Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Tingapewe Bwanji Matenda?

Kodi Tingapewe Bwanji Matenda?

Tsiku lililonse thupi lanu limamenya nkhondo yolimbana ndi adani osaoneka koma oopsa kwambiri. Pali tizilombo tosiyanasiyana, monga mabakiteriya, mavairasi ndi maparasaiti, tomwe timayambitsa matenda. * Nthawi zambiri simungadziwe zoti thupi lanu likulimbana ndi tizilombo timeneti chifukwa chakuti m’thupi lanu muli asilikali amene amapha tizilomboti musanayambe kudwala. Koma nthawi zina tizilomboti timatha kugonjetsa asilikaliwa ndipo mungayambe kudwala. Zikatero mumafunika kuwonjezera chitetezo cha thupi lanu pogwiritsa ntchito mankhwala.

Kale anthu sankadziwa zoti pali tizilombo tosaoneka timene tingawadwalitse. Koma m’zaka za m’ma 1800, asayansi anatulukira kuti matenda ambiri amayamba chifukwa cha majeremusi. Zimenezi zinathandiza kuti papezeke njira zodzitetezera ku tizilomboti. Kuchokera nthawi imeneyo, akatswiri azaumoyo ayesetsa kuthetsa kapena kuchepetsa kufala kwa matenda ena monga nthomba ndi poliyo. Koma masiku ano, matenda ena monga chikasu ndi chingwangwa ayambiranso kufala. Kodi zimenezi zachitika chifukwa chiyani? Tiyeni tione:

  • Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amapita mayiko ena ndipo nthawi zambiri amapita ndi tizilombo toyambitsa matenda. Nkhani ya m’magazini ina ya zaumoyo inanena kuti “pafupifupi matenda onse oopsa” amatha kufalitsidwa ndi anthu amene amayenda kupita mayiko ena.—Clinical Infectious Diseases.

  • Mabakiteriya ena azolowera mankhwala. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linati: “Posachedwapa zikhoza kupezeka kuti mabakiteriya asiya kufa ndi mankhwala, moti anthu akhoza kuyambiranso kufa ndi matenda amene panopa timawatenga ngati osaopsa.”

  • Nthawi zambiri nkhondo komanso umphawi zimalepheretsa zimene boma likufuna kuchita polimbana ndi kufala kwa matenda.

  • Anthu ambiri sadziwa mmene angapewere matenda.

Ngakhale kuti pali mavuto onsewa, pali zinthu zambiri zimene mungachite kuti mudziteteze komanso kuti muteteze banja lanu ku matenda. Nkhani yotsatira isonyeza kuti pali zinthu zosavuta zimene anthu onse, kuphatikizapo a m’mayiko osauka, angachite kuti adziteteze.

^ ndime 3 Tizilombo tambiri tosaoneka sitimayambitsa matenda. Koma nkhanizi zikufotokoza za tizilombo timene timatha kuyambitsa matenda.