Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tingathandize Bwanji Mwana Yemwe Wachibale Wake Wamwalira?

Kodi Tingathandize Bwanji Mwana Yemwe Wachibale Wake Wamwalira?

Kodi Tingathandize Bwanji Mwana Yemwe Wachibale Wake Wamwalira?

Nthawi zambiri zimakhala zovuta kuuza munthu wachikulire kuti wachibale wake wamwalira. Koma zimakhala zovuta kwambiri ngati amene mukufunika kumuuzayo ali mwana.

ANA ambiri amasokonezeka maganizo kapena kuchita mantha kumene wachibale wawo kapena mnzawo akamwalira. Kuthandiza mwana pa nthawi imeneyi kumakhala kovuta, makamaka kwa makolo omwenso ali ndi chisoni, chifukwa nawonso amafuna munthu woti awalimbikitse.

Makolo ena amauza mwana wawo kuti munthu amene wamwalirayo wachoka kapena wapita kwinakwake. Iwo amachita zimenezi kuti mwanayo asamve chisoni kwambiri. Komabe, mawu ngati amenewa ndi abodza komanso osokoneza. Ndiyeno mungamuuze bwanji mwana ngati m’bale wake wamwalira?

Renato ndi Isabelle, omwe ndi a Mboni za Yehova, anakumanapo ndi vuto limeneli. Mwana wawo wazaka zitatu ndi miyezi 6, dzina lake Nicolle, anamwalira. Iwo anafunika kulimbikitsa mwana wawo wamwamuna, dzina lake Felipe, yemwe anali ndi zaka 5 pamene Nicolle amamwalira.

Mtolankhani wa Galamukani!: Nicolle atamwalira, kodi munamufotokozera bwanji Felipe?

Isabelle: Tinaona kuti ndi bwino kumuuza zoona zokhazokha. Tinamulimbikitsa kuti azifunsa mafunso ndipo tinkamuyankha mogwirizana ndi msinkhu wake. Mwachitsanzo, Nicolle anamwalira ndi matenda omwe amayamba ndi mabakiteriya, choncho pomufotokozera Felipe tinamuuza kuti, kabakiteriya kanalowa m’thupi mwa Nicolle, ndipo madokotala analephera kukapha.

Mtolankhani wa Galamukani!: Kodi munamufotokozera Felipe zimene mumakhulupirira pa nkhani ya imfa?

Renato: Tinaona kuti kumufotokozera Felipe zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa kungamulimbikitse. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti akufa sadziwa kanthu. (Mlaliki 9:5) Tinkaganiza kuti Felipe azichita mantha makamaka akakhala yekha usiku. Choncho tinaona kuti kukambirana naye mfundo imeneyi kungamuthandize kuthetsa mantha amenewo.

Isabelle: Baibulo limaphunzitsanso kuti anthu amene anamwalira adzauka ndipo adzakhala m’paradaiso padziko lapansi. Ifeyo timakhulupirira zimenezi ndipo tinaona kuti zingamuthandizenso Felipe. Choncho tinakambirana naye zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, tinakambirana zimene Yesu anachita poukitsa mwana wamkazi wa Yairo, wazaka 12. Kenako tinamufotokozera kuti Nicolle adzauka ngati mmene anachitira mwana wamkazi wa Yairo. Zimenezi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.—Maliko 5:22-24, 35-42; Yohane 5:28, 29.

Mtolankhani wa Galamukani!: Kodi mukuona kuti Felipe anamvetsa zimene munkamuuzazo?

Renato: Inde, tikuona kuti anamvetsa chifukwa nthawi zambiri ana savutika kumvetsa zimene zimachitika munthu akamwalira mukawauza zoona zokhazokha komanso mosavuta kumva. Zimenezi zimathandizanso kuti asamangokhala achisoni nthawi zonse. Palibe chifukwa chobisira chifukwa imfa sichinthu chobisa. Choncho makolo ayenera kuthandiza ana awo kudziwa zimene angachite ngati m’bale wawo kapena mnzawo wamwalira. N’zimenenso tinachita pothandiza mwana wathu wina dzina lake Vinicius. *

Mtolankhani wa Galamukani!: Kodi Felipe analipo pa mwambo wamaliro?

Renato: Titaganizira mofatsa, tinaona kuti asakhalepo chifukwa ana ngati iyeyu amavutika ndi maganizo kwambiri. N’zoona kuti makolo ena angafune kuti mwana wawo wamng’ono akhale pa mwambo wamaliro chifukwa ana amasiyanasiyana. Koma ngati makolo asankha kuti akhalepo, zingakhale bwino kuti amuuziretu zimene zimachitika pa mwambowo.

Mtolankhani wa Galamukani!: Ndikudziwa kuti imfa ya Nicolle inakukhudzani kwambiri. Kodi munkachita manyazi kulira poopa kuti mwana wanu Felipe akuonani?

Isabelle: Ine ndi mwamuna wanga sitinachite manyazi kulira. Tinaona kuti kulira sikulakwa chifukwa ngakhale Yesu “anagwetsa misozi” mnzake wapamtima atamwalira. (Yohane 11:35, 36) Zinali zoyenera kuti Felipe atione tikulira chifukwa zinamuthandiza kudziwa kuti kulira posonyeza chisoni sikulakwa. Kulira kumasonyeza mmene munthu akumvera mumtima. Tinkafuna kuti Felipe azimasuka kusonyeza chisoni chake m’malo mongozisunga mumtima.

Renato: Munthu mmodzi akamwalira m’banja, nthawi zambiri ana amakhala ndi mantha. Choncho ngati makolofe timamasuka kuuza ana athu mmene tikumvera, nawonso amakhala omasuka kufotokoza mmene akumvera. Ngati choyamba makolo amvetsera zimene zikuwadetsa nkhawa ana awo, akhoza kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kuti asakhale ndi mantha.

Mtolankhani wa Galamukani!: Kodi pali anthu ena amene anakuthandizani?

Renato: Inde, anthu a ku mpingo kwathu anatithandiza kwambiri. Ankabwera kudzationa, kutiimbira foni komanso kutilembera makhadi. Zimenezi zinathandiza mwana wathu Felipe kuona kuti anthu a ku mpingo kwathu amatikonda kwambiri.

Isabelle: Achibale athunso anatithandiza kwambiri. Titaika malirowo, bambo anga ankabwera m’mawa uliwonse kudzadya nafe chakudya cha m’mawa. Iwo ankachita zimenezi pofuna kudzatilimbikitsa ndipo zimenezi zinamuthandiza kwambiri Felipe.

Renato: Tinalimbikitsidwanso kwambiri chifukwa chopezeka pa misonkhano yachikhristu. Tinkayesetsa kuti tisaphonye misonkhano ngakhale kuti nthawi zina tikakhala pa misonkhanopo tinkalira tikakumbukira Nicolle. Komabe tinkadziwa kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri, makamaka kwa mwana wathu Felipe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani imeneyi, werengani nkhani yakuti “Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni,” mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2008, patsamba 18 mpaka 20, komanso kabuku kakuti, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 14]

Mabuku amene ali m’munsiwa angalimbikitse anthu amene wachibale wawo kapena mnzawo wamwalira. Mabukuwa amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

ACHIKULIRE ANGAWERENGE:

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Mutu 6: Kodi Akufa Ali Kuti?

Mutu 7: Chiyembekezo Chotsimikizika Chokhudza Okondedwa Anu Amene Anamwalira

ANA ANGAWERENGE:

Buku Langa la Nkhani za M’baibulo

Mutu 92: Yesu Aukitsa Akufa

ANA OKULIRAPO ANGAWERENGE:

phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso

Mutu 34: Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?

Mutu 35: Tingauke kwa Akufa!

Mutu 36: Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti?

ACHINYAMATA ANGAWERENGE:

Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa​—Buku Loyamba

Mutu 16: Kodi N’kwachibadwa Kumva Chisoni Monga Momwe Ndimachitira?

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 15]

MMENE MUNGAMUTHANDIZIRE

● Mulimbikitseni kuti azifunsa mafunso ndipo yesetsani kuchita zinthu zimene zingamuthandize kuti amasuke kulankhula zokhudza imfa komanso zimene zimachitika munthu akamwalira.

● Pomuuza, musagwiritse ntchito mawu okuluwika monga akuti, “watisiya” kapena “wapita.”

● Muuzeni zokhudza imfa m’mawu osavuta kumva. Mwachitsanzo ena akafuna kuuza mwana za munthu amene wamwalira amamuuza kuti thupi lake “lasiya kugwira ntchito.”

● Muuzeni zimene zimachitika pamaliro ndipo mufotokozereni kuti munthu womwalirayo sangathe kumva kapena kuona zimene zikuchitikazo.

● Musachite manyazi kulira chifukwa zimenezi zingamuthandize mwana wanuyo kudziwa kuti kulira pamaliro sikulakwa.

● Dziwani kuti pali njira zosiyanasiyana zosonyezera chisoni ndipo ana amasonyezanso chisoni mosiyanasiyana mogwirizana ndi mmene amamudziwira womwalirayo.

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera ku: www.kidshealth.org

[Chithunzi patsamba 15]

Kuchokera kumanzere: Felipe, Renato, Isabelle, ndi Vinicius