Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

  ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Brazil

Dziko la Brazil

Anthu a ku Brazil amakonda kwambiri chakudya chokoma chotchedwa feijoada

Mbalame yotchedwa toucan

POYAMBA ku Brazil kunkakhala alenje ndi alimi. Kenako Apwitikizi anafika m’dzikoli n’kuyambitsa Chikatolika ndipo patapita nthawi, m’dzikoli munamangidwa matchalitchi ambiri. Ena mwa matchalitchiwa ankawakongoletsa ndi ziboliboli zokutidwa ndi golide.

Cham’katikati mwa zaka za m’ma 1500 mpaka 1800, sitima zapanyanja zinabweretsa akapolo okwana 4 miliyoni kuchokera ku Africa kuti azigwira ntchito m’minda. Anthu amenewa anabwera ndi miyambo yakwawo, zimene zinapangitsa kuti m’dzikoli mukhale zipembedzo zophatikizana monga macumba komanso candomblé. Nyimbo, magule komanso zakudya za m’dzikoli zimasonyeza kuti zinachokera ku chikhalidwe cha ku Africa.

Anthu a m’dzikoli amakonda kudya chakudya china chotchedwa feijoada chimene amachipanga pophatikiza nyama komanso nyemba zakuda ndipo amadyera mpunga wosakaniza ndi masamba. Chakudyachi chinachokera ku Portugal. M’zaka za m’ma 1800 mpaka  1900, m’dzikoli munafikanso anthu ochokera ku Germany, Italy, Poland, Spain, Japan komanso mayiko ena.

Ku Brazil kuli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 11,000 ndipo muli Mboni zoposa 750,000. A Mboniwa amaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 800,000. Pofuna kuti akhale ndi malo abwino oti azisonkhanamo, magulu 31 ogwira ntchito yomanga, amamanga komanso kukonza Nyumba za Ufumu pafupifupi 250 kapena 300 pa chaka. Kuchokera mu March 2000, Nyumba za Ufumu zokwana 3,647 zamangidwa kapena kukonzedwa.

KODI MUKUDZIWA?

Mtsinje wa Amazon ndi wautali makilomita 6,275 ndipo ndi umene umathira madzi ambiri m’nyanja kuposa mtsinje uliwonse padziko lonse

Mbali yaikulu ya mtsinje wa Amazon ili m’nkhalango yaikulu padziko lonse