yesu. Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Akhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.”​—Ahebri 7:25.

Ngati Yesu akufunitsitsa kutipempherera, n’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri olambira a m’Matchalitchi Achikristu amapempha mwa “oyera mtima”? M’buku lake lakuti The Age of Faith, wolemba mbiri Will Durant, anafotokoza mmene zimenezi zinayambira. Durant atavomereza kuti Mulungu Wamphamvuyonse anali kuopedwa ndipo Yesu ankaoneka kuti anali wosavuta kwambiri kum’fikira, anati: “Palibe ankafuna kulankhula kwa [Yesu] mwachidunji popeza kuti iwo anali atanyalanyaziratu zimene Iye anaphunzitsa pa Ulaliki wake wa pa Phiri. Zinkaoneka zanzeru kupempha oyera mtima amene anali atavomerezedwa kuti ndi oyera mtima komanso amene ankawakhulupirira kuti ali kumwamba, kuti awapempherere kwa Kristu.” Kodi zifukwa zimenezi n’zomveka?

Baibulo limatiphunzitsa kuti kudzera mwa Yesu, tikhoza kupempha Mulungu ndi “ufulu wa kulankhula ndi chidaliro.” (Aefeso 3:11, 12, NW) Mulungu Wamphamvuyonse sali patali ndi ife koti sangamve mapemphero athu. Wamasalmo Davide anapemphera mwachikhulupiriro kuti: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.” (Salmo 65:2) M’malo mopereka mphamvu kudzera m’mafano a “oyera mtima” amene anamwalira, Yehova amapereka mzimu wake woyera kwa amene amaupempha mwachikhulupiriro. Yesu anati: “Ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?”​—Luka 11:13.

Ntchito ya Oyera Mtima

Oyera mtima amene Paulo anawalembera kalata anamwalira zaka zambiri zapitazo ndipo m’kupita kwa nthaŵi anayenera kulandira “korona wa moyo,” kuwaukitsira kumwamba. (Chivumbulutso 2:10) Olambira Yehova Mulungu amadziŵa kuti kulemekeza anthu oyera mtima enieni ameneŵa si kwa m’Malemba ndipo sikungawateteze ku matenda, masoka achilengedwe, mavuto a zachuma, ukalamba, kapena imfa. Ndiyeno, mungafunse kuti, ‘Kodi oyera mtima a Mulungu amatisamaliradi? Kodi tiziyembekezera kuti angatichitire kanthu?’

Oyera mtima anatchulidwa kwambiri mu ulosi umene Danieli analemba. M’zaka za m’ma 500 B.C.E., iye anaona masomphenya ochititsa chidwi, omwe kukwaniritsidwa kwake kukuchitika ngakhale masiku athu ano. M’nyanja munatuluka nyama zinayi zoopsa zimene zimaimira maboma a anthu, amene akulephera kukwaniritsa zofunika zenizeni za anthu. Ndiyeno Danieli analosera kuti: “Opatulika a Wam’mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nawo ufumu kosatha, ku nthaŵi zomka muyaya.”​—Danieli 7:17, 18.

Paulo anatsimikizira ‘choloŵa cha oyera mtima’ chimenechi, chakuti adzalamulira pamodzi ndi Kristu kumwamba. (Aefeso 1:18-21) Mwazi wa Yesu unatsegula njira yakuti anthu oyera mtima 144,000 akaukitsidwire ku ulemerero wakumwamba. Mtumwi Yohane anati: “Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiŵiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.” (Chivumbulutso 20:4, 6; 14:1, 3) Yohane m’masomphenya anamva khamu la zolengedwa zakumwamba likuimba pamaso pa Yesu waulemereroyo, kuti: “Ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.” (Chivumbulutso 5:9, 10) N’zolimbikitsa bwanji! Yehova Mulungu wasankha yekha bwinobwino amuna ndi akazi ameneŵa. Ndiponso, atumikira mokhulupirika padziko lapansi, akumanadi ndi mavuto onse amene anthu amakumana nawo. (1 Akorinto 10:13) Choncho tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti opatulika, kapena kuti oyera mtima oukitsidwa ameneŵa, adzakhala mafumu achifundo ndi omvetsa, azidzakumbukira zofooka zathu ndi kupereŵera kwathu.

Madalitso a Ufumu wa Mulungu

Posachedwapa boma la Ufumu lichitapo kanthu kuti lichotse kuipa ndi kuvutika konse padziko lapansi. Panthaŵi imeneyo anthu adzayandikana kwambiri ndi Mulungu kuposa kale lonse. Yohane analemba kuti: “Ndipo ndinamva mawu akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo.” Izi zidzabweretsa madalitso osaneneka kwa anthu pakuti ulosiwo ukupitiriza kuti: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Idzakhala nthaŵi yosangalatsatu kwambiri! Zimene ulamuliro wangwiro wa Kristu Yesu ndi anthu oyera mtima 144,000 udzachite akupitiriza kuzifotokoza m’mawu awa olembedwa pa Mika 4:3, 4, akuti: “[Yehova] adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”

Oyera mtima ndi amene akuitana anthu kuti akalandire nawo madalitso ameneŵa. Oyera mtima enieni amene akuimiridwa ndi mkwatibwi, akupitiriza kunena kuti: “Idzani.” Lembali likupitiriza kuti: “Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Kodi n’chiyaninso chili ‘m’madzi a moyo’? Mwa zina, ndicho kudziŵa zolondola zokhudza zimene Mulungu amafuna. Yesu popemphera kwa Mulungu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Munthu angadziŵe zimenezi mwa kuphunzira Baibulo mokhazikika. Tili osangalala kwambiri kuti kudzera m’Mawu a Mulungu tingaŵadziŵe bwinobwino oyera mtima ndipo tingaphunzire momwe adzawagwiritsire ntchito kuti mtundu wa anthu upindule kwa muyaya.

[Chithunzi patsamba 4]

Paulo analemba makalata ouziridwa kwa oyera mtima enieni

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Atumwi okhulupirika a Yesu anali oyera mtima enieni, kapena kuti opatulika

[Chithunzi patsamba 6]

Tingapemphere ndi mtima wonse kwa Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu

[Chithunzi patsamba 7]

Oyera mtima, kapena kuti opatulika amene adzaukitsidwe adzakhala mafumu achifundo pa dziko lapansi