Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zomwe Muyenera Kudziŵa Pankhani za Ufiti

Zomwe Muyenera Kudziŵa Pankhani za Ufiti

Zomwe Muyenera Kudziŵa Pankhani za Ufiti

UFITI wamakono n’ngwovuta kuulongosola. Izi zili choncho chifukwa chakuti awo amene amauchita amachita zinthu zosiyana kotheratu. Iwo sakutsogozedwa ndi ulamuliro waukulu umodzi kapena chiphunzitso kapena buku loyera kuti agwirizanitse chikhulupiriro chawo. N’ngosiyananso miyambo, kugwirizana kwawo, zizoloŵezi, komanso malingaliro akuti kodi ndi milungu yotani imene angamaipatse ulemu. Wolemba nkhani wina anathirira ndemanga kuti: “Nkhani ya matsenga imapatsa munthu malingaliro ‘ambirimbiri osatsatirika bwino.’” Winanso anati: “Achikunja Amakono ambiri sagwirizana pafupifupi pa chilichonse.”

Kwa ambiri, kutsutsanako sivuto ayi. Buku lina lamalangizo la ofuna kukhala mfiti limati: “Ngati nkhani inayake yooneka monga yosemphana yakuthetsani nzeru, pendani nkhani imeneyi ndipo sankhani chomwe mungafune kutsatira. Mverani mphamvu yanu yodziŵiratu zinthu pasadakhale. M’mawu ena, khalani womasuka kusankha pa miyambo yofalitsidwa ndi mabuku a miyambo kuti musankhe chomwe chikuoneka kuti n’chabwino.”

Kwa awo amene amazindikira mmene choonadi chimakhalira, kusemphana koteroko kumakhala vuto. Choonadi ndi chinthu chenicheni, chomwe chimachitikadi. Zinthu sizingakhale zoona kokha chifukwa chakuti munthu akulingalira kapena akufunitsitsa kapena akukhulupirira kuti n’zoona. Mwachitsanzo, nthaŵi inayake madokotala ankakhulupirira kuti angachize chibayo mwa kudula nkhuku yamoyo m’zigawo ziŵiri ndi kuika zigawo ziŵirizo pachifuwa cha wodwalayo. Mosakayikira, odwala ambiri ankakhulupirira moona mtima kuti njira imeneyi ingaŵachizedi. Komabe, zikhulupiriro ndi ziyembekezo zawozo sizinali zogwirizana ndi zenizeni zake zakuti mchitidwe umenewu suchiza chibayo. Anthu sapeka choonadi; iwo amakalamira kuti achimvetse.

Baibulo limanena kuti lili ndi zoona zake za nkhani zauzimu. Yesu Kristu, pamene anali padziko lapansi, anati kwa Atate wake m’pemphero: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) Ambiri omwe amachita ufiti savomereza mfundo imodzi. Mmalo mwake, amafunafuna kuuziridwa ndi kutsogozedwa pokhulupirira nthano, zipembedzo zakalekale, ndiponso ngakhale nkhani zongoyerekezera za sayansi. Chotero, kodi sikuli kwanzeru kuyesa kulingalira zomwe Baibulo limanena? Ndiiko komwe, n’lodziŵika pafupifupi dziko lonse lapansi monga buku lopatulika. Ilo lilinso limodzi mwa mabuku akale zedi achipembedzo omwe akhalako mpaka lero. Baibulo linalembedwa pa nyengo ya zaka zoposa 1,600, komabe ziphunzitso zake sizisintha. Tatiyeni tiyerekezere ziphunzitso za Baibulo ndi zikhulupiriro zina zofala zomwe awo amene amachirikiza ufiti amalongosola masiku ano.

Ndani Amene Amakhala Kumalo Amizimu?

Funso lofunika kwambiri m’kufunafuna kumvetsetsa zinthu zauzimu ndi ili lakuti, Ndani omwe amakhala kumalo amizimu? Pamene kuli kwakuti mfiti zambiri zamakono zimatsatira chikhulupiriro cholambira zinthu zachilengedwe cha milungu yambirimbiri, ena amalambira mulungu wamkazi wamkulu, yemwe amaonetsedwa m’misinkhu itatu yomwe ili namwali, mayi, ndi nkhalamba yaikazi yamaonekedwe oopsa, kuimira zigawo zikuluzikulu m’moyo. Chibwenzi chake ndicho mulungu wokhala ndi nyanga. Mfiti zina zimalambira mulungu wamwamuna komanso mulungu wamkazi panthaŵi imodzi. Wolemba wina anati: “Mulungu wamkazi komanso Mulungu wamwamuna amaonedwa ngati kusonyezedwa kwa mphamvu zachikazi ndi zachimuna za chilengedwe. Aliyense [ali] ndi mikhalidwe yapadera yomwe pamene igwirizanitsidwa imapanga chilengedwe chogwirizana cha moyo.” Winanso analemba kuti: “Chimodzi mwa zosankha zovuta kwambiri mu Ufiti ndicho milungu yomwe mungakonde (Milungu Yaimuna/​Milungu Yaikazi) imene muzigwira nayo ntchito. . . . Ufiti umakupatsani ufulu wosankha ndiyeno pambuyo pake kumalemekeza mitundu yanuyanu ya Milungu.”

Baibulo silichirikiza alionse mwa malingaliro ameneŵa. Yesu Kristu anapatulira utumiki wake wonse ku kuphunzitsa ena za Yehova, “Mulungu woona yekha.” (Yohane 17:3) Baibulo limati: “Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano.”​—1 Mbiri 16:25, 26.

Bwanji nanga ponena za Mdyerekezi? Buku lomasulira mawu lotchedwa Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary linamasulira ufiti monga “mgwirizano ndi mdyerekezi.” Kungakhale kovuta zedi lerolino kupeza mfiti yomwe ingavomereze tanthauzoli, popeza kuti mfiti zambiri sizimavomereza n’komwe kuti Satana Mdyerekezi aliko. Msungwana wina wotchulidwa m’nyuzipepala ya The Irish Times kukhala “mfiti yolemekezeka komanso mtsogoleri wa limodzi mwa magulu a mfiti odziŵika kwambiri mu Ireland,” anati: “Kukhulupirira kuti kuli Mdyerekezi kumaphatikizapo kuvomereza Chikristu . . . [Mdyerekezi] sangakhale m’chilengedwe momwe mulibe Mulungu.”

Baibulo limatsimikizira kuti Mdyerekezi alipo ndipo limanenetsa kuti n’njemwe wadzetsa mavuto ochuluka ndi chipwirikiti padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:12) Yesu sanangophunzitsa kuti Mdyerekezi alipo koma anasonyezanso kuti n’kotheka kuchita zofuna za Mdyerekeziyo tisakudziŵa. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo odzilungamitsa a m’zaka za zana loyamba anadzikweza akumati, anali ana a Mulungu ndipo ankakhulupirira kuti iwo anali kuchita chifuniro cha Mulungu. Yesu, yemwe anali wokhoza kudziŵa zomwe zili m’mitima yawo, anadziŵa zosiyana ndi zimenezo. Anawauza mwachindunji kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.” (Yohane 8:44) Komanso, buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limanena kuti Mdyerekezi ndiye “wonyenga wa dziko lonse.”​—Chivumbulutso 12:9.

Kodi Matsenga Ena N’ngabwino?

Ndithudi, anthu nthaŵi zonse amagwirizanitsa matsenga ndi zamizimu. * Anthu ambiri m’nthaŵi zonse ziŵiri zakale ndi zamakono zomwe amakhulupirira kuti matsenga ochitidwa ndi mfiti amachitidwa pofuna kungovulaza ena. Amati mfiti zili ndi mphamvu zodzetsa ululu waukulu ngakhale imfa imene mwa matsenga. Malinga ndi mwambo, mfiti zakhala zikuimbidwa mlandu chifukwa cha masoka otsatanatsatana osalekeza, kuphatikizapo matenda, imfa, ndi kulephera kwa mbewu.

Mfiti lerolino zimatsutsa mwamphamvu nkhani zoterozo. Povomereza kuti nthaŵi ndi nthaŵi pamakhala mfiti ina yaupandu yomwe imachita zoipa, ambiri amaumirirabe kunena kuti koma iwo matsenga awo amagwiritsidwa ntchito mopindulitsa osati kuvulaza. Athakati amaphunzitsa kuti zochitika za matsenga zimabweretsera munthu amene akuchita matsengayo mapindu oŵirikiza katatu ndipo amati chimenechi n’chododometsa chachikulu cha kulodza. Zitsanzo za matsenga ameneŵa otchedwa opindulitsa zikuphatikizapo matsenga odzitetezera, kuyeretsa panyumba panu kuchotsa mphamvu zovulaza zomwe wina amene poyamba amakhala pamalopo anazisiya, kupangira munthu mankhwala kuti akukonde, kuchirikiza machiritso ndi thanzi, kudziteteza kuti asakuchotseni ntchito, ndi kupeza ndalama mwachitaka. Ndi mphamvu zochuluka zotere zomwe akuti zimakhala ndi mfitizi, n’zosadabwitsa kuti ufiti wafala kwambiri chomwechi.

Komabe, Baibulo silimasiyanitsa pakati pa matsenga omwe ali abwino ndi matsenga omwe ali oipa. Mu Chilamulo choperekedwa kwa Mose, Mulungu ananenetsa momveka bwino. Iye anati: “Musamachita nyanga.” (Levitiko 19:26) Timaŵerenganso kuti: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.”​—Deuteronomo 18:10, 11.

N’chifukwa chiyani Mulungu ananena zimenezi? Si chifukwa chakuti anagofuna kutikaniza zinthu zabwino ayi. Yehova anapereka malamulo ameneŵa kwa anthu ake chifukwa chakuti ankaŵakonda ndipo sanafune kuti iwo akhale akapolo a mantha ndi miyambo. M’malo mwake, akuitana atumiki ake kuti adze kwa iye kuti apeze zomwe angafune. Iye ali Wopatsa wa “mphatso ili yonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Mtumwi Yohane anatsimikizira okhulupirira anzake kuti: “Chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa [Mulungu] chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zom’kondweretsa pamaso pake.”​—1 Yohane 3:22.

Bwanji Nanga za Mizimu Yoipa?

Mfiti zambiri zimagwirizana ndi Baibulo pamfundo iyi: Mizimu yoipa ilipodi. M’nkhani ina, winawake wochirikiza ufiti akuchenjeza kuti: “Zipukwani zilipodi kunjaku: Zimakhala m’dziko losaoneka lofanana ndi lathu lino, lomwe n’lodzala ndi zolengedwa zamoyo zokhazokha. . . . Mawu akuti ‘Ndondocha’, ‘Mizimu Yoipa’ ndi ‘Chiŵanda’ n’ngolondoladi. Mizimuyo n’njamphamvu kwambiri. . . . Mtundu wanzeru kwambiri . . . ungakhoze (ngati winawake ali waufulu kwambiri kuitsegulira pakhomo) kuloŵa m’dziko lathu lino. . . . Ingaloŵe m’thupi lanu . . . , ngakhalenso kusonyeza ulamuliro wawo pa inu. Inde, zimenezi n’zofanana ndendende ndi nkhani zakale za kugwidwa ndi Chiŵanda.”

M’nthaŵi za Baibulo, kugwidwa ndi chiŵanda kunazunza anthu m’njira zosiyanasiyana. Ena mwa omwe ankazunzikawo sanali okhoza kulankhula, ena anali akhungu, ena ankangochita zozerezeka, ndipo enanso ankakhala ndi nyonga zoposa zamunthu. (Mateyu 9:32; 12:22; 17:15, 18; Marko 5:2-5; Luka 8:29; 9:42; 11:14; Machitidwe 19:16) Nthaŵi zina vuto linkakula kwambiri pamene ziŵanda zambirimbiri ziloŵa mwa munthu nthaŵi imodzi. (Luka 8:2, 30) Ndithudi, pali chifukwa chabwino chomwe Yehova akuchenjezera anthu kuti apeŵe ufiti ndi zochitika zina za matsenga.

Chipembedzo Chozikika pa Choonadi

Ambiri akuphunzira ufiti lerolino chifukwa chakuti ukuoneka ngati chipembedzo chosavulaza, chosaopsa, ndi cha chilengedwe. M’midzi ina wavomerezedwa. Sukuwopedwanso. M’malo mwake, kaŵirikaŵiri umaonedwa ngati chinthu wamba. M’madera ena komwe ufulu wa kupembedza umachititsa ambiri kuloŵerera m’zinthu zachilendo, ufiti walemekezedwa kwambiri.

Indedi, dziko la zipembedzo langokhala malo a anthu onse kumene anthu amakhala omasuka kusankha china chilichonse chimene angakonde, monga momwe munthu angagulire nsapato. Molekana ndi zimenezo, Yesu analankhulapo za zosankha ziŵiri zokha. Iye anati: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Mwachibadwa, tili ndi ufulu wosankha njira imene tingafune kuyendamo. Koma popeza kuti ubwino wathu wosatha uli pangozi, kusankha kumeneko n’kofunika kwambiri. Kuti tipeze kuunika kwauzimu, tiyenera kupeza njira ya choonadi, njira yomwe imapezeka m’Mawu a Mulungu okha, Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Liwulo “matsenga” limagwiritsidwanso ntchito pofuna kutchula matsenga achiphamaso ochitidwa pabwalo lochitira seŵero amene ali olekanitsidwa ndi mitundu ya zamizimu. Onani Galamukani!, ya September 8, 1993, tsamba 12, “Kodi Kuchita Matsenga Kuli ndi Upandu?”

[Chithunzi patsamba 5]

Ambiri lerolino amaona ufiti monga chipembedzo cha chilengedwe chosavulaza

[Chithunzi patsamba 6]

Matsenga nthaŵi zonse agwirizanitsidwa ndi zamizimu

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi ochita za ufiti akuchita chifuno cha Mdyerekezi mosadziŵa?

[Zithunzi patsamba 7]

Baibulo likuvumbula njira ya choonadi