Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi N’zotheka Kusintha Zomwe Munazolowera?

Kodi N’zotheka Kusintha Zomwe Munazolowera?
  • AUSTIN akupitirizabe kugona ngakhale kuti alamu yalira. Kenako akudzuka mwadzidzidzi, n’kuvala zovala zothamangira zomwe anazikonzeratu madzulo, n’kupita kothamanga. Iye amathamanga katatu pa mlungu ndipo wakhala akuchita zimenezi kwa chaka.

  • Pambuyo pokangana ndi mwamuna wake, Laurie akuthamangira ku khitchini atakwiya ndipo akutenga paketi ya maswiti n’kudya onse. Zikuoneka kuti nthawi zambiri amachita zimenezi akakwiya.

Pali chinthu chimodzi chimene Austin ndi Laurie akufanana. Onsewa amangochita zinthu zomwe anazolowera ndipo mwina amachita zimenezi asakudziwa n’komwe.

Nanga inuyo mumatani? Kodi pali zinthu zina zabwino zomwe mumafuna mutamachita pamoyo wanu? Mwachitsanzo, mwina mumafuna mutamachita masewera olimbitsa thupi, kumagona mokwanira kapenanso kucheza ndi achibale anu.

Mwinanso pali zinthu zina zoipa zomwe mumafuna mutasiya, monga kusuta, kukonda zakudya zonenepetsa, kapenanso kuthera nthawi yambiri pa intaneti.

Kunena zoona, kusiya zinthu zoipa zomwe munthu anazolowera, sikophweka. Mpake kuti anthu ena amanena kuti kuzolowera kuchita zinthu zoipa kuli ngati kuwotha moto m’nthawi yozizira. Kuyamba kuwotha moto sikuvuta koma kuti uwusiye, imakhala nkhani.

Ndiyeno kodi mungatani kuti muzolowere kumachita zinthu zabwino osati zoipa? Taonani malangizo atatu otsatirawa, omwe ndi ogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.