Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Kodi Mungatani Kuti Musamawononge Ndalama Zambiri?

Kodi Mungatani Kuti Musamawononge Ndalama Zambiri?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti mwangokwatirana kumene koma mukuona kuti ndalama zimene mukupeza sizikuchedwa kutha ndipo zikungokhala ngati zikulowa m’thumba lobooka. Kodi vuto ndi ndani? Musayambe kulozana chala. M’malomwake, ganizirani zimene nonsenu mungachite kuti musamawononge ndalama. *

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kusintha kwa zinthu pa moyo. Ngati munkakhala ndi makolo anu musanalowe m’banja, n’kutheka kuti simunazolowere kugwiritsa ntchito ndalama komanso kulipira zinthu zina. Zikhozanso kutheka kuti mumagwiritsa ntchito ndalama mosiyana. Mwachitsanzo, wina akhoza kukhala kuti amakonda kugwiritsa ntchito ndalama zonse zimene ali nazo pamene wina amakonda kusunga. Pamatenga nthawi yaitali kuti mwamuna ndi mkazi wake ayambe kuona nkhani ya ndalama mofanana.

Mofanana ndi mmene udzu umakulira m’munda ukapanda kulimidwa, kulephera kubweza ngongole kungachititse kuti ngongole zizingounjikana

Kuzengereza. Bambo wina dzina lake Jim, amene ali ndi bizinezi yaikulu, ananena kuti atangokwatira kumene sankagwiritsa bwino ntchito ndalama ndipo zimenezi zinamubweretsera mavuto aakulu. Iye anati: “Chifukwa choti ndinkachedwa kupereka ngongole, tinkawononga ndalama zambiri chifukwa polipira ngongoleyo tinkafunikanso kupereka chindapusa.”

Kuwononga ndalama zambiri mosadziwa. Munthu akhoza kuwononga ndalama zambiri ngati sakuona ndalamazo zikutuluka m’thumba mwake. Zimenezi zingachitike ngati amakonda kugula zinthu pa ngongole kapena pogwiritsa ntchito khadi la kubanki. Mwachitsanzo, kutenga zinthu pangongole kungapangitse anthu amene angokwatirana kumene kuti akopeke ndi kugula zinthu za ndalama zambiri.

Nkhani ya ndalama ikhoza kubweretsa mavuto aakulu m’banja lanu. Buku lina linanena kuti: “Mabanja ambiri amanena kuti nkhani ya ndalama ndi imene imayambitsa mavuto m’banja lawo, kaya ali ndi ndalama zambiri kapena ayi. Ndipo kawirikawiri anthu okwatirana amakangana pa nkhani za ndalama.”—Fighting for Your Marriage.

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzichita zinthu mogwirizana. M’malo moona kuti mnzanu ndi amene akuwononga kwambiri ndalama, muzikambirana zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. Musanayambe kukambira, muzitsimikiza mtima kuti nkhaniyi isapangitse kuti mukangane.—Lemba lothandiza: Aefeso 4:32.

Muzipanga bajeti. Kwa mwezi umodzi, lembani ndalama iliyonse imene mwagwiritsa ntchito ngakhale itakhala yochepa. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa mmene mukugwiritsira ntchito ndalama. Zingakuthandizeninso kuona ngati pali zinthu zosafunika kwenikweni zimene zakuwonongerani ndalama. Jim amene tamutchula kale uja ananenanso kuti: “Si bwino kuwononga ndalama pa zinthu zosafunika.”

Lembani zinthu zofunika kwambiri zoti mugule kapena kulipira monga chakudya, zovala, lendi, kukonzetsera galimoto ndi zina zotero. Kenako lembani ndalama zimene mungawononge pa chinthu chilichonse pa mwezi umodzi.—Lemba lothandiza: Luka 14:28.

“Wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsayo.”—Miyambo 22:7

Mwezi uliwonse, muziika padera ndalama zimene mukuyenera kuwononga pa zinthu mwalemba zija. Ena amaika mu maemvulopu osiyana ndalama zimene akufuna kugwiritsa ntchito pa chinthu chilichonse. * Akaona kuti ndalama za mu emvulopu ina zatha, amasiya kugula zinthuzo kapena amatenga ndalama za mu emvulopu ina.

Muzikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya katundu. Kukhala ndi katundu wambiri si kumene kumachititsa kuti munthu akhale wosangalala. Pa mfundo imeneyi, Yesu anati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Mmene mumagulira katundu zimasonyeza ngati mumakhulupira zimene Yesu ananenazi kapena ayi.—Lemba lothandiza: 1 Timoteyo 6:8.

Sinthani zina ndi zina. Aaron amene wakhala m’banja zaka ziwiri ananena kuti: “Zinthu ngati kukhala ndi matchanelo a TV olipira kapena kukadya kulesitilanti, zimawononga ndalama ngakhale kuti poyamba munthu sungazindikire. Tinkafunika kudziletsa kugula kapena kuchita zinthu zina n’cholinga choti tisamawononge ndalama zambiri kuposa zimene tinkapeza.”

^ ndime 4 Ngakhale kuti nkhaniyi ikukamba kwambiri za anthu amene angokwatirana kumene, mfundo zake zingathandizenso anthu amene akhala m’banja kwa nthawi yaitali.

^ ndime 14 Ngati mumagwiritsira ntchito makadi a kubanki kapena makadi a ngongole pogula zinthu, mungalembe chiwerengero cha ndalama zimene mukufuna kugwiritsira ntchito pa chinthu chilichonse, n’kuika mu maemvulopumo.