Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukongola

Kukongola

Anthu amene amakhala ndi maganizo oyenera pa nkhani yokhudza kukongola amakhala osangalala.

N’chifukwa chiyani timasangalala ndi zinthu zokongola?

Ubongo wathu unapangidwa modabwitsa kwambiri moti umatha kuzindikira zinthu zokongola. Palibe amadziwa mmene zimenezi zimachitikira ndipo ngakhale Baibulo silifotokoza. Komabe limanena kuti anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu ndipo izi zimachititsa kuti tizichita chidwi ndi zinthu zokongola. (Genesis 1:27; Mlaliki 3:11) Mulungu analenganso thupi lathu mogometsa kwambiri ndipo limagwira ntchito modabwitsa. Munthu wina wolemba nyimbo ataganizira mmene thupi lathu linalengedwera, ananena kuti: “Ndidzakutamandani [Mulungu] chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.”—Salimo 139:14.

Masiku ano, anthu amakhala ndi maganizo olakwika pa nkhani yokhala wokongola. Anthu opanga mafilimu, zovala komanso oimba amachititsa kuti anthu azikhala ndi maganizo olakwikawa. Buku lina linanena kuti: “Anthu ambiri amasangalala ngati ali ooneka bwino ndipo sadandaula ngakhale atakhala kuti alibe makhalidwe abwino.” (Body Image) Maganizowa ndi olakwika ndipo amapangitsa kuti anthu asamayesetse kukhala ndi khalidwe labwino, lomwe ndi lofunika kuposa maonekedwe.—1 Samueli 16:7.

M’madera ambiri anthu amaona kuti maonekedwe a munthu ndi ofunika kwambiri

Anthu amene amachita chidwi kwambiri ndi mmene thupi la munthu linaumbidwira, makamaka la akazi, amaganiza kuti akazi ooneka bwino amasangalatsa kugonana nawo. Lipoti la bungwe lina linanena kuti: “Nthawi zambiri, pa TV kapena pa intaneti, amasonyeza zithunzi za akazi okongola akamalengeza malonda. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu aziona ngati akazi okongola analengedwa kuti amuna azingogona nawo basi.” (2007 American Psychological Association) Mpake kuti Baibulo limaletsa kutengera maganizo amenewa.—Akolose 3:5, 6.

“Ndipo kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja, . . . koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima, atavala zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa umene uli wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”1 Petulo 3:3, 4.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala pa nkhani yokhudza kukongola?

Anthu ena amanena kuti: “Munthu akakhala wokongola, asamabise kukongola kwake.” Lipoti linanso la bungwe lija linanena kuti m’madera amene anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa, atsikana amayesetsa kudzikongoletsa n’cholinga choti “anthu aziwasirira komanso aziona kuti ndi okongola kwambiri kuposa ena.” Koma maganizo amenewa angabweretse mavuto oopsa. Ndipotu zimenezi zimabweretsa mavuto ambiri pa moyo wa achinyamata komanso zingapangitse kuti “asamasangalale.” Ena mwa mavutowa ndi nkhawa, kudziona kuti ndi wosafunika . . . , kusafuna kudya, kudzikaikira, komanso kudwala matenda a maganizo.”

“Chotsa zosautsa mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku tsoka, chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo n’zachabechabe.”Mlaliki 11:10.

Kodi munthu angasonyeze bwanji kuti amachita zinthu mwanzeru pa nkhaniyi?

Baibulo limasonyeza kuti kuchita zinthu mwanzeru kumagwirizana n’kudzichepetsa. (1 Timoteyo 2:9) Anthu odzichepetsa samadziona kuti ndi apadera ndiponso samangoganizira mmene amaonekera. Iwo amachita zinthu mosapitirira malire komanso amapewa kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. Zimenezi zimapangitsa kuti anthu aziwalemekeza komanso Mulungu aziwakonda. (Mika 6:8) Ndipotu anthu oterewa amapeza anzawo abwino komanso savutika kupeza munthu woti adzakwatirane naye. Mabanja a anthu otere amakhala olimba chifukwa amakwatirana ndi munthu yemwe samangochita chidwi ndi maonekedwe.

Mpake kuti Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukhala ndi khalidwe labwino lomwe ndi “munthu wobisika wamumtima.” (1 Petulo 3:3, 4) Kunena zoona, khalidwe labwino silikalamba. Izi ndi zogwirizana ndi mfundo yopezeka pa Miyambo 16:31 yakuti: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.” Choncho anthu omwe amatsatira malangizo a m’Baibulo amaonedwa kuti ndi okongola ndiponso amapatsidwa ulemu chifukwa cha khalidwe lawo labwino.

“Chikoka chikhoza kukhala chachinyengo ndipo kukongola kukhoza kukhala kopanda phindu, koma mkazi woopa Yehova ndi amene amatamandidwa chifukwa cha zochita zake.”Miyambo 31:30.