Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Bambo Wabwino Amatani?

Kodi Bambo Wabwino Amatani?

Bambo wina wa ku South Africa, dzina lake Michael, * amadzifunsa kuti: “Kodi ndinalakwitsa pati polera mwana wanga?” Bamboyu anayesetsa kulera bwino mwana wake wamwamuna koma mmene mwanayo amafika zaka 19, anali atalowerera. Nthawi zonse bamboyu akaganizira za mwana wakeyo amadandaula kuti mwina sanamulere bwino.

Koma mosiyana ndi Michael, Terry, yemwe amakhala ku Spain, anakwanitsa kulera bwino mwana wake. Mwana wake Andrew, ananena kuti: “Ndimakumbukira kuti ndili mwana bambo anga ankakonda kundiwerengera mabuku komanso kusewera nane. Tinkakondanso kupita kumalo osiyanasiyana zomwe zinkachititsa kuti tizikhala ndi nthawi yocheza. Anandiphunzitsa zinthu zosiyanasiyana.”

Kunena zoona, kukhala bambo wabwino si nkhani yamasewera. Koma m’Baibulo muli malangizo amene angathandize kuti bambo alere bwino ana ake. Tiyeni tione ena mwa malangizo amenewa.

 1. Muzipeza Nthawi Yocheza ndi Banja Lanu

Kodi mumasonyeza bwanji kuti mumakonda ana anu? Pali zambiri zimene mumachita, mwachitsanzo, mumayesetsa kupezera ana anu chakudya komanso malo abwino okhala. Simukanachita zimenezi mukanakhala kuti simumawakonda. Koma ngati simupeza nthawi yokwanira yocheza ndi ana anu, iwo angamaganize kuti mumakonda ntchito yanu, anzanu komanso zinthu zina kuposa iwowo.

Ndiye kodi bambo angayambe liti kucheza ndi ana ake? Mayi ndi mwana amayamba kukondana mwanayo adakali m’mimba. Mwanayo amayamba kumva zimene zikuchitika pakadutsa miyezi inayi kuchokera pamene mayiyo anatenga pakati. Pa nthawi imeneyi bambo akhozanso kuyamba kukondana ndi mwanayo. Akhoza kumamvetsera kugunda kwa mtima wake, kumamva akasuntha, kumamulankhula kapena kumamuimbira nyimbo.

Mfundo ya m’Baibulo: Kale, azibambo ankafunika kumaphunzitsa ana awo. Ankauzidwa kuti azipeza nthawi yocheza ndi ana awo. Zimenezi n’zimene zinalembedwa pa Deuteronomo 6:6, 7, pomwe pamati: “Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako. Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.”

2. Muzimvetsera Ana Anu Akamalankhula

Muzimvetsera moleza mtima ndipo musamafulumire kumuimba mlandu

Kuti muzilankhulana bwino ndi ana anu, muyenera kumamvetsera mwatcheru akamalankhula. Komanso muzipewa kukwiya msanga.

Ngati ana anu amadziwa kuti akakuuzani nkhani simuchedwa kukwiya kapena kuwaimba mlandu, sangamasuke kukuuzani nkhawa zawo. Koma mukamawamvetsera moleza mtima, mumasonyeza kuti mumawadera nkhawa ndipo zimenezi zingachititse kuti azimasuka kukuuzani nkhawa zawo komanso maganizo awo.

Mfundo ya m’Baibulo: Malangizo opezeka m’Baibulo amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino pambali zosiyanasiyana za moyo wathu. Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) Bambo akamatsatira malangizo amenewa sizikhala zovuta kulankhulana bwino ndi ana ake.

 3. Muziwalangiza Komanso Kuwayamikira

Bambo ayenera kupereka chilango kwa mwana n’cholinga choti athandize mwanayo kuti zinthu zidzamuyendere bwino akadzakula, osati kuti aphwetsere mkwiyo wake pa mwanayo. Chilangocho chingakhale kungomulangiza, kumudzudzula, kumuphunzitsa kapena kumukwapula kumene ngati pakufunika kutero.

Nthawi zambiri ana amamvera malangizo a makolo ngati makolowo amawayamikira akachita zabwino. Baibulo limati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” (Miyambo 25:11) Ana akamaona kuti makolo awo amawayamikira amakhala ndi makhalidwe abwino. Komanso akaona kuti makolo awo amawaona kuti ndi ofunika samadziderera. Bambo amene amayamikira ana ake amawathandiza kuti aziyesetsa kuchita zabwino nthawi zonse.

Mfundo ya m’Baibulo: “Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”Akolose 3:21.

4. Muzikonda ndi Kulemekeza Mkazi Wanu

Abambo ayenera kukumbukira kuti mmene amachitira zinthu ndi mkazi wawo zimakhudzanso ana. Akatswiri ena oona za mmene ana amakulira ananena kuti: “Njira imodzi imene bambo angaphunzitsire ana ake makhalidwe abwino ndi kulemekeza mkazi wake . . . Makolo amene amakondana komanso kulemekezana amapangitsa kuti ana azisangalala komanso azimva kuti amakondedwa.”—The Importance of Fathers in the Healthy Development of Children. *

Mfundo ya m’Baibulo: “Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, . . . aliyense wa inu akonde mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha.”—Aefeso 5:25, 33.

 5. Muzitsatira Malangizo a Mulungu

Bambo amene amakonda kwambiri Mulungu amathandiza ana ake kuti akhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, chomwe ndi chinthu chamtengo wapatali chimene bambo angachitire ana ake.

Bambo wina wa Mboni za Yehova yemwe anakwanitsa kulera bwino ana 6, dzina lake Antonio, analandira kalata yochokera kwa mwana wake wamkazi. Kalatayo inalembedwa kuti: “Okondedwa Adadi, ndikufuna kukuthokozani chifukwa chondithandiza kukonda Yehova Mulungu komanso anthu ena. Mmene munkachitira zinthu munkasonyeza kuti mumakonda Yehova komanso kuti munkandidera nkhawa. Zikomo kwambiri chifukwa cha zimenezi komanso chifukwa chotikonda ngati mphatso yochokera kwa Mulungu.”

Mfundo ya m’Baibulo: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Ndipo mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako.”Deuteronomo 6:5, 6.

N’zoona kuti pali zinthu zambiri zimene mungachite kuti mukhale bambo wabwino kuwonjezera pa zimene takambiranazi. Komabe, choti mudziwe n’chakuti, ngakhale mutayesetsa kukhala bambo wabwino, muzikumanabe ndi mavuto. Komabe mukhoza kukhala bambo wabwino ngati muzikonda ana anu komanso kuwapatsa zimene amafunikira. *

^ ndime 3 Tasintha mayina m’nkhaniyi.

^ ndime 19 Mfundo imeneyi ndi yothandizanso ngati banja linatha. Kaya anawo akukhala ndi bamboyo kapena mayi, ngati bamboyo amalemekezabe mayiyo, zingathandize kuti anawo azilemekezanso mayi awo.

^ ndime 25 Mukhoza kupeza mfundo zina zothandiza m’banja m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lomwenso likupezeka pa Webusaiti ya www.jw.org.