GALAMUKANI! Na. 4 2016 | Kodi N’zotheka Kusintha Zomwe Munazolowera?

Zinthu zimene tinazolowera zingatithandize kapena kutibweretsera mavuto, ndipo nthawi zina zimenezi zingachitike tisakudziwa n’komwe.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi N’zotheka Kusintha Zomwe Munazolowera?

Muzizolowera kuchita zinthu zabwino osati zoipa.

NKHANI YAPACHIKUTO

1 N’zosatheka Kusintha Lero ndi Lero

N’zosatheka kusiya zoipa zomwe munazolowera n’kuyamba zabwino lero ndi lero. Onani zomwe zingakuthandizeni.

NKHANI YAPACHIKUTO

2 Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kukwaniritsa Zolinga Zanu

Muzikhala malo komanso kucheza ndi anthu omwe angakuthandizeni kuti muzichita zinthu zabwino.

NKHANI YAPACHIKUTO

3 Musafulumire Kugwa Ulesi

Ngakhale zitamakuvutani kusiya zinthu zomwe munazolowera kapena kuzolowera zinthu zatsopano, musagwe ulesi.

Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?

Kodi Baibulo limaletsa kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha? Kodi limalimbikitsa anthu kuti azidana ndi amuna kapena akazi ogonana okhaokha?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Kyrgyzstan

Anthu a ku Kyrgyzstan ndi ochereza komanso aulemu. Kodi amatsatira miyambo yanji yokhudza banja?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukongola

Makampani ofalitsa nkhani komanso opanga zovala angapangitse anthu kuti azingoganizira za maonekedwe awo.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nyenje za Moyo Wautali

Nyenjezi ndi zodabwitsa kwambiri chifukwa zimaonekera kunja kwa milungu yochepa yokha pambuyo pa zaka 13 kapena 17.

Zina zimene zili pawebusaiti

Zimene Mungachite Kuti Musamakangane

Kodi simuchedwa kukangana ndi mwamuna kapena mkazi wanu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zimene zingathandize banja lanu.

Achinyamata Ena Akufotokoza Zokhudza Kukhulupirira Kuti Kuli Mulungu

M’vidiyo ya maminitsi atatuyi, achinyamata akufotokoza chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mulungu.