Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Agulugufe Ochita Zinthu Mogometsa

Agulugufe Ochita Zinthu Mogometsa

KWA NTHAWI yaitali anthu ambiri a ku Ulaya akhala akuchita chidwi kwambiri ndi agulugufe enaake ndipo ankadabwa kuti nyengo yozizira ikamayamba agulugufewa amapita kuti. Kodi amafa chifukwa cha kuzizira? Koma pa kafukufuku wina amene wachitika posachedwapa apeza zimene agulugufewa amachita, zomwe n’zochititsa chidwi kwambiri. Chaka chilichonse iwo amasamuka n’kuyenda mtunda wautali kwambiri kuchoka kumpoto kwa Ulaya kupita ku Africa.

Ochita kafukufukuyo anaphatikiza zimene anapeza zokhudza agulugufewa ndi zomwe anthu ena omwe amachitanso nawo chidwi anawauza. Zimene anapeza zinasonyeza kuti agulugufewa, omwe amakhalapo ambirimbiri, amasamuka nyengo yotentha ikamatha n’kuyamba ulendo wautali kwambiri wopita ku Africa. Zimakhala zovuta kuti anthu aone agulugufewa chifukwa nthawi zambiri amauluka m’mwamba kwambiri, mamita oposa 500. Agulugufewa amadikira mphepo inayake imene imawathandiza kuti aziuluka pa liwiro la makilomita 45 pa ola limodzi. Ulendowu ndi wautali makilomita 15,000, ndipo umayambira kumpoto kwa Ulaya mpaka kukafika kum’mwera kwa West Africa. Ulendo umenewu ndi wautali kuwirikiza kawiri ulendo umene agulugufe ena amene amapezeka ku North America amayenda. Kuti agulugufewa ayende ulendo wochoka ku Ulaya kupita ku Africa n’kubwereranso ku Ulaya, pamatenga mibadwo 6 ya agulugufewa.

Pulofesa wa pa yunivesite ina ya ku England, dzina lake Jane Hill, ananena kuti: “Agulugufewa amayenda ulendowu osatopa ndipo ali pa ulendowu, amaswa ana kenako n’kumapitirira.” Chaka chilichonse, gulu lonse la agulugufewa limachita zimenezi ndipo limachoka ku Ulaya kupita ku Africa n’kubwereranso ku Ulaya.

Mkulu wa malo ena ofufuza zokhudza agulugufe, dzina lake Richard Fox, anati: “Ngakhale agulugufewa amayenda ulendo wautali chonchi, ndi ang’onoang’ono kwambiri ndipo kaubongo kawo n’kakang’ono kwambiri kuposa kanjere kampiru. Komanso alibe mwayi wophunzira za ulendowu kuchokera kwa makolo awo chifukwa makolowo amafa mkati mwa ulendowu.” Iye ananenanso kuti poyamba anthu ankaganiza kuti agulugufewa amangokankhidwa ndi mphepo imene imawathandiza kuti asafe ndi nyengo yozizira. Koma kafukufuku amene wachitika posachedwayu anasonyeza kuti agulugufe amenewa ndi anzeru kwambiri ndipo amadziwa zimene akuchita.