Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

  MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?

Kodi Mungatani Kuti Muzimvetsera Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akamalankhula?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti mkazi kapena mwamuna wanu akunena kuti, “Simukumvetsera zimene ndikunena!” Koma inuyo mukuona kuti mukumvetsera. Apa ndiye kuti zimene inuyo mwamva si zimene mnzanuyo akutanthauza. Zimenezi zingangopangitsa kuti muyambenso kukangana.

Koma n’zotheka kupewa mavuto amenewa. Choyamba mungafunike kudziwa chimene chimapangitsa kuti musamve mfundo zina zimene mkazi kapena mwamuna wanu akunena, ngakhale inuyo mutaona kuti mukumvetsera.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kusokonezedwa ndi zinthu zina komanso kutopa. Mkazi wanu akuyamba kulankhula pa nthawi imene ana akulira, TV ikusokosera kapena pa nthawi imene inuyo mukuganizira za mavuto amene mwakumana nawo kuntchito. Ndiyeno akukuuzani kuti madzulo mukhala ndi alendo. Mukugwedeza mutu n’kunena kuti, “Chabwino.” Koma kodi mwamvadi zimene iye wanena? Mwina ayi.

Kuganiza molakwika. Mkazi kapena mwamuna wanu akalankhula mawu enaake mungaganize kuti akutanthauza zinazake osati zimene akunenazo. Koma mwina zimene mukuganizazo si zoona. Mwachitsanzo, mnzanuyo angakuuzeni kuti: “Mlungu uno mwagwira maovataimu ambiri.” Poganiza kuti akukudzudzulani, mungayankhe kuti: “Koma iweyo ndi amene umachititsa kuti ndizigwira maovataimu chifukwa umawononga ndalama zambiri. Ukuganiza kuti tingamapeze kuti ndalama zimene umagulira zinthu, nditapanda kumagwira maovataimu?” Apa mnzanuyo akuyankha mopsa mtima kuti: “Ine sindikuti mwalakwa.” Maganizo ake anali oti mukhale pakhomo Loweruka ndi Lamlungu kuti mupume chifukwa mwagwira ntchito kwambiri.

Kupupuluma. Mkazi wina, dzina lake Marcie, * ananena kuti: “Nthawi zina ndimangofuna kunena mmene ndikumvera, koma mwamuna wanga, Mike, amayamba kundiuza mmene ndingathetsere vutolo. Sikuti cholinga changa chimakhala choti andiuze mmene ndingathetsere vutolo. Ndimangofuna adziwe mmene ndikumvera.” Kodi pamenepa vuto limakhala chiyani? Mike amangothamangira kupeza njira yothetsera vuto. Zotsatira zake zimakhala zoti samva zonse zimene Marcie akunena.

Kaya chimayambitsa vuto n’chiyani, komabe kodi mungatani kuti muzimvetsera mwamuna kapena mkazi wanu akamalankhula?

 ZIMENE MUNGACHITE

Muzimvetsera mwatcheru. Tiyerekeze kuti mkazi kapena mwamuna wanu ali ndi nkhani imene akufuna akuuzeni. Koma kodi ndinu wokonzeka kumvetsera? Mwina ayi, chifukwa choti pa nthawiyi mukuganizira zina. Ngati ndi choncho, musayerekezere ngati mukumvetsera. Siyani kaye zimene mukuchitazo n’kuyamba kumvetsera mwatcheru. Apo ayi muuzeni mnzanuyo kuti akudikireni kuti mumalize kaye zimene mukuchitazo.—Lemba lothandiza: Yakobo 1:19.

Musamadulane mawu. Mnzanuyo akamalankhula, yesetsani kuti musamudule mawu kapena kumutsutsa. Mulankhula nthawi yanu ikafika. Panopa mukuyenera kumvetsera basi.—Lemba lothandiza: Miyambo 18:13.

Muzifunsa mafunso. Zimenezi zingathandize kuti mumvetse bwino zimene mnzanuyo akunena. Marcie uja ananena kuti: “Ndimasangalala mwamuna wanga akamandifunsa mafunso. Zimasonyeza kuti akufuna kumvetsa zimene ndikulankhula.”

Musamangoganizira mawu amene mnzanuyo wanena koma muziyesetsa kumvetsa zimene akutanthauza. Muziona mmene mnzanuyo akuyendetsera manja, akuyang’anira komanso mmene mawu ake akumvekera, chifukwa zimenezi zingakuthandizeni kudziwa zimene akutanthauza. Mawu akuti, “Zili bwino” angatanthauze kuti “Sizili bwino” potengera mmene wawalankhulira. “Simufuna kundithandiza” angatanthauze kuti, “Ndimaona kuti simuona kuti ndine wofunika.” Muziyesetsa kumvetsa zimene mnzanuyo akutanthauza ngakhale pamene sananene mwatchutchutchu. Apo ayi mukhoza kumangokangana pa zimene mnzanuyo wanena m’malo moganizira zimene akutanthauza.

Muzimvetsera mpaka mnzanuyo atamaliza kulankhula. Musachokepo kapena kusiya kumvetsera, ngakhale zitakhala kuti zimene mnzanuyo akulankhula sizikukusangalatsani. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mnzanuyo akulankhula mawu osonyeza kuti inuyo ndinu olakwa? Bambo wina yemwe wakhala m’banja kwa zaka zoposa 60, dzina lake Gregory, ananena kuti: “Muzimvetserabe mwatcheru zimene mnzanuyo akunena. Kuchita zimenezi n’kovuta koma n’kothandiza kwambiri ndipo kumasonyeza kuti simuchita zinthu mwachibwanabwana.”—Lemba lothandiza: Miyambo 18:15.

Muzikhala ndi chidwi chenicheni ndi mnzanuyo. Kumvetsera mwatcheru si luso chabe koma ndi njiranso yosonyezera kuti mnzanuyo mumamukonda. Ngati mukufunadi kumva zimene mnzanuyo akunena, kumvetsera kumakhala kosavuta ndipo simuchita zimenezo chifukwa chokakamizika. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

^ ndime 9 Tasintha mayina m’nkhaniyi.