Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndani Angakwanitse Kusintha Zinthu Padzikoli?

Ndani Angakwanitse Kusintha Zinthu Padzikoli?

Zimene Baibulo Limanena

Ndani Angakwanitse Kusintha Zinthu Padzikoli?

“Anthu padziko lonse akufuna kuti atsogoleri awo awathandize kuthetsa mavuto amene akukumana nawo. Iwo akuyembekezera kuti atsogoleriwo apeza njira zothetseratu mavuto onse.”—ANATERO BAN KI-MOON, YEMWE NDI MLEMBI WAMKULU WA BUNGWE LA UNITED NATIONS.

BAIBULO limanena kuti tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Nthawi zonse tikumamva nkhani za nkhondo, uchigawenga, mavuto azachuma komanso anthu akukhala mwa mantha chifukwa choopa ngozi zachilengedwe.

Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzasintha padzikoli? Kodi maboma a anthu angathetse mavuto amene alipowa? Kodi ndi ndani amene angathetsedi mavuto athu?

Zimene Mayiko Ambiri Amaganiza

Mayiko ambiri amanena kuti amathandizidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, mawu olemekeza mbendera komanso osonyeza kukhulupirika ku dziko la United States, amanena kuti: “Ndife ogwirizana mothandizidwa ndi Mulungu.” Komanso pa ndalama za dzikolo analembapo mawu akuti, “Timadalira Mulungu.”

Koma chodabwitsa n’choti m’dziko la United States lomwelo muli anthu ambiri omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Ndi mmene zililinso m’mayiko ena omwe amati Mulungu ndi amene akuyendetsa zinthu m’dziko lawo. Ndiponso anthu amene amati amakhulupirira Mulungu amasiyana maganizo pa nkhani ya mmene Mulungu amathandizira anthu.

● Ena amanena kuti Mulungu salowerera pa zochita za anthu moti anasiyira anthu kuti azidzilamulira okha mmene akufunira.

● Ena amanena kuti Mulungu amathandiza anthu pogwiritsa ntchito maboma ndipo amadalitsa zimene mabomawo akuchita kuti asinthe zinthu padzikoli.

Kodi pa mfundo ziwirizi, inuyo mumakhulupirira iti?

Taganizirani izi: Mfundo yoyambayo ikanakhala kuti ndi yoona bwenzi anthufe tili pa mavuto aakulu. Komanso mfundo yachiwiriyo ikanakhala kuti ndi yoona, bwenzi anthu akudzifunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amakonda anthu a dziko lina kuposa linzake? Ngati mayiko awiri atayamba kumenyana ndipo dziko lililonse n’kumapemphera kuti Mulungu awathandize, kodi angakhale kumbali iti?’ Kodi kapena Mulungu angangosiya osathandiza dziko lililonse?

Zimene Baibulo Limaphunzitsa

1. Munthu sanapangidwe kuti azidzilamulira yekha. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zomwe zachitikapo mbuyomu zimasonyeza kuti mawu amenewa ndi oona. Ngakhale kuti atsogoleri ena ayesapo kuchita zinthu zofuna kuthandiza, iwo alephera kuthetsa mavuto padzikoli. M’malo moti zinthu zisinthe, “munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

2. Mulungu amamva chisoni tikamavutika. Mulungu amadziwa zimene zikutichitikira ndipo amamva chisoni tikamavutika. Komanso posachedwapa athetsa mavuto amene tikukumana nawo. Iye achita zimenezi pogwiritsa ntchito Ufumu wake “umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.”—Danieli 2:44.

3. Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni. Ufumu umenewu ndi umene anthu mamiliyoni ambiri amaupempherera akamapemphera pemphero la Atate Wathu lomwe ena amalitchula kuti Pemphero la Ambuye. Mu pemphero limeneli, anthu amapempha Mulungu kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Pemphero limeneli limasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ukuchititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba komanso kuti chidzachitike padziko lapansi pano.

4. Mulungu adzagwiritsa ntchito ufumu wake kusintha zinthu padzikoli. Ngati mumakayikira mfundo imeneyi, taonani zimene Baibulo limaphunzitsa:

● Mulungu analenga munthu kuti azikhala mosangalala ndipo anamuika m’malo okongola kwambiri.—Genesis 1:27-31.

● Ngakhale kuti padzikoli pali mavuto ambiri, Mulungu sanasinthe cholinga chake chimene analengera dziko lapansi.—Salimo 37:11, 29.

● Mulungu anayamba kale kuchita zinthu zothandiza kuti anthu komanso dziko lapansili lidzakhale mmene ankafunira poyamba.—Yohane 3:16.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za Ufumu wa Mulungu komanso mmene udzasinthire zinthu padzikoli, pemphani a Mboni za Yehova a m’dera lanu kuti akuthandizeni. Mungachite bwino kudzakambirana nawo mfundo zotsatirazi:

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu udzasintha chiyani padzikoli?

Kodi udzabwera liti ndipo udzasintha bwanji zinthu?

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

● N’chifukwa chiyani maboma a anthu sangakwanitse kuthetsa mavuto onse a anthu?—Yeremiya 10:23.

● Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amatikonda?—Yohane 3:16.

● Kodi Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso otani kwa anthu?—Salimo 37:11, 29.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Kodi maboma a anthu angathetse mavuto amene alipowa? Kodi ndani amene angathetsedi mavuto athu?