Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 3

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 3

Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 3

“Tapeza Mesiya”

Nkhani zokwanira 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani!, zizifotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Nkhanizi zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.

KUDAKALI zaka zambiri Yesu asanabadwe, aneneri achiheberi ananeneratu kuti kudzabwera Mesiya. M’chiheberi, dzina lakuti Mesiya limatanthauza “Wodzozedwa.” Aneneriwa anafotokoza mwatsatanetsatane za moyo wa Mesiyayo. Iwo ananeneratu za nthawi, malo komanso mzere umene adzabadwire. Anafotokozanso zinthu zina zimene zidzamuchitikire.

Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankakhulupirira kuti Yesu anakwaniritsa maulosi onsewa. Iwo ankaona Yesu ngati mmene Andireya ankamuonera. Iye anauza m’bale wake Simoni kuti: “Ifetu tapeza Mesiya.” (Yohane 1:40, 41) Kodi iwo ankalakwitsa kuganiza choncho? Kuti tipeze yankho, tiyeni tione maulosi anayi onena za Mesiya. Pa ulosi uliwonse tiona umboni wosonyeza kuti Yesu analidi Mesiya.

Ulosi woyamba: Adzakhala “pampando wachifumu wa Davide.”—Yesaya 9:7.

Kukwaniritsidwa kwake: Uthenga Wabwino wa Mateyu umayamba ndi mawu akuti: “Buku la mzere wa makolo a Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abulahamu.” Mateyu ndi Luka anatchula mzere womwe Yesu anabadwira, womwe umasonyeza kuti Yesu anali mbadwa ya Davide.—Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-38.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Zimene katswiri wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Josephus analemba, zimasonyeza kuti mabuku amene ankalembamo mabanja a ku Isiraeli ankasungidwa kumalo osungira zinthu zakale. Koma mabukuwo anawonongedwa pamene mzinda wa Yerusalemu unkawonongedwa mu 70 C.E. Komabe, Yerusalemu asanawonongedwe, anthu ambiri ankadziwa kuti Yesu anali mbadwa ya Davide. (Mateyu 9:27; 20:30; 21:9) Ikanakhala kuti mfundo imeneyi ndi yabodza, anthu akanaitsutsa, koma palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti pali amene ankatsutsa.

Ulosi wachiwiri: “Iwe Betelehemu Efurata, ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda. Komabe mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli.”—Mika 5:2.

Kukwaniritsidwa kwake: Yesu anabadwira ku Betelehemu. Kaisara Augusto atalamula kuti pachitike kalembera, Yosefe, yemwe anali bambo ake a Yesu omulera, anachoka ku Nazareti “n’kupita ku Yudeya [Yuda], kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu, chifukwa anali wa m’banja ndi m’fuko la Davide. Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya.” Ali kumeneko, Mariya “anabereka mwana wake woyamba wamwamuna,” ndipo mwanayo anali Yesu.—Luka 2:1-7.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Akatswiri ofufuza zinthu zakale anapeza umboni wosonyeza kuti ufumu wa Roma unkachita kalembera ku Middle East n’cholinga choti udziwe ndalama za msonkho zimene uzitolera komanso anthu amene angayenerere usilikali. Umboni umodzi wosonyeza kuti kalembera ameneyu ankachitika ndi chikalata chimene bwanamkubwa wachiroma wa ku Iguputo analemba mu 104 C.E. Chikalatachi chili kumalo osungira zinthu zakale ku Britain ndipo analembapo kuti: “Poona kuti nthawi yoti kalembera achitike panyumba iliyonse yakwana, ndi bwino kulimbikitsa aliyense amene akukhala dera lina pa zifukwa zilizonse, kuti abwerere kwawo n’cholinga choti akalembetse. Komanso ayenera kuonetsetsa kuti walima bwinobwino munda wake umene anagawiridwa.”

● Pa nthawi imene Yesu anabadwa, ku Isiraeli kunali matawuni awiri omwe ankadziwika kuti Betelehemu. Tawuni ina inali kumpoto, kufupi ndi mzinda wa Nazareti. Ndipo inayo inali ku Yuda, kufupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Zikuoneka kuti poyamba tawuni imeneyi inkadziwika kuti Efurata. (Genesis 35:19) Mogwirizana ndi zimene Mika ananena zaka pafupifupi 800 Yesu asanabadwe, zinachitikadi kuti Yesu anabadwira m’tawuni ya Betelehemu Efurata.

Ulosi wachitatu: “Kuchokera pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleri adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.”—Danieli 9:25.

Kukwaniritsidwa kwake: Nthawi imene inatchulidwa mu ulosi wa Danieli inali masabata 69, sabata lililonse limaimira zaka 7, kapena kuti zaka 483 zonse pamodzi. Ntchito yomanganso Yerusalemu inayamba mu 455 B.C.E. Mogwirizana ndi ulosiwu, patatha zaka 483 (masabata 69 oimira zaka), Yesu anakhala Wodzozedwa, kapena Mesiya mu 29. C.E. Zimenezi zinachitika pamene iye anabatizidwa ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera. *Luka 3:21, 22.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe, “anthu anali kuyembekezera” kubwera kwa Mesiya. (Luka 3:15) Katswiri wina wachiyuda, dzina lake Abba Hillel Silver, analemba buku lomwe linafotokoza kuti Yerusalemu asanawonongedwe “anthu ambiri ankakhulupirira kuti Mesiya abwera posachedwa.” Bukuli linanenanso kuti: “Anthu ankayembekezera kuti Mesiya adzabwera Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa.” Linapitirizanso kuti Ayuda ankayembekezera zimenezi chifukwa cha zimene “anthu ambiri ankaganiza pa nthawi imeneyo.”

Ulosi wachinayi: “Manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa, ndipo adzakhala limodzi ndi anthu olemera pa imfa yake.”—Yesaya 53:9.

Kukwaniritsidwa kwake: Yesu anapachikidwa limodzi ndi zigawenga ziwiri koma anaikidwa m’manda amene munthu wina wachuma, dzina lake Yosefe wa ku Arimateya, anapereka.—Mateyu 27:38, 57-60; Yohane 19:38.

Zimene mbiri imasonyeza:

● Anthu ambiri olemba mabuku omwe sanali Akhristu amavomereza kuti Yesu anaphedwa ngati wachifwamba. Ena mwa anthu amenewa ndi Josephus, yemwe anali wachiyuda ndiponso Tacitus wachiroma.

● Akatswiri ofufuza zinthu zakale ku Palestine anapeza manda akale omwe anawasema pamwala. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa nthawi imeneyo, anthu olemera ngati Yosefe wa ku Arimateya ankakhala ndi manda osemasema kale.

M’nkhaniyi, tangoona maulosi ochepa chabe mwa maulosi ambirimbiri onena za Mesiya omwe Yesu anakwaniritsa. Palibe munthu amene akanatha kungopeka nkhani zimenezi. Kukwaniritsidwa kwa maulosiwa kumatitsimikizira kuti analembedwa ndi Mulungu. Zimatithandizanso kukhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa maulosi onse onena za madalitso amene anthu okhulupirika adzapeze mu ulamuliro wa Mesiya.

Nkhani yotsatira idzayankha funso ili: Ngati Yesu analidi Mesiya amene Mulungu analonjeza, n’chifukwa chiyani analola kuti azunzidwe komanso kuphedwa?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri za ulosi wonena za nthawi imene Mesiya anadzozedwa, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 197 mpaka 199. Bukuli limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Tchati/​Zithunzi pamasamba 22, 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KUKWANIRITSIDWA KWA MAULOSI OKHUDZA MESIYA

1 Mesiya adzakhala mbadwa ya Mfumu Davide

1070 B.C.E.

Davide akhala mfumu ya Isiraeli

607 B.C.E.

Asilikali a ku Babulo awononga mzinda wa Yerusalemu

455 B.C.E.

Lamulo lomanganso Yerusalemu liperekedwa

2 Mesiya adzabadwira ku Yudeya mumzinda wa Betelehemu

2 B.C.E.

Yesu abadwa ku Yudeya mumzinda wa Betelehemu mu mzera wobadwira wa Davide

3 Mesiya adzabwera patatha zaka 483, lamulo lomanganso Yerusalemu litaperekedwa

29 C.E.

Yesu abatizidwa ndiponso kudzozedwa ngati Mesiya

4 Mesiya adzapachikidwa limodzi ndi ochimwa koma adzaikidwa m’manda ndi olemera

33 C.E.

Yesu apachikidwa pamodzi ndi achifwamba koma aikidwa m’manda ndi anthu olemera