Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Khirisimasi?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Khirisimasi?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo silinena deti limene Yesu anabadwa komanso silinena kuti tizikondwerera kubadwa kwake. Buku lina limanena kuti: “Mulungu sananene kuti anthu azikondwerera Khirisimasi ndipo m’Chipangano Chatsopano palibe pamene ananena kuti tizikondwerera Khirisimasi.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia

 Ndipo kuona bwinobwino mbiri ya Khirisimasi kungathandize munthu kuzindikira kuti inachokera ku miyambo yachikunja. Baibulo limasonyeza kuti timakhumudwitsa Mulungu tikamamulambira mwanjira imene saivomereza.—Ekisodo 32:5-7.

Mbiri ya miyambo ya Khirisimasi

  1.   Kukondwerera kubadwa kwa Yesu: “Akhristu oyambirira sankakondwerera tsiku limene Yesu anabadwa chifukwa ankaona kuti mwambo wokondwerera tsiku lobadwa la munthu aliyense unali wachikunja.”—The World Book Encyclopedia.

  2.   December 25: Palibe umboni wosonyeza kuti Yesu anabadwa pa December 25. Atsogoleri a Tchalitchi ayenera kuti anasankha detili kuti lifanane ndi zikondwerero zachikunja zomwe zinkachitika cha m’nyengo yozizira.

  3.   Kupatsana mphatso, kuchita phwando, kuvina: Buku lakuti The Encyclopedia Americana limanena kuti: “Anthu amasangalala pa chikondwerero cha Khirisimasi potengera chikondwerero chachiroma chotchedwa Saturnalia, chomwe chinkachitika pakati pa mwezi wa December. Mwachitsanzo, anthu ankachita phwando, kupatsana mphatso komanso kuyatsa makandulo.” Buku lina linanenanso kuti pa nthawi ya Saturnalia, “anthu sankaloledwa kuchita malonda kapena kugwira ntchito.”—The Encyclopædia Britannica.

  4.   Magetsi a Khirisimasi: Buku lina limanena kuti anthu a ku Ulaya amakongoletsa nyumba zawo “ndi magetsi obiriwira” pokondwerera nyengo yozizira komanso pofuna kuthamangitsa mizimu yoipa.—The Encyclopedia of Religion.

  5.   Mitengo Yobiriwira: “Anthu ena ankakhulupirira kuti mtengo winawake wobiriwira unkathandiza anthu mwamatsenga. Anthu ankalambira mtengowu pofuna kuti dzuwa liwale.”—The Encyclopedia Americana.

  6.   Mtengo wa Khirisimasi: “Anthu achikunja a ku Ulaya omwe ankalambira mitengo anapitirizabe kuilambira atalowa Chikhristu.” Iwo “ankaika mtengo wotchedwa Yule pakhomo kapena mkati mwa nyumba nthawi ya maholide a m’nyengo yozizira” n’kumaulambira.—Encyclopædia Britannica.