Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 2

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 2

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndimangocheza Naye, Kapena Ndimamufuna? Gawo 2

MU GAWO 1, tinakambirana kuti ngati mutayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana musanakonzeke kukhala pachibwenzi:

● Mukhoza kukhumudwa kapena kukhumudwitsa mnzanuyo.—Miyambo 6:27.

● Mukhoza kudana. *Miyambo 18:24.

MU NKHANI INO, Tikambirana

● Mfundo yachitatu yokhudza kucheza kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana

● Mmene mungadziwire kuti mwayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana

DZIWANI IZI: Ngati mutayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana musanakonzeke kukhala pachibwenzi, mukhoza kuwononga mbiri yanu. Mtsikana wina dzina lake Mia * anati: “Anyamata ena amakonda kucheza ndi atsikana ambirimbiri moti atsikanawo amaona ngati awafunsira. Koma sikuti anyamatawo amafuna kufunsira atsikanawo. Iwo amangomva bwino mumtima mtsikana akamawasekerera.”

Taganizirani izi:

● Kodi kucheza kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana kungakhudze bwanji mbiri yanu?

“Kulemberana mameseji ndi mnyamata kapena mtsikana kumabweretsa mavuto. Mwachitsanzo, ukhoza kuyamba kutumizirana mameseji ndi munthu mmodzi koma kenako umayamba kulemberana ndi anthu ambiri. Zikatero umangozindikira kuti anyamata ambiri akopeka nawe ndipo aliyense wa anyamatawo akuona ngati umangoganizira za iyeyo basi. Koma amakhumudwa kwambiri akazindikira kuti sumawafuna. Zotsatira zake n’zoti anthu amayamba kukuona ngati umangokopa anyamata.”—Anatero Lara.

Baibulo limanena kuti: “Mnyamata [kapena mtsikana] amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.”—Miyambo 20:11.

Mfundo yaikulu: Kucheza ndi atsikana kapena anyamata sikulakwa. Koma ngati simungadziikire malire, mukhoza kukhumudwa, kudana ndi anzanu komanso mukhoza kuwononga mbiri yanu.

Kodi mungadziwe bwanji kuti mwayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana? Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndikumakonda kuuzana zachinsinsi ndi mnyamata kapena mtsikana winawake?’ Mtsikana wina dzina lake Erin ananena kuti: “Ngati umangocheza ndi mnyamata kapena mtsikana ndipo si ufuna kuti ukhale naye pa chibwenzi, ndiye palibe chifukwa choti iye azikhala munthu woyamba kulankhula naye tsiku lililonse, kumuuza zakukhosi kapena mavuto ako.”

Taganizirani izi:

● N’chifukwa chiyani zimakhala zosangalatsa kuuza zakukhosi mnyamata kapena mtsikana yemweyemweyo? Kodi mukuganiza kuti zimenezi zingabweretse mavuto otani?

“Ndimacheza ndi anyamata koma sikuti ndimacheza nawo kwambiri ngati mmene ndingachitire ndi atsikana anzanga. Ndipo pali nkhani zimene sindingakambirane nawo.—Anatero Rianne.

Baibulo limanena kuti: “Samalani ndi zimene mumalankhula . . . Wolankhula mosasamala amadziwononga yekha.”—Miyambo 13:3, Good News Translation.

Taganizirani izi: Kodi mukuona kuti pali vuto ngati mutamauza mnyamata kapena mtsikana zinthu zanu zachinsinsi? Kodi mukuganiza kuti zingakhale bwanji mutadzasiya kucheza ndi munthuyo? Kodi mungadzadziyimbe mlandu kuti bola mukanapanda kumuuza?

Pa mfundo imeneyi, mtsikana wina dzina lake Alexis ananena kuti: “Sikuti muziopa kucheza ndi anyamata kapena atsikana. Koma ngati simukudziikira malire, mukhoza kuyamba kukopana ndipo pamapeto pake mukhoza kukhumudwa kapena kukhumudwitsa mnzanuyo.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri, werengani Galamukani! ya June 2012, masamba 15 mpaka 17.

^ ndime 9 Mayina ena tawasintha m’nkhaniyi.

[Bokosi patsamba 17]

NKHANI IMENE INACHITIKADI: “Ndinkakonda kucheza kwambiri ndi mnyamata winawake ndipo pasanapite nthawi tinayamba kumakambirana zachinsinsi komanso kucheza kwa nthawi yaitali. Ndinkadziwa kuti tsiku lina adzandifunsira chifukwa anayamba kumasuka nane n’kumandiuza zakukhosi kwake. Kenako tsiku lina ananditumizira imelo yondiuza kuti amandifuna. Poyamba ndinasangalala chifukwa ndi zimene aliyense amachita akadziwa kuti winawake amamuona kuti ndiwofunika kwambiri. Komabe ndinali ndi nkhawa chifukwa ndinali ndisanakonzeke kukhala pa chibwenzi komanso ndinkadziwa kuti akhumudwa ndikamuuza kuti sitingakhale pa chibwenzi chifukwa tidakali ana. Choncho, ndinauza makolo anga za nkhaniyi ndipo anandilangiza kuti ndisamacheze naye kwambiri. Zimene zinachitikazi zinandithandiza kuona kuti zinthu zikhoza kusintha mofulumira moti anthu omwe poyamba ankangocheza, akhoza kuyamba kufunana. Kungoyambira pompo, ndimapewa kucheza kwambiri ndi anyamata ndipo sinditumizirana nawo mameseji kawirikawiri. Ndimaonanso kuti ndibwino kumacheza pagulu kusiyana n’kumacheza awiriwiri ndi mnyamata. Zimenezi zimathandiza kuti musamakambirane zinthu zimene zingachititse kuti muyambe kufunana.”—Anatero Elena.

[Bokosi patsamba 18]

FUNSANI MAKOLO ANU

Funsani makolo anu kuti anene maganizo awo pa mafunso amene ali ndi madontho m’nkhani ino. Kodi maganizo awo akusiyana ndi anu? Ngati akusiyana, akusiyana pati? Kodi mukuona kuti maganizo awowo akhoza kukhala othandiza?—Miyambo 1:8.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 18]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Andre—Ukamacheza kwambiri ndi mtsikana, umayamba kumufuna komanso iyeyo amayamba kuganiza kuti ukumufuna. Choncho ngati mukuona kuti simunakonzeke kukhala ndi chibwenzi panopa, musamapange dala zinthu zoonetsa ngati mukumufuna winawake.

Cassidy—Ndimakonda kucheza ndi anthu koma ndimamasuka kwambiri kucheza ndi anyamata chifukwa ndinakula ndi anyamata. Komabe sibwino kumacheza ndi mnyamata ngati mmene ungachezere ndi mtsikana mnzako chifukwa nthawi zina mnyamatayo akhoza kuganiza kuti ukumufuna. Ndi bwino kuti ukamacheza ndi anyamata uzingowaona ngati azichimwene ako.

[Bokosi patsamba 19]

MAWU KWA MAKOLO

Palibe cholakwika ngati anyamata ndi atsikana akucheza pamalo pomwe palinso anthu ena omwe akuwaona. Komabe ngati mwana wanu sanakonzeke kukhala pa chibwenzi ayenera kudziikira malire. * Ngati akucheza ndi anyamata kapena atsikana, azingocheza nawo ngati anzake basi.

Kodi chimachitika n’chiyani ngati anthu awiri ayamba kukondana kwambiri asanakonzeke kulowa m’banja? Poyamba amaoneka kuti akusangalala, koma kenako amadzakhumudwa. Zimakhala ngati akwera galimoto yopanda mateyala ndipo amadzazindikira kuti zimene akuchitazo zilibe phindu lililonse. Zikatero, ena amayamba kuchita zibwenzi mobisa komanso makhalidwe ena oipa. Ena amangosiiratu kuchezerana zomwe zimachititsa kuti wina aone kuti wangopusitsidwa ndipo pamapeto pake onse amakhumudwa. Ndiye kodi mungathandize bwanji mwana wanu wachinyamata kuti zimenezi zisamuchitikire?—Mlaliki 11:10.

Chinthu chofunika kwambiri ndi kukambirana ndi mwanayo momasuka nkhani zokhudza kucheza ndi anyamata kapena atsikana. Zimenezi zingachititse kuti mudziwe komanso kumuthandiza mwanayo mwansanga ngati atayamba kukondana kwambiri ndi mnyamata kapena mtsikana winawake.

Makolo ena sadziwa kuti zimene amachita zimapangitsa kuti mwana wawo asamamasuke kuwafotokozera za anyamata kapena atsikana amene amacheza nawo. Tamvani zimene achinyamata ena anauza mtolankhani wa Galamukani!

“Ndinkafunitsitsa nditawauza mayi anga za mnyamata amene ndinkamufuna, koma ndinkalephera chifukwa ndinkaopa kuti akwiya kwambiri.”—Anatero Cara.

“Ndinkati ndikawauza mayi anga za mnyamata winawake amene ndikumufuna, ankakonda kundiuza kuti, ‘Kuteroku ukuganiza zokwatiwa?’ m’malo mondifunsa kuti ‘Tandiuze za mnyamata ameneyu, amakusangalatsa chiyani?’ Akanakhala kuti mayi anga ankandifunsa mafunso amenewa, bwenzi ndikumvera kwambiri malangizo awo.”—Anatero Nadeine.

Tamvani zimene zimachitika makolo akamamvetsera kaye ana awo asanawapatse malangizo.

“Makolo anga sanandikalipire nditawauza za mnyamata wina amene ndinkamufuna. Iwo anandipatsa malangizo othandiza komanso anasonyeza kuti ankandimvetsa. Zimenezi zachititsa kuti ndizimvera malangizo awo komanso ndizimasuka kuwauza zakukhosi kwanga.”—Anatero Corrina.

“Makolo anga ankandiuza momasuka anyamata kapena atsikana amene ankawafuna komanso ankandifotokozera zimene zinachititsa kuti zibwenzi zawo zithe. Zimenezi zinathandiza kuti ndisamachite mantha kukambirana nawo za mnyamata amene ndikumufuna.”—Anatero Linette.

Muzikumbukiranso kuti achinyamata amayamba zibwenzi pa zifukwa zosiyanasiyana.

“Nthawi ina ndinkachita chibwenzi mobisa chifukwa ndinkasangalala ndikakhala ndi mnyamatayo komanso chifukwa chakuti ankandimvetsera ndikamalankhula.”—Anatero Annette.

“Panali mnyamata wina amene ndinkakonda kucheza naye chifukwa ankachita nane chidwi. Vuto langa ndilakuti munthu akangochita nane chidwi ndimangofuna kuti ndizingocheza naye.”—Anatero Amy.

“Makolo anga ankandiyamikira moona mtima kuti ndikuoneka bwino kapena kuti ndatchena, ndimasangalala kwambiri moti sindingafunenso kuti mnyamata andiuze zimenezi.”—Anatero Karen.

Makolo dzifunseni kuti:

Kodi ndingatani kuti mwana wanga wachinyamata azimasuka nane?—Afilipi 4:5.

Kodi ndine “wofulumira kumva” komanso “wodekha polankhula”?—Yakobo 1:19.

Kodi ndingatani kuti mwana wanga asamakafunefune anthu ena oti azimusonyeza chikondi?—Akolose 3:21.

Zoyenera kuchita: Thandizani mwana wanu kuti azicheza ndi anyamata komanso atsikana moyenerera n’cholinga choti apewe mavuto. Zimenezi zingadzamuthandize ngakhale atakula.—Akolose 3:5; 1 Atesalonika 4:3-6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 37 Onani nkhani imene yayambira patsamba 16 komanso nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” mu Galamukani! ya June 2012.

[Tchati patsamba 17]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

DZIIKIRENI MALIRE

ZOYENERA KUCHITA

muzicheza pa gulu

dziwanani bwino ndi aliyense

muzicheza momasuka ndi aliyense

ZIMENE SIMUYENERA KUCHITA

X musamacheze awiriwiri

X musamakambirane zachinsinsi

X musamakopane

[Chithunzi patsamba 18]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KUCHEZA

KUKOPANA

KUGWIRANAGWIRANA

KUGWIRANA MANJA

KUKISANA