Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa? (April 2009) Ndine mayi wa zaka 24 ndipo ndakhala ndikuwerenga Baibulo koma sindinkasangalala ndikamaliwerenga. Koma ndinayamba kutsatira malangizo amene munafotokoza mu nkhaniyi. Panopa ndikuyesetsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’kabokosi munati tidule kaja. Zimenezi zachititsa kuti ndizisangalala nthawi yanga yowerenga Baibulo ikakwana. Ndikamawerenga ndikumaona kuti nkhani za m’mabuku a m’Baibulo ndi zogwirizana. Sindinasangalalepo chonchi pa moyo wanga chifukwa chowerenga Baibulo. Ndikukuthokozani kwambiri.

K. T., United States

Buku Limene Mungathe Kulikhulupirira—Gawo 6 (April 2011) Mutu wa nkhaniyi unali wakuti, “Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Ufumu wa Roma.” Ponena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu, nkhaniyi inanena kuti: “Asilikali a Roma anabwereranso [ku Yerusalemu] ndipo pa nthawiyi ankatsogoleredwa ndi Vasipashani ndi mwana wake Tito. Iwo anali ndi asilikali okwana 60,000.” Nkhaniyi inasonyeza kuti Vasipashani ndi mwana wake Tito ndi amene ankatsogolera asilikali pa nkhondo yolanda mzinda wa Yerusalemu. Koma zimene mabuku ena amanena zimasonyeza kuti, pomwe nkhondoyi inkachitika n’kuti Vasipashani ali ku Roma.

J. O., Australia

Yankho la “Galamukani!”: Buku lakuti “Josephus—The Essential Writings,” limene Paul L. Maier analemba limanena kuti: “Tito anachoka ku Alesandriya ndi gulu la asilikali n’kupita ku Tolemayi komwe bambo ake ankamudikirira ndi magulu enanso awiri a asilikali.” Komanso buku lina limene Matthew Bunson analemba limanena kuti: “Mu 68.C.E [Vasipashani] ndi mwana wake Tito anagonjetsa Ayuda omwe sankagwirizana ndi ufumu wa Roma. Koma pomwe ankakonzekera kuti akalande kachisi wa ku Yerusalemu, analandira uthenga woti Nero wamwalira ndipo Galba ndi amene wayamba kulamulira m’malo mwake. . . . Vasipashani anafika ku Roma chakumapeto kwa 70.C.E.” Zimenezi zikusonyeza kuti poyamba Vasipashani ndi Tito anamenyera limodzi nkhondo yolanda mzinda wa Yerusalemu koma nkhondoyi ili mkati, Vasipashani anabwerera ku Roma n’kumusiya Tito kuti atsogolere pa nkhondoyo.

Kodi Zolinga Zimene Muli Nazo N’zotheka Kuzikwaniritsa? (February 2011) Nkhaniyi inapereka zitsanzo za zinthu zimene munthu amafuna atakhala nazo koma sangazikwanitse. Zina mwa zinthuzi zinali, “kufuna kutchuka, kulemera, kupeza mkazi kapena mwamuna wopanda vuto lililonse, kapena kufuna kukhala ndi thanzi labwino kwambiri.” N’chifukwa chiyani “kupeza mkazi kapena mwamuna wopanda vuto lililonse,” kuli m’gulu la zinthu zosatheka?

S. K., United States

Yankho la “Galamukani!”: Nkhaniyi sinanene kuti munthu amene akufuna kukwatira ndiye kuti akufuna zinthu zosatheka. M’malomwake inanena za kufufuza “mkazi kapena mwamuna wopanda vuto lililonse.” Mfundo yaikulu mu nkhaniyi inali yakuti n’zosatheka kupeza mkazi kapena mwamuna yemwe sangalakwitse chilichonse. Tikutero pa zifukwa ziwiri izi: Choyamba, padziko lapansi palibe munthu amene salakwitsa. (Aroma 3:23) Chachiwiri, munthu amene amalakalaka zimenezi amasonyeza kuti ndi wodzikonda chifukwa amangofuna kupeza zinthu zimene zingamusangalatse iyeyo basi. Anthu enanso amene ali kale pabanja amakhala ndi maganizo akuti akhoza kumusintha mwamuna kapena mkazi wawo kuti azichita zimene iwo amafuna. Koma mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amakhala ndi banja losangalala ndi amene amazindikira kuti onse nthawi zina amalakwitsa zinthu. Chifukwa cha zimenezi, iwo amayesetsa kupitirizabe “kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.”—Akolose 3:13.