Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Anthu ena akumagwiritsa mafoni a m’manja pofuna kuti asalankhulane ndi anzawo. Akuti anthu 13 pa 100 aliwonse ananamizirapo kulankhula pa foni n’cholinga choti anthu ena asawalankhulitse.”—PEW RESEARCH CENTER, U.S.A.

Pa zaka zisanu zapitazi madzi oundana akhala akusungunuka m’madera ozizira kwambiri pa dziko lapansi.—BBC NEWS, BRITAIN.

“Ku Africa kuno kuli malo ambirimbiri omwe anthu angamalime koma sakulimidwa.”—THE WITNESS, SOUTH AFRICA.

“Pa zaka 10 zapitazi, mayiko a Netherlands, Belgium, Canada, Spain, South Africa, Norway, Sweden, Portugal, Iceland, ndi Argentina anakhazikitsa malamulo ololeza kuti amuna kapena akazi okhaokha azikwatirana.”—FAMILY RELATIONS, U.S.A.

Akuvutikabe Ndi Nkhondo Yakalekale

Kafukufuku amene yunivesite ina ya ku Northern Ireland inachita anasonyeza kuti anthu ambiri akuvutika maganizo chifukwa cha nkhondo imene inachitika m’dzikolo kwa pafupifupi zaka 30. Nkhondoyi inachitika chifukwa chosiyana zipembedzo ndi zipani. Pa kafukufukuyu anapezanso kuti munthu mmodzi pa anthu 10 aliwonse amachita mantha chifukwa cha zinthu zoopsa zimene zinachitika pa nthawi ya nkhondoyi. Nyuzipepala ina inanena kuti: “Chiwerengero chimenechi ndi chokwera kwambiri” poyerekeza ndi cha m’mayiko ena. Inanenanso kuti: “Nkhondoyi ndi chimodzi mwa zinthu zimene zapha anthu ambiri pa dziko lonse.”—The Irish Times.

Anthu Angofika Pozolowera Kusintha kwa Nyengo

Nyengo yasintha kwambiri ku United States ndipo zimenezi zikuchititsa kuti kusefukira kwa madzi, chilala komanso mphepo ya mkuntho zizichitika kawirikawiri moti anthu angofika pozizolowera. Akatswiri ena a zanyengo m’dzikolo anachita msonkhano wokambirana za kusintha kwa nyengo. Pa msonkhanowu mmodzi wa akatswiriwa, dzina lake Katharine Hayhoe, wa pa yunivesite ya Texas Tech, ananena kuti: “Nyengo yasintha kwambiri moti zimene zikuchitika masiku ano ndi zachilendo.” Hayhoe komanso akatswiri ena akukhulupirira kuti nyengo yasintha kwambiri chifukwa anthu akuwononga zachilengedwe.