Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nsomba Yochititsa Chidwi Kwambiri

Nsomba Yochititsa Chidwi Kwambiri

Nsomba zachikasu

PALI nsomba zochepa zomwe n’zochititsa chidwi kuposa nsomba imeneyi. Tikhoza kuchita chidwi ndi nsombayi chifukwa ndi yokongola kwambiri ndipo imaoneka ngati wina wachita kuipenta. Nsombayi ndi yochititsanso chidwi chifukwa cha malo amene imakhala. Imakhala pakati pa nyama zinazake zam’madzi zooneka ngati maluwa zomwe zimakhala ndi minga zapoizoni.

Mofanana ndi anthu a m’mafilimu, nsombazi siziopa anthu akafuna kuzijambula zithunzi. Anthu osambira m’nyanja akakumana ndi nsombazi amayembekezera kuti ziima kaye kuti azijambule. Zili choncho chifukwa nsombazi sizikonda kupita kutali ndi malo amene zimakhala komanso siziopa anthu.

Koma chochititsa chidwi kwambiri ndi nsombazi ndi malo oopsa amene zimakhala. Zimakhala pakati pa nyama zokhala ndi minga zapoizoni ndipo izi zingafanane ndi munthu yemwe wasankha kumanga nyumba pamalo amene pamakhala njoka zambirimbiri. Komabe n’zodabwitsa kuti nsombazi zimakhala bwinobwino ndi nyamazi. Kodi izi zimatheka bwanji?

 ZIMATHANDIZANA NDIPONSO KUTETEZANA

Mtundu wina wa nsombazi womwe umakhala ndi mizere iwiri

Mofanana ndi anthu amene amagwirizana, nsombazi zimadalirana ndi nyamazi. Nsombazi sizingakhale ndi moyo popanda kuthandizidwa ndi nyamazi. Zili choncho chifukwa zimavutika kusambira. Choncho popanda kutetezedwa ndi nyamazi, zikhoza kugwidwa mosavuta ndi nsomba zina. Koma popeza kuti zimatha kuthawira m’minga za nyamazi, nsombazi zikhoza kufika zaka 10 zili ndi moyo.

Nsombazi zimakhala ndiponso kuikira mazira ake pakati pa minga za nyamazi. Zimaikira mazira m’munsi mwenimweni mwa mingazi ndipo nsomba yaimuna ndi yaikazi yomwe, zimathandizana kuteteza mazirawo. Ndipo zikaswa, ana limodzi ndi makolo amakhalabe pamalowo.

Nanga nyamazi zimathandizidwa bwanji ndi nsombazi? Nsombazi zimateteza nyamazi chifukwa zimathamangitsa nsomba zina zomwe zimakonda kudya minga za nyamazi. Pali mtundu wina wa nyamazi umene sungakhale ndi moyo popanda kuthandizidwa ndi nsombazi. Tikutero chifukwa chakuti pofuna kutsimikizira nkhaniyi, asayansi anachotsa nsombazi pamalo enaake amene panali nyama za mtunduwu. Koma patangopita maola 24 okha, nyama zonse zapamalowa zinadyedwa ndi nsomba zina.

Zikuoneka kuti nsombazi zimathandizanso nyamazi kuti zikhale ndi mphamvu. Mpweya umene nsombazi zimatulutsa umathandiza kuti nyamazi zizikula bwino. Komanso nsombazi zikamasambira, zimachotsa madzi oipa n’kuchititsa kuti madzi abwino azibwera kwa nyamazi.

ZIMAKHALA M’MALO AMENE NSOMBA ZINA ZIMAOPA

Nsomba zapinki

Nsombazi zimatulutsa madzi enaake onanda pakhungu lake omwe amaziteteza ku minga zapoizoni za nyamazi. Chifukwa cha zimenezi nyamazi zimaona ngati nsombazi ndi nyama zinzake. Katswiri wina wa zamoyo zam’madzi ananena kuti zili ngati “nsombazi zimavala zovala za nyamazi pofuna kubisala.”

Akatswiri anapeza kuti pali zinthu zina zimene nsombazi zimayenera kuchita zikafuna kukakhala pamalo a nyama ina yatsopano. Nsombazi zikafika kwa nthawi yoyamba pomwe pali nyamayo, zimakhudza minga zake mobwerezabwereza kwa maola angapo. Zikuoneka kuti kukhudza mingazi n’kumene kumathandiza kuti madzi oteteza khungu la nsombazi azolowere poizoni wa nyama yatsopanoyo. Komabe poyamba zimavutika ndi poizoniyu koma kenako zimazolowera ndipo zimakhala bwinobwino ndi nyamayo.

Pali zambiri zimene tingaphunzire pa zimene zimachitika pakati pa nsomba ndi nyamazi. Anthu azikhalidwe zosiyanasiyana akamakhalira limodzi n’kumathandizana, akhoza kukwanitsa kuchita zinthu zovuta kwambiri. Komabe mofanana ndi nsombazi, nafenso zingatitengere nthawi kuti tizolowere kugwira ntchito ndi anthu ena. Koma tikazolowera tikhoza kuchita zambiri chifukwa muumodzi muli mphamvu.