Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

  KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kuchuluka kwa Zinthu Zimene DNA Imasunga

Kuchuluka kwa Zinthu Zimene DNA Imasunga

ANTHU amene amagwiritsa ntchito makompyuta amapanga zinthu zambirimbiri n’kuzisunga pakompyuta kuti azizigwiritsa ntchito akazifuna. Asayansi akufuna atapeza njira zatsopano zapamwamba kwambiri zosungira zinthu zambirimbiri potengera mmene DNA imasungira zinthu.

Taganizirani izi: DNA imapezeka m’maselo ndipo imasunga zinthu mabiliyoni ambirimbiri. Katswiri wina wasayansi yokhudza za makompyuta, dzina lake Nick Goldman, ananena kuti: “Pogwiritsa ntchito kachidutswa ka fupa la zinyama zikuluzikulu zimene sizipezekanso masiku ano, tingathe kudziwa zinthu zambiri zokhudza nyamazo. Ngakhale kuti kachidutswaka kamakhala kakang’ono kwambiri, kamasunga zinthu zambirimbiri ndipo sikafuna mphamvu iliyonse kuti kasunge zinthuzo. Choncho kusunga komanso kutumiza kanthuka sikuvuta.” Kodi DNA ingasunge zinthu monga nyimbo komanso zinthu zina zimene anthu amasunga pakompyuta? Akatswiri akuona kuti ikhoza kusunga.

Asayansi atulukira njira yosungira zinthu mu DNA ngati mmene zimasungidwira mukompyuta. Zinthu zimenezi ndi monga zithunzi, mawu olembedwa komanso nyimbo. Mwachitsanzo, atasintha zinthuzi n’kuziika mu DNA, kenako, anayesanso kuzisintha n’kuzibwezeretsa kuti zikhale mmene zinalili poyamba, koma anapeza kuti palibe chilichonse chimene chinasintha. Asayansiwa akuganiza kuti pogwiritsa ntchito njirayi, DNA yochita kupanga yaing’ono kwambiri, izitha kusunga zinthu zimene zingasungidwe m’ma CD okwana 3 miliyoni ndipo zinthu zimenezi zikhoza kusungidwa kwa zaka mahandiredi kapenanso masauzande ambirimbiri. Ngati zimenezi zitatheka, ndiye kuti angathe kusunga zinthu zonse zimene anthu angafune kusunga padziko lonse. Choncho DNA ndi chipangizo chapamwamba kwambiri chosungira zinthu.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti DNA izitha kusunga zinthu zochuluka chonchi kapena pali wina amene anachita kukonza kuti izichita zimenezi?