Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?

 N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Nthawi?

KUSUNGA nthawi kapena kuchita zinthu pa nthawi yake, n’kovuta. Zinthu zina zimene zimachititsa kuti tisasunge nthawi ndi kuyenda mitunda italiitali, kuchuluka kwa magalimoto pamsewu ndiponso kupanikizika ndi zochita. Komabe, kusunga nthawi n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, anthu amaona kuti munthu amene amasunga nthawi kuntchito ndi wodalirika ndiponso wakhama. Koma munthu amene amachedwa kuntchito amasokoneza anzake ndiponso amasokoneza ntchito yonse. Mwana wasukulu akachedwa, saphunzira nawo zinthu zina ndipo izi zingachititse kuti asadzakhoze mayeso. Munthu akapita kuchipatala mochedwa, salandira thandizo loyenerera.

M’madera ena anthu saona kuti kusunga nthawi n’kofunika. M’madera oterewa, anthu amakhala ndi chizolowezi chochedwa. Ngati kudera lanu kuli chizolowezi chimenechi muyenera kuyesetsa kuti muzichita zinthu pa nthawi yake. Kumvetsa ubwino wosunga nthawi kungatithandize kuti tizichita zinthu pa nthawi yake. Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kusunga nthawi? Kodi tingatani kuti tizisunga nthawi? Nanga tingapindule bwanji chifukwa chosunga nthawi?

Yehova Ndi Mulungu Wosunga Nthawi

Chifukwa chachikulu chimene tiyenera kusungira nthawi ndi chakuti timafuna kutsanzira Mulungu amene timalambira. (Aef. 5:1) Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye sachedwa. Amachita zinthu ndiponso kukwaniritsa zolinga zake pa nthawi  yake. Mwachitsanzo, pamene Yehova ankafuna kuwononga anthu oipa ndi chigumula, anauza Nowa kuti: “Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale.” Kutatsala nthawi yochepa kuti iye awononge anthuwo, Yehova anauza Nowa kuti alowe m’chingalawacho ndipo anamuuza kuti: “Akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziwononga pa dziko lapansi.” Ndiyeno pa nthawi yake, ‘patapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi.’ (Gen. 6:14; 7:4, 10) Kodi chikanachitikira Nowa ndi banja lake n’chiyani akanachedwa kulowa m’chingalawa? Mofanana ndi Mulungu amene ankalambira, iwo anafunika kusunga nthawi.

Patapita zaka 450, kuchokera pamene chigumula chinachitika, Yehova anauza Abulahamu kuti adzakhala ndi mwana ndipo Mbewu yolonjezedwa idzafika kudzera mwa mwanayo. (Gen. 17:15-17) Mulungu anati Isake adzabadwa “nthawi yomwe ino chaka chamawa.” Kodi zimenezi zinachitikadi? Malemba amati: “Ndipo Sara anatenga pakati, nam’balira Abrahamu muukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi  yomweyo Mulungu anamuuza iye.”​—Gen. 17:21; 21:2.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza kuti Mulungu amasunga nthawi. (Yer. 25:11-13; Dan. 4:20-25; 9:25) Baibulo limatilimbikitsa kudikira tsiku la chiweruzo la Yehova limene likubwera. Ngakhale tsikuli litaoneka ngati ‘likuchedwa’ tidziwe kuti ‘lifika ndithu, osazengereza.’​—Hab. 2:3.

Kusunga Nthawi N’kofunika pa Kulambira Kwathu

Amuna onse a Isiraeli anafunika kufika pa nthawi yake pamalo a msonkhano wokumbukira “nyengo zoikika za Yehova.” (Lev. 23:2, 4) Mulungu anatchulanso nthawi yoperekera nsembe zosiyanasiyana. (Eks. 29:38, 39; Lev. 23:37, 38) Izitu zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azisunga nthawi pa kulambira.

M’nthawi ya atumwi, Paulo analangiza Akorinto za mmene misonkhano iyenera kuchitikira. Iye anawalimbikitsa kuti: “Zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.” (1 Akor. 14:40) Choncho, misonkhano yachikhristu inayenera kuyamba pa nthawi yake. Pa nkhani ya kusunga nthawi, Yehova sanasinthe. (Mal. 3:6) Kodi tingatani kuti tizifika pa nthawi yake pa misonkhano yachikhristu?

Zimene Mungachite Kuti Muzisunga Nthawi

Ena aona kuti kukonzekera pasadakhale n’kothandiza kwambiri. (Miy. 21:5) Mwachitsanzo, ngati mukupita kwinakwake ndipo mukufuna kuti mugwire nthawi, kodi ndi nzeru kunyamuka pa nthawi yoti mungokafika pa nthawi yeniyeniyo? Kodi sizingakhale bwino kunyamuka kutatsala nthawi ndithu n’cholinga choti musachedwe ngakhale mutakumana ndi ‘zakugwa’ mwadzidzidzi m’njira? (Mlal. 9:11) Mnyamata wina amene amasunga nthawi kwambiri dzina lake José * anati: “Chinthu china chimene chingathandize kuti munthu afike pa nthawi yake, ndi kudziwa nthawi imene angatenge popita kumaloko.”

Anthu ena amakonza zoti aziweruka msanga kuntchito n’cholinga choti azifika ku misonkhano pa nthawi yake. Izi ndi zimene m’bale wina anachita ku Ethiopia. Iye anaona kuti nthawi imene mnzake amabwera kudzasinthana naye pa ntchito ikanachititsa kuti azichedwa ku misonkhano ndi maminitsi 45. Choncho anakonza zoti pa tsiku la misonkhano, mnzakeyo azifika mofulumira kuti iye aziweruka msanga. Ndiye anagwirizana ndi mnzakeyo kuti azimugwirira ntchito maola 7 owonjezera.

Kufika msanga pa misonkhano kumakhala kovuta kwambiri ngati muli ndi ana. Nthawi zambiri, mayi ndi amene amakhala ndi udindo wokonzekeretsa ana koma anthu ena ayenera kuthandiza. Mayi wina ku Mexico, dzina lake Esperanza, amasamalira yekha ana 8. Tsopano anawa, ali ndi zaka za pakati pa 5 ndi 23. Esperanza anafotokoza zimene zimathandiza banja lake kuti lizisunga nthawi. Iye anati: “Ana akuluakulu amakonzekeretsa ana ang’onoang’ono. Izi zimandithandiza kuti ndimalize ntchito zapakhomo, kukonzekera ndiponso kunyamuka nthawi yomwe tinagwirizana.” Banjali linagwirizana nthawi yeniyeni yonyamukira ndipo aliyense amachita mbali yake kuti azinyamuka pa nthawiyo.

Ubwino Wofika Mofulumira pa Misonkhano Yathu

Kuganizira madalitso amene timapeza chifukwa chofika msanga pa misonkhano yachikhristu kungatilimbikitse kuchita zonse zimene tingathe kuti tizifika msanga pa misonkhano nthawi zonse. Mtsikana wina dzina lake Sandra yemwe ali ndi chizolowezi chofika msanga pa misonkhano anati: “Kufika msanga pa misonkhano kumandisangalatsa chifukwa chakuti ndimakhala ndi nthawi yopatsa moni abale ndi alongo, kucheza nawo ndiponso kuwadziwa bwino.” Tikafika msanga pa Nyumba ya Ufumu timakhala ndi mwayi womva mmene abale athu amene afika pa misonkhanopo akupiririra ndiponso zimene akuchita potumikira Mulungu mokhulupirika. Tikamafika msanga pa misonkhano ndiponso kucheza ndi abale ndi  alongo athu zimathandiza kwambiri chifukwa ‘timawalimbikitsa pa chikondi ndi ntchito zabwino.’​—Aheb. 10:24, 25.

Pa misonkhano yathu yachikhristu, nyimbo yoyamba ndi pemphero loyamba n’zofunika kwambiri pa kulambira kwathu. (Sal. 149:1) Nyimbo zathu zimatamanda Yehova, zimatikumbutsa makhalidwe ake amene tiyenera kukhala nawo, ndipo zimatilimbikitsa kuti tizilalikira mosangalala. Nalonso pemphero loyamba ndi lofunika kwambiri. Kale, Yehova anatcha kachisi kuti “nyumba yopemphereramo.” (Yes. 56:7) Masiku ano timasonkhana pamodzi kuti tipemphere kwa Mulungu. M’pemphero loyamba timapempha Yehova kuti atitsogolere, kutipatsa mzimu woyera ndiponso kuti atsegule maganizo ndi mitima yathu n’cholinga chakuti timvetse mfundo zimene tiphunzire. Choncho, tizifika mofulumira pa misonkhano yathu kuti tiimbe nawo nyimbo yoyamba ndiponso tikhalepo pa nthawi ya pemphero loyamba.

Mlongo wina wa zaka 23 dzina lake Helen anafotokoza chifukwa chimene amafikira pa misonkhano mofulumira. Iye anati: “Ndimaona kuti imeneyi ndi njira imene ndingamusonyezere Yehova kuti ndimamukonda chifukwa chakuti iye ndi amene amapereka malangizo amene timalandira kuphatikizapo akuti tiziyamba ndi nyimbo ndi pemphero.” Nafenso tiyenera kukhala ndi maganizo ngati amenewa. Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala ndi chizolowezi chosunga nthawi pa zochita zathu zonse makamaka pa zinthu zokhudza kulambira Mulungu woona.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Tasintha mayina.

[Chithunzi patsamba 26]

Muzikonzekera bwino

[Chithunzi patsamba 26]

Muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti musachedwe ‘pakagwa’ za mwadzidzidzi

[Zithunzi patsamba 26]

Mukamafika pa misonkhano mofulumira, muzipindula kwambiri