Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Inuyo Mungakonde Kusintha Zinthu Ziti?

Kodi Inuyo Mungakonde Kusintha Zinthu Ziti?

Kodi Inuyo Mungakonde Kusintha Zinthu Ziti?

Kodi ndi zinthu ziti padzikoli zimene zimakudetsani nkhawa kwambiri?

NJALA

UMPHAWI

MATENDA

KUPHWANYA MALAMULO

KUPANDA CHILUNGAMO

NKHONDO

KUWONONGEKA KWA MPWEYA, NTHAKA NDI MADZI

TSANKHO

Kodi pa zinthu zotsatirazi, ndi ziti zimene mumalakalaka zitachitika?

ANTHU AMITUNDU YONSE ATAMAKHALA MOGWIRIZANA

ALIYENSE ATAMAPEZA CHITHANDIZO CHAMANKHWALA MOSAVUTA

TSANKHO LITATHA

ALIYENSE ATAMAPEZA CHAKUDYA NDI MADZI AKUMWA OKWANIRA

ANTHU ATAMAKHALA M’NYUMBA ZAWO MOPANDA MANTHA

ANTHU ALI NDI MALO ABWINO OKHALA

ALIYENSE ATAMACHITIRIDWA ZINTHU MWACHILUNGAMO

Kodi mukuganiza kuti zimene mumalakalakazi zidzachitikadi? Ena amaganiza kuti zikhoza kuchitika ngati maboma atamayendetsa bwino zinthu. Koma kodi atsogoleri a mayiko angasinthedi zinthu padzikoli? Kodi zimene zikuchitika masiku ano zikusonyeza kuti iwo angasinthedi zinthu?