Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kusunga Nthawi

Kusunga Nthawi

Anthu ambiri amene amachedwa kawirikawiri, nawonso amavomereza kuti kusunga nthawi n’kofunika. Baibulo lili ndi malangizo othandiza kwambiri pa nkhaniyi.

Kodi kusunga nthawi n’kofunika bwanji?

KUFUNIKA KWAKE

Anthu ena amaona kuti kufika mwamsanga kuntchito kapena kumalo enaake kumawathandiza kuti asakhale ndi nkhawa kwambiri. Kusunga nthawi kumathandizanso kuti munthu akhale ndi mbiri yabwino. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kumasonyeza kuti ndinu wadongosolo. Mukamasunga nthawi mumasonyeza kuti mumayendetsa bwino zinthu pa moyo wanu moti simulola kuti zinthu zina zikusokonezeni pa zimene mukufuna kuchita.

Kumasonyeza kuti ndinu wodalirika. M’dzikoli anthu ambiri sakwaniritsa zimene alonjeza. Choncho anthu amayamikira kwambiri anthu omwe amachita zimene amanena. Anthu odalirika amalemekezedwa ndi anzawo komanso achibale awo. Mabwana amasangalalanso ndi anthu omwe amafika kuntchito pa nthawi yake komanso amamaliza ntchito zawo pa nthawi yabwino. Anthu oterewa akhoza kukwezedwa pa ntchito komanso kulandira malipiro okwera.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

M’Baibulo muli malemba othandiza pa nkhani ya kusunga nthawi. Mwachitsanzo, limanena kuti: “Zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akorinto 14:40) Anthu akapangana kuti akumane pa nthawi inayake, ndi bwino kuti aliyense afike pa nthawi imene agwirizanayo. Baibulo limanenanso kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake.” (Mlaliki 3:1) Ndipo vesi lotsatira limanena kuti pali “nthawi yobzala ndi nthawi yozula.” (Mlaliki 3:2) Alimi amabzala mbewu pa nthawi yoyenera n’cholinga choti adzapeze zokolola zambiri. Choncho tinganene kuti alimi akamasunga nthawi, zinthu zimawayendera bwino.

Baibulo limatchulanso chifukwa china chofunika chosungira nthawi. Chifukwa chake n’choti timasonyeza kuti timalemekeza ena komanso nthawi yawo. (Afilipi 2:3, 4) Koma anthu amene amakonda kuchedwa zimakhala ngati akuba nthawi ya anthu ena.

“Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”Afilipi 2:4.

Kodi mungatani kuti muzisunga nthawi?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikonzekera pasadakhale. (Miyambo 21:5) Ngati mumakonda kuchedwa, n’kutheka kuti mumachita zambiri kuposa zimene mungakwanitse. Ngati zili choncho, mungachite bwino kusiya kuchita zinthu zomwe n’zosafunika. Mungachitenso bwino kugawa nthawi yokwanira yoti muchitire zinazake komanso kuyesetsa kuti mukafike mofulumira kumene mukupita. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mufike pa nthawi yake ngakhale mutakumana ndi mavuto enaake panjira.

Baibulo limatilimbikitsanso kukhala odzichepetsa. (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa amadziwa zimene sangakwanitse. Choncho musanavomere kuchita zinazake, ndi bwino kuona kaye ngati mulidi ndi nthawi yokwanira yochitira zinthuzo. Mukamangovomera kuchita zinthu zambirimbiri, mumakhala wopanikizika ndiponso anthu ena amakhumudwa mukalephera kuchita zimene munavomerazo.

Baibulo limatiuzanso kuti tiyenera kumagwiritsa ntchito bwino nthawi yathu ndipo tiyenera kumaika zinthu zofunika pa malo oyamba. (Aefeso 5:15, 16; Afilipi 1:10) Mwachitsanzo, ngati mwakwera basi kapena mukudikira munthu wina, mukhoza kumawerenga kapena kukonzekereratu zinthu zina zomwe mukufuna kuchita pa tsikulo.

“Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”Miyambo 21:5.