Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mumadziŵa Zambiri Ponena za Baibulo”

“Mumadziŵa Zambiri Ponena za Baibulo”

Olengeza Ufumu Akusimba

“Mumadziŵa Zambiri Ponena za Baibulo”

PAMENE Yesu wa zaka 12 zakubadwa anayankhula molimba mtima kwa atsogoleri a chipembedzo ku Yerusalemu, “onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziŵitso chake, ndi mayankho ake.” (Luka 2:47) Mofananamo lerolino, atumiki ambiri achinyamata a Yehova amalimba mtima kuti ayankhule ndi aphunzitsi awo ndiponso anzawo a kusukulu ponena za Mulungu ndi Baibulo, ndipo kaŵirikaŵiri amakhala ndi zotsatira zosangalatsa.

Tiffany, msungwana wa zaka 14 zakubadwa, anali m’kalasi momwe nkhani ina inakhudza ulosi wa Baibulo wa masabata 70 a zaka, wopezeka pa Danieli 9:24-27. Mphunzitsi anagogomezapo mwachidule pa mavesi ameneŵa ndipo mwamsanga anasiya nkhaniyo.

Poyamba, Tiffany amachita mantha kuti akweze dzanja. “Koma pa zifukwa zina,” iye akutero, “zinandivutitsa maganizo kwambiri kuti mavesiwo sanafotokozedwe mokwanira. Mwadzidzidzi, ndinakweza dzanja.” Mphunzitsiyo anadabwa kuona kuti winawake ali ndi zoti anenepo pa phunzirolo, chifukwa chakuti ambiri mwa ophunzira anali ndi vuto lakuti alimvetse bwino.

Atapatsidwa mwayi woti afotokozere ulosiwo, Tiffany anaimirira ndi kuyankhula mosaonera m’buku. Atatha kuyankhula, m’kalasimo munali zii! Tiffany anachita mantha pang’ono. Kenako kalasiyo inayamba kuomba m’manja kwambiri.

“N’zochititsa chidwi kwambiri zimenezi, Tiffany, n’zochititsa chidwi kwabasi,” anatero mphunzitsiyo mobwerezabwereza. Iye ananena kuti ankadziŵa kuti mavesi amenewo ayenera kukhala ndi mfundo zinanso zambiri, koma Tiffany anali woyamba kum’fotokozera momveka bwino kwambiri. Pamene amaŵeruka, mphunzitsiyo anafunsa Tiffany momwe anadziŵira zambiri chotero ponena za Baibulo.

“N’chifukwa chakuti ndine mmodzi wa Mboni za Yehova,” anayankha motero. “Makolo anga anandifotokozera ulosi umene uja maulendo angapo ndisanaumvetsetse.”

Nawonso anzake a m’kalasi anali odabwa ndi chidziŵitso chake cha Baibulo. Wophunzira wina anati kwa Tiffany: “Tsopano ndadziŵa chifukwa chake inu a Mboni za Yehova mumapita ku khomo ndi khomo; n’chifukwa chakuti mumadziŵa zambiri ponena za Baibulo.” Ena analonjeza kuti sadzamusekanso chifukwa cha zikhulupiriro zake.

Tiffany atauza makolo ake zimenezi, makolowo anam’pempha ngati iye angakagaŵire buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha kwa mphunzitsi wakeyo. Atatero ndi kusonyeza mphunzitsiyo kachigawo kamene kamafotokoza za ulosi wa Danieli, iye analandira bukulo ndi mtima wonse ndi kum’thokoza.

Ndithudi, pamene achinyamata achikristu ayankhula molimba mtima za zinthu zimene makolo awo anawaphunzitsa ponena za Mulungu ndiponso Baibulo, amadzetsa chitamando ndi ulemu kwa Yehova ndiponso madalitso kwa iwo eni.​—Mateyu 21:15, 16.