Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tim’guza Ndowe Timachita Zogometsa

Tim’guza Ndowe Timachita Zogometsa

TIZILOMBO tina totchedwa tim’guza ndowe timagwiritsa ntchito ndowe m’njira zosiyanasiyana. Tizilomboti timadya ndowe, kuikira mazira ake mu ndowe komanso tatimuna timaumba m’bulu waukulu wa ndowe n’kuupereka kwa tatikazi n’cholinga chofuna kukopa tatikazito. Tizilomboti timakanganirana ndowe zosauma chifukwa timaona kuti ndi zosavuta kuumba komanso kukankha. Anthu ena ofufuza zinthu, pa nthawi ina anaona tim’guza ndowe tokwana 16,000 titaunjikana pamulu wa ndowe za njovu. Mmene pankatha maola awiri, mulu wonsewo unali utatha.

Tim’guza ndowe tina timaumba m’bulu waukulu wa ndowe ndipo kenako timaugubuduza n’kukaukwirira mu dothi lofewa. Tizilomboti tikamagubuduza m’buluwo timayenda mosakhotakhota. Timachita izi kuti tiziyenda mwachangu komanso kuti tim’guza ndowe tina tisabe m’buluwo.

Koma kodi tizilomboti timatha bwanji kuyenda mosakhotakhota, makamaka ukhala usiku?

Taganizirani izi: Zotsatira za kafukufuku wina zinasonyeza kuti tim’guza ndowe timatha kuyenda mothandizidwa ndi kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi. Koma timathanso kuyenda usiku mosakhotakhota ngakhale kutakhala kuti kulibe mwezi. Akatswiri ofufuza zinthu a ku South Africa, anapeza kuti tim’guza ndowe timatha kuchita zimenezi, osati chifukwa cha kuwala kwa nyenyezi inayake payokha, koma chifukwa cha kuwala kwa mlalang’amba wa nyenyezi wotchedwa Milky Way. Magazini ina inanena kuti: “Iti n’tizilombo toyamba kudziwika kuti timagwiritsa ntchito kuwala kwa m’lalang’ambawu kuti tizitha kuyenda usiku.”—Current Biology.

Katswiri wina wofufuza zinthu, dzina lake Marcus Byrne, ananena kuti tim’guza ndowe tili ndi “luso linalake lomwe limatithandiza kuyenda bwinobwino ngakhale kukakhala kuti kuli mdima.” Iye ananenanso kuti: “Zimene tizilomboti timachita zingathandize anthu kudziwa njira zopezera zinthu zovuta kuziona.” Choncho potengera mmene tim’guza ndowe timayendera, anthu angathe kukonza loboti m’njira yoti izitha kufufuza mkati mwa nyumba imene yagwa kuti aone ngati muli anthu oti angathe kuwapulumutsa.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tim’guza ndowe tizitha kuchita zinthu mogometsa chonchi, kapena pali winawake amene anatilenga m’njira yoti tizitha kuchita zimenezi?

Kodi mukudziwa?

Tim’guza ndowe timathandiza kuti nthaka isakhale yogwirana kwambiri, timawonjera chonde m’nthaka, timamwaza mbewu komanso timachititsa kuti tizilombo touluka tisachuluke.