Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Khazikitsani Malamulo oti Mwana Wanu Azitsatira

Khazikitsani Malamulo oti Mwana Wanu Azitsatira

ZOMWE ZIMACHITIKA

Mwana wanu amaona kuti mumakhazikitsa malamulo ovuta kwambiri kutsatira. Pomwe inuyo mumaona kuti mukapanda kutero ndiye kuti mwanayo alowa m’mavuto.

Sikulakwa kukhazikitsa malamulo oti mwana wanu azitsatira. Komabe ngati iye amaona kuti malamulo anu ndi ovuta kutsatira, fufuzani kuti mudziwe chomwe chimachititsa kuti aziona choncho.

ZOMWE ZIMACHITITSA

Zimene ena amakhulupirira: Mwana aliyense akafika pamsinkhu wachinyamata, amakhala wosamvera malamulo ndipo zimenezi n’zosapeweka.

Zoona zake: Ngati makolo akhazikitsa malamulo omveka bwino n’kukambirana bwino ndi mwana wawo, mwanayo amakhala womvera.

Pali zinthu zambiri zomwe zingachititse mwana kukhala wosamvera, koma nthawi zambiri ana samvera makolo awo chifukwa chakuti makolowo safuna kumva maganizo a ana awo komanso chifukwa chakuti makolowo saganizira msinkhu wa anawo pokhazikitsa malamulo.

  • Kusafuna kumva maganizo a ana. Makolo akamangokhazikitsa malamulo koma osafuna kukambirana kapena kusintha zinthu zina, ana amayamba kuona kuti malamulowo ndi otopetsa. M’malo moti mwana wanu aziona malamulowo ngati nekilesi yomwe ingachititse kuti azioneka bwino, akhoza kuyamba kumaona malamulowo ngati tcheni chomangira galu. Ndiye ngati mwanayo atamaona kuti malamulo anu ndi otopetsa, angamanamizire kuwatsatira koma kwinaku akuchita zosemphana ndi malamulo amene inuyo munakhazikitsa.

  • Kusaganizira msinkhu wa ana. Makolo akamapatsa ana awo malamulo ayenera kuganizira msinkhu wa anawo. Mwachitsanzo, nthawi zambiri makolo akapatsa mwana wamng’ono malamulo, mwanayo amangomvera ndipo safunsa kalikonse. Koma achinyamata asanatsatire malamulo enaake, amafuna aone kaye ngati malamulowo aperekedwa pa zifukwa zabwino. Zili choncho chifukwa choti akamakula amayamba kuganiza mwauchikulire ndipo amadziwa kuti m’zaka zochepa m’tsogolomu azidzakhala paokha n’kumasankha okha  zochita. Choncho ndi bwino kuti aphunzire kusankha zinthu mwanzeru adakali ndi makolo awo.

Ndiye kodi mungatani ngati mwana wanu wachinyamata akuoneka kuti sakumvetsa malamulo anu ndipo akuona ngati ndi ovuta kuwatsatira?

ZIMENE MUNGACHITE

Choyamba, muyenera kukumbukira kuti ana amafuna kudziwa zimene ayenera kuchita ndi zimene sayenera kuchita. Choncho mukakhazikitsa malamulo muzionetsetsa kuti mwana wanu akuwamvetsa bwino. Buku lina linanena kuti: “Achinyamata amakhala omvera akapatsidwa malamulo omveka bwino komanso akadziwa kuti makolo awo akuwayang’anira kuti aone ngati akutsatira malamulowo.” (Letting Go With Love and Confidence) Koma makolo akamangolekerera ana awo kuti azichita zomwe akufuna, anawo amaona ngati makolowo alibe nawo chidwi ndipo zimenezi zingachititse kuti asamamverenso makolowo.—Lemba lothandiza: Miyambo 29:15.

Ndiye kodi mungachite bwanji zimenezi? M’pempheni mwana wanu kuti anene mmene amaonera malamulo amene munakhazikitsa. Mwachitsanzo, mufunseni maganizo ake pa nkhani ya nthawi imene munamuuza kuti azikhala atafika pakhomo. Mumvetsereni mosamala akamafotokoza maganizo ake. Mwana wanu akaona kuti mukumumvetsera komanso kumudera nkhawa, amamvera mwamsanga zimene mwamuuza ngakhale atakhala kuti sakugwirizana nazo.—Lemba lothandiza: Yakobo 1:19.

Komano musanasankhe zochita muyenera kukumbukira kuti achinyamata amafuna ufulu wambiri pomwe makolonu mwina mungaone kuti achinyamatawo safunikira kupatsidwa ufulu wambiri. Choncho musanasankhe zochita muziganizira zimene mwana wanu akufuna. Muyenera kuonanso ngati mwana wanu amachita zinthu mwauchikulire. Komanso ndi bwino kusintha ngati mwaona kuti n’zofunika kutero.—Lemba lothandiza: Genesis 19:17-22.

Kuwonjezera pa kumvetsera maganizo a mwana wanu, muyeneranso kumuuza maganizo anu. Zimenezi zingamuthandize kudziwa kuti nthawi zonse asamangoganizira zofuna zake koma aziganiziranso zofuna za ena.—Lemba lothandiza: 1 Akorinto 10:24.

Pamapeto pake, khazikitsani malamulo oti mwana wanu aziyendera ndipo muuzeni zifukwa zomwe mwawakhazikitsira. Ngakhale atakhala kuti sakugwirizana ndi malamulo omwe mwakhazikitsa, mwana wanu anganyadire kuti ali ndi makolo omwe amamva maganizo ake. Ndipotu muzikumbukira kuti pamene wachinyamata adakali pakhomo amakhala akuphunzira zinthu zambiri zomwe zidzamuthandize akadzakula.—Lemba lothandiza: Miyambo 22:6.