Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

China

Kuyambira January mpaka September 2013, chiwerengero cha mabanja omwe anatha, chinawonjezereka kwambiri mumzinda wa Beijing poyerekeza ndi chiwerengero cha mabanja amene anatha kuyambira January mpaka September 2012. Akatswiri akukhulupirira kuti anthu ambiri akumathetsa mabanja pofuna kuti alipire ndalama zochepa pa msonkho umene munthu amene wagulitsa nyumba amafunika kulipira ku boma. Izi zili choncho chifukwa anthu amene athetsa banja lawo, akafuna kugulitsa nyumba yawo yachiwiri amalipira ndalama zochepa ku boma.

Padziko Lonse

Bungwe la United Nations likulimbikitsa anthu kuti azidya tizilombo todyedwa, pofuna kuthana ndi vuto losowa zakudya m’thupi. Malinga ndi lipoti lina la posachedwapa, tizilombo todyedwati timakhala topatsa thanzi ndipo “tikhoza kulowa m’malo mwa nyama.” Tizilomboti timadya zakudya zopatsa thanzi zimene anthu samadya ndiye anthu akadya tizilomboti amakhala athanzi. Komabe lipotili linasonyezanso kuti “m’mayiko ena anthu saloledwa kudya tizilomboti.”

Canada

Zipatala zina zimathandiza anthu amene akulephera kukhala ndi mwana, potenga dzira la mayi n’kuliphatikiza ndi umuna, kenako n’kuliikanso m’mimba mwa mayiyo. Ogwira ntchito m’zipatalazi sakudziwa kuti angatani ndi mazira osungidwa m’firiji amene anayamba kukula koma eniake sakudziwika. Iwo akufuna kudziwa zimene angachite ndi mazirawa, zomwe zingakhale zogwirizana ndi malamulo komanso chikhalidwe. Lipoti lina linasonyeza kuti chipatala chimodzi chokha chikusunga mazira oposa 1,000 amene eni ake sabweranso.

Ireland

M’mbuyomu Akatolika a ku Ireland akafuna kumangitsa ukwati, ankasankha kutsatira mwambo wa chipembedzo, kapena kukangolembetsa kuboma. Koma kuyambira mu 2013, anthu akuthanso kusankha mwambo wina womwe umayendetsedwa ndi anthu osakhulupirira Mulungu. Mogwirizana ndi zimene magazini ina inanena, anthu osakhulupira Mulungu omwe akumamangitsa maukwati a anthu akumalandira anthu ambiri. Zili choncho chifukwa “anthu omwe alembetsa ukwati wawo kuboma ndipo akufuna kuchitanso mwambo wina, koma osati wa m’tchalitchi, akumapita kwa anthuwa kuti awachititsire mwambo wa ukwati.”