GALAMUKANI! June 2014 | Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?

N’zomvetsa chisoni kuti ndi anthu ochepa okha amene ali ndi anzawo enieni. Koma kodi zimayenera kukhala chonchi? Kodi munthu angatani kuti akhale ndi anzake abwino? Werengani malangizo othandiza a m’Baibulo.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake ndi monga zakuti: Zoyenera kuchita ndi mazira omwe anaikidwa m’firiji m’zipatala za ku Canada, zomwe zingakhale zogwirizana ndi malamulo komanso chikhalidwe, zakudya zopatsa thanzi zomwe zingalowe m’malo mwa nyama, komanso maukwati a anthu amene sakhulupirira kuti kuli Mulungu ku Ireland.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bwenzi Labwino?

Anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi mabwenzi n’kofunika. Kodi mungatani kuti mukhale bwenzi labwino? Nkhaniyi ikufotokoza mfundo 4 za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Imfa

Kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira? Kodi pali chiyembekezo choti tingadzaonanenso ndi okondedwa anthu amene anamwalira? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limanena.

TIONE ZAKALE

Joseph Priestley

Priestley akamalemba za sayansi kapena zachipembedzo, ankatsutsa mfundo zabodza ndipo ankayesetsa kupeza zoona pa nkhaniyo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene anachitira zimenezi.

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Chiseyeye

Chiseyeye ndi amodzi mwa matenda ofala kwambiri padziko lonse. Kodi n’chiyani chimayambitsa matendawa? Kodi mungadziwe bwanji kuti mukudwala matendawa? Kodi mungatani kuti musadwale matendawa.

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Musamawononge Ndalama Zambiri?

Musadikire mpaka ndalama zanu kutha musanayambe kuganizira njira yoyenera yogwiritsira ntchito ndalama. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito ndalama mosamala.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Tim’guza Ndowe Timachita Zogometsa

Kodi tim’guza ndowe tili ndi luso lotani? Kodi anthu angaphunzire chiyani kwa tizilomboti?

Zina zimene zili pawebusaiti

Mose Anabadwira ku Iguputo

Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani yokhudza Mose ali ku Iguputo? Koperani nkhanizi ndipo muzikambirane pamodzi monga banja.