GALAMUKANI! December 2013 | Kodi Ofalitsa Nkhani Tingawakhulupirire?

Anthu ambiri akamvetsera kapena kuwerenga nkhani, amakayikira ngati ili yoona. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti musamangokhulupirira nkhani iliyonse.

Zochitika Padzikoli

Nkhani zake: Ophunzira kwambiri, matenda a m’mapapo, kusokonezeka powoloka msewu, ndi zina zambiri.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Ofalitsa Nkhani Tingawakhulupirire?

Werengani kuti mudziwe zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati nkhani imene mwawerenga kapena kumvetsera ili yolondola.

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Brazil

Dziko la Brazil ndi lalikulu pafupifupi hafu ya South America. Werengani kuti mudziwe kumene chikhalidwe cha m’dziko la Brazil chinachokera.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yesu

Kodi Yesu ndi Mulungu? Kodi Yesu anabadwa liti? Kodi anaukitsidwadi?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?

Kumvetsera mwatcheru si luso chabe koma ndi njiranso yosonyezera kuti mnzanuyo mumamukonda. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene mungachite kuti muzimvetsera mwamuna kapena mkazi wanu akamalankhula.

Agulugufe Ochita Zinthu Mogometsa

Kwa nthawi yaitali anthu ambiri a ku Ulaya akhala akuchita chidwi kwambiri ndi agulugufe enaake. Akatswiri ofufuza apeza zimene agulugufewa amachita nyengo yozizira ikamayamba.

Mlozera Nkhani wa Magazini a Galamukani! a 2013

Mlozera nkhani wa nkhani zonse zimene zinatuluka m’magazini a Galamukani! a 2013 mogwirizana ndi nkhani zake.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kuchuluka kwa Zinthu Zimene DNA Imasunga

Werengani kuti mudziwe mmene DNA ilili chipangizo chapamwamba kwambiri chosungira zinthu.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Ndingatani Ngati Anthu Ena Akukonda Kunena za Ine?

Kodi mungatani kuti zinthu zabodza zimene anthu akufalitsa zokhudza inuyo zisawononge mbiri yanu?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani pa Nkhani Yotumizirana Mameseji ndi Zinthu Zina Zolaula?

Kodi munthu wina amakukakamizani kuti mumutumizire zolaula? Kodi kutumizirana zolaula kuli ndi mavuto otani? Kodi ndi kukopana basi?

Farao Anapatsa Yosefe Udindo Waukulu

Malizitsani kujambula chithunzichi kuti mudziwe chifukwa chake abale ake a Yosefe analephera kumuzindikira.